Nahumu 3:1-19
3 Tsoka mzinda wokhetsa magazi!
Mzindawo wadzaza ndi chinyengo ndi zauchifwamba,
Ndipo nthawi zonse umatenga zinthu za anthu omwe wagonjetsa.
2 Kukumveka kulira kwa mikwapulo ndiponso phokoso la mawilo,Mgugu wa mahatchi* ndi kuthamanga kwa magaleta.
3 Komanso pali asilikali okwera pamahatchi, malupanga owala ndiponso mikondo yonyezimira.Palinso anthu ambiri ophedwa komanso milu ya mitembo,Moti mitembo ili paliponse.
Anthu akupunthwa pamitemboyo.
4 Zili choncho chifukwa cha kuchuluka kwa zochita zake zauhule.Iye ndi mkazi wokongola mochititsa kaso ndiponso waluso lamatsenga.Ndipo amakopa mitundu ya anthu ndi uhule wake komanso mabanja ndi zochita zake zamatsenga.
5 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Taona! Ine ndikukuukira,*+Ndipo ndidzakuvula zovala zako nʼkukuphimba nazo kumaso.Ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ione maliseche ako,Ndipo maufumu adzaona kuti wachititsidwa manyazi.
6 Ndidzakuponyera zinthu zonyansa.Ndidzakuchititsa kukhala chinthu chonyozeka,Ndiponso chochititsa mantha.+
7 Aliyense wokuona adzakuthawa+ ndipo adzanena kuti,‘Nineve wawonongedwa!
Ndani adzamumvere chisoni?’
Kodi anthu oti akutonthoze ndidzawapeza kuti?
8 Kodi iwe uli pabwino kuposa No-amoni*+ amene anali pafupi ndi ngalande zochokera mumtsinje wa Nailo?+
Iye anazunguliridwa ndi madzi.Nyanja inali chuma chake ndiponso khoma lake.
9 Mphamvu zake zopanda malire zinkachokera ku Itiyopiya ndi ku Iguputo.
Anthu a ku Puti+ ndi a ku Libiya ankamuthandiza.+
10 Koma No-amoni anatengedwa kupita kudziko lina,Anamugwira nʼkupita naye ku ukapolo.+
Ana ake anaphwanyidwaphwanyidwa mʼmakona a misewu yonse.
Ndipo anthu ake olemekezeka anawachitira maere.Anthu ake onse otchuka amangidwa mʼmatangadza.
11 Iwenso udzaledzera,+Ndipo udzabisala.
Udzafunafuna malo oti uthawireko kuti mdani wako asakupeze.
12 Malo ako onse okhala ndi mipanda yolimba ali ngati mitengo ya mkuyu yokhala ndi nkhuyu zoyambirira kupsa.Munthu akagwedeza mitengoyo, nkhuyu zakezo zimagwera mʼkamwa mwa munthu wozidya.
13 Taona! Asilikali ako ali ngati akazi.
Mageti a dziko lako adzatsegulidwa kuti adani ako alowemo.
Ndipo moto udzawotcheratu mipiringidzo ya mageti ako.
14 Tunga madzi pokonzekera nthawi imene adani adzakuzungulire.+
Limbitsa malo ako okhala ndi mipanda yolimba.
Lowa mʼmatope ndi kupondaponda dothi.Gwira chikombole.
15 Koma ngakhale utero, moto udzakuwotcheratu.
Lupanga lidzakudula.+
Ndipo lidzakudya ngati mmene dzombe lingʼonolingʼono limadyera zomera.+
Dzichulukitseni ngati dzombe lingʼonolingʼono,
Dzichulukitseni ngati dzombe.
16 Iwe wachulukitsa amalonda ako kuposa nyenyezi zakumwamba.
Dzombe lingʼonolingʼono limafundula* kenako nʼkuulukira kutali.
17 Alonda ako ali ngati dzombe.Ndipo akapitawo ako ali ngati gulu la dzombe.
Pa tsiku lozizira limakhala mʼmakoma.Koma dzuwa likawala, dzombelo limauluka nʼkupita kutali.Ndipo palibe amene amadziwa kumene lapita.
18 Abusa ako ayamba kuodzera, iwe mfumu ya Asuri,Ndipo anthu ako olemekezeka akungokhala mʼnyumba zawo.
Anthu ako amwazikana mʼmapiri,Ndipo palibe amene akuwasonkhanitsa.+
19 Mavuto ako sadzakupatsa mpata wopuma.
Bala lako lafika posachiritsika.
Onse amene adzamve za iwe, adzawomba mʼmanja.+Chifukwa palibe amene sanavutike ndi zoipa zako zosatha.”+