Nahumu 2:1-13

  • Nineve adzakhala bwinja (1-13)

    • “Zotsekera madzi amʼmitsinje zidzatsegulidwa” (6)

2  Womwaza wabwera kudzalimbana nawe.*+ Teteza malo amene ali ndi mpanda wolimba kwambiri. Londera njira yako. Konzekera kumenya nkhondo* ndipo sonkhanitsa mphamvu zako zonse.   Chifukwa Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.Limodzi ndi ulemerero wa Isiraeli.Popeza owononga awawononga,+Ndipo asakaza mphukira zawo.   Zishango za amuna amphamvu zaviikidwa mu utoto wofiira,Asilikali ake avala zovala zofiira kwambiri. Zitsulo za magaleta ake ankhondo zili waliwali ngati moto,Pa tsiku limene akukonzekera nkhondo.Ndipo mikondo ya mitengo ya junipa* aipukuta.   Magaleta awo ankhondo akuthamanga kwambiri mʼmisewu. Iwo akuthamanga uku ndi uku mʼmabwalo a mzinda. Akuwala ngati matochi komanso kungʼanima ngati mphezi.   Mfumu idzaitanitsa asilikali ake amaudindo akuluakulu. Iwo azidzapunthwa pamene akuthamanga, Adzathamangira kumpanda wa mzinda.Iwo adzakhwimitsa chitetezo.   Zotsekera madzi amʼmitsinje zidzatsegulidwa,Ndipo nyumba yachifumu idzagwa.   Nkhani imeneyi ndi yotsimikizirika. Mzindawo wavulidwa nʼkuchititsidwa manyazi,Anthu ake atengedwa ndipo akapolo ake aakazi akulira.Akumveka ngati nkhunda pamene akudziguguda pamtima.   Kuyambira kalekale, Nineve+ anali ngati dziwe la madzi,Koma tsopano anthu ake akuthawa. Ena akufuula kuti: “Taimani! Taimani!” Koma palibe amene akubwerera.+   Tengani siliva wawo, tengani golide, Iwo ali ndi chuma chankhaninkhani. Ali ndi zinthu zosiyanasiyana zamtengo wapatali. 10  Mzindawu watsala wopanda kanthu, wawonongedwa ndipo wakhala bwinja.+ Mitima yawo yasungunuka ndi mantha, mawondo ndi ziuno zawo zikunjenjemera.Nkhope zawo zonse zili ndi nkhawa. 11  Ali kuti malo amene mikango yamphamvu+ inkadyerako?Malo amene mikango inkatsogolera ana ake,Popanda aliyense woiwopseza? 12  Mkango unkakhadzula nyama yokwanira kuti udyetse ana ake.Ndipo unkapha nyama kuti upatse mikango yaikazi. Mapanga ake ankakhala odzaza ndi nyama,Ndipo mʼmalo ake obisalamo munkakhala nyama zokhadzulakhadzula. 13  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, “Ine ndikukuukira.+Nditentha magaleta ako ankhondo mpaka akhala phulusa.+Ndipo lupanga lidzapha mikango yako yamphamvu. Ndidzachititsa kuti usagwirenso nyama padziko lapansi,Ndipo mawu a anthu amene umawatuma kukanena uthenga sadzamvekanso.”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza Nineve.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Limbitsa chiuno chako.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.