Nehemiya 2:1-20

  • Nehemiya anatumizidwa ku Yerusalemu (1-10)

  • Nehemiya anayendera mpanda (11-20)

2  Mʼmwezi wa Nisani,* mʼchaka cha 20+ cha mfumu Aritasasita,+ mfumuyo inkafuna vinyo choncho ndinatenga vinyoyo nʼkukapereka kwa mfumu ngati mmene ndinkachitira nthawi zonse.+ Koma ndinali ndisanakhalepo wachisoni pamaso pake.  Choncho mfumu inati: “Nʼchifukwa chiyani ukuoneka wachisoni pamene sukudwala? Payenera kuti pali chinachake chimene chikukuvutitsa mumtima.” Atanena zimenezi ndinachita mantha kwambiri.  Kenako ndinayankha mfumuyo kuti: “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Ndilekerenji kuoneka wachisoni pamene mzinda umene makolo anga anaikidwako uli bwinja ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto?”+  Mfumuyo inandifunsa kuti: “Ndiye ukufuna chiyani?” Nthawi yomweyo ndinapemphera kwa Mulungu wakumwamba.+  Kenako ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima ine mtumiki wanu, munditumize ku Yuda, kumzinda umene makolo anga anaikidwako kuti ndikaumangenso.”+  Mfumu inandiyankha kuti: “Ulendo wako udzatenga masiku angati, ndipo udzabwera liti?” Pa nthawiyi, mkazi wamkulu wa mfumu anali atakhala pambali pake. Choncho mfumu inandilola kupita+ nditaiuza nthawi.+  Ndiyeno ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, lolani kuti ndipatsidwe makalata okasonyeza kwa abwanamkubwa a tsidya lina la Mtsinje,*+ kuti akandilole kudutsa mpaka ndikafike ku Yuda.  Komanso andipatse kalata yopita kwa Asafu amene akuyangʼanira Nkhalango ya Mfumu, kuti akandipatse mitengo yokakonzera mageti a Nyumba ya Chitetezo Champhamvu+ yakukachisi, mpanda wa mzindawo+ ndiponso nyumba imene ndizikakhalamo.” Choncho mfumu inandipatsa makalatawo+ chifukwa Mulungu anandikomera mtima.+  Kenako ndinafika kwa abwanamkubwa akutsidya lina la Mtsinje nʼkuwapatsa makalata a mfumu aja. Mfumu inandipatsanso akuluakulu a asilikali komanso asilikali okwera pamahatchi* kuti andiperekeze. 10  Sanibalati wa ku Beti-horoni+ ndi Tobia,+ mtumiki wa Chiamoni,+ anakwiya kwambiri atamva zimenezi komanso ataona kuti kwabwera munthu wodzachitira Aisiraeli zinthu zabwino. 11  Patapita nthawi, ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12  Ndinadzuka usiku limodzi ndi amuna angapo amene ndinali nawo. Sindinauze aliyense zimene Mulungu wanga anaika mumtima mwanga zoti ndichitire Yerusalemu. Pa nthawiyo ndinalibe chiweto chilichonse kupatulapo chiweto chimene ndinakwerapo. 13  Usikuwo ndinatulukira pa Geti ya Kuchigwa+ nʼkukadutsa kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu* mpaka ndinakafika ku Geti ya Milu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinkaona mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera mageti ake.+ 14  Ndinayendabe mpaka kukafika ku Geti la Kukasupe+ ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma kunalibe njira yoti chiweto chimene ndinakwerapo chidutse. 15  Koma usikuwo ndinayendabe mʼchigwamo+ molowera kumtunda ndipo ndinapitiriza kuona mpandawo. Kenako ndinabwerera nʼkukalowanso pa Geti ya Kuchigwa. 16  Atsogoleri+ sanadziwe kumene ndinapita komanso zomwe ndinkachita chifukwa sindinanene chilichonse kwa Ayuda, ansembe, anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu ena onse ogwira ntchito. 17  Kenako ndinawauza kuti: “Inu mukuona vuto lalikulu limene tili nalo. Yerusalemu ndi bwinja ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto. Tiyeni timangenso mpanda wa Yerusalemu kuti anthu asiye kutinyoza.” 18  Ndinawauzanso mmene dzanja la Mulungu wanga landithandizira+ ndiponso mawu amene mfumu inandiuza.+ Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timange mpandawo.” Choncho anadzilimbitsa* kuti agwire ntchito yabwinoyi.+ 19  Ndiyeno Sanibalati wa ku Beti-horoni, Tobia+ mtumiki wa Chiamoni+ ndi Gesemu Mluya+ atamva zimenezi anayamba kutiseka ndi kutinyoza.+ Iwo anati: “Nʼchiyani chimene mukuchitachi? Kodi mukugalukira mfumu?”+ 20  Koma ine ndinawayankha kuti: “Mulungu wakumwamba ndi amene adzatithandize kuti zinthu zitiyendere bwino,+ ndipo ife atumiki ake tipitiriza kumanga mpandawu. Inuyo sizikukukhudzani komanso mulibe ufulu kapena choti nʼkukukumbukirani nacho mu Yerusalemu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “a chakumtsinje wa Firate.”
Ena amati “mahosi.”
Mwina amenewa anali malo amene ankatchedwanso “Chitsime cha Eni-rogeli.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “analimbitsa manja awo.”