Nehemiya 4:1-23
4 Sanibalati+ atangomva kuti tikumanganso mpanda, anakwiya ndiponso anapsa mtima kwambiri moti anapitiriza kunyoza Ayuda.
2 Iye anauza abale ake komanso asilikali a ku Samariya kuti: “Kodi Ayuda ofookawa akuchita chiyani? Kodi akuona ngati angaikwanitse ntchito imeneyi? Kodi adzapereka nsembe? Kodi amaliza kumangako tsiku limodzi? Kodi afukula miyala imene inatenthedwa nʼkukwiririka ndi dothi kuti aigwiritsenso ntchito?”+
3 Tobia+ Muamoni,+ yemwe anaima pambali pake anati: “Ngakhaletu nkhandwe itakwera pampanda wamiyala umene akumangawo ikhoza kuugwetsa.”
4 Nehemiya anati: “Inu Mulungu wathu, onani mmene akutinyozera.+ Abwezereni chipongwe chawo+ ndipo lolani kuti atengedwe ngati katundu kupita ku ukapolo.
5 Musanyalanyaze zolakwa zawo+ kapena kufufuta machimo awo chifukwa anyoza anthu omanga mpanda.”
6 Choncho tinapitiriza kumanga mpandawo moti khoma lonse linalumikizana ndipo linafika hafu kupita mʼmwamba. Anthu anapitiriza kugwira ntchitoyo ndi mtima wonse.
7 Sanibalati, Tobia,+ Aluya,+ Aamoni ndi Aasidodi+ atamva kuti ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu ikuyenda bwino ndipo malo ogumuka ayamba kutsekedwa, anakwiya kwambiri.
8 Choncho anakonza chiwembu kuti abwere kudzamenyana ndi Yerusalemu nʼkusokoneza ntchito yathu.
9 Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinaika alonda kuti azititeteza masana ndi usiku.
10 Koma anthu a ku Yuda anayamba kunena kuti: “Mphamvu za anthu ogwira ntchito zatha, koma pali zinthu zambiri zofunika kuchotsa, ndipo sitingathe kumanga mpandawu.”
11 Adani athu ankanena kuti: “Adzangozindikira tafika ndipo tidzawapha nʼkuimitsa ntchito yomangayo.”
12 Ayuda okhala pafupi ndi adaniwo anabwera nʼkutiuza mobwerezabwereza* kuti: “Adaniwo adzatiukira kuchokera kumbali zonse.”
13 Choncho ndinaika amuna kuseri kwa mpanda pamalo otsika omwe anali poonekera. Ndinawaika mogwirizana ndi mabanja awo atanyamula malupanga, mikondo ingʼonoingʼono ndi mauta.
14 Nditaona kuti akuchita mantha, nthawi yomweyo ndinanyamuka nʼkuuza anthu olemekezeka,+ atsogoleri ndiponso anthu onse kuti: “Musachite nawo mantha.+ Kumbukirani Yehova yemwe ndi Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha.+ Menyani nkhondo kuti muteteze abale anu, ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu komanso nyumba zanu.”
15 Adani athuwo atamva zoti tadziwa za chiwembu chawo ndipo Mulungu woona wasokoneza mapulani awo, tonse tinayambiranso kumanga mpanda.
16 Kungochokera tsiku limenelo, hafu ya anyamata anga ankagwira ntchito+ ndipo hafu inayo ankanyamula mikondo ingʼonoingʼono, zishango, mauta ndipo ankavala zovala za mamba achitsulo. Akalonga ankathandiza*+ anthu onse amʼnyumba ya Yuda
17 amene ankamanga mpandawo. Anthu amene ankanyamula zinthu ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi ndipo kudzanja linalo ankanyamula chida.
18 Aliyense amene ankamanga, anali atamangirira lupanga mʼchiuno ndipo woliza lipenga la nyanga+ ya nkhosa anaima pafupi ndi ine.
19 Kenako ndinauza anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu ena onse kuti: “Ntchitoyi ndi yaikulu ndipo tikumakhala motalikirana kuzungulira mpandawu.
20 Ndiye mukamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, muzibwera kumene tili ndipo Mulungu wathu atimenyera nkhondo.”+
21 Choncho tinkagwira ntchito uku hafu ina itanyamula mikondo ingʼonoingʼono, kuyambira mʼbandakucha mpaka usiku nyenyezi zitatuluka.
22 Pa nthawiyo ndinauza anthu kuti: “Mwamuna aliyense limodzi ndi wantchito wake azigona mu Yerusalemu ndipo usiku azikhala alonda athu koma masana azigwira ntchito.”
23 Choncho ine, abale anga, atumiki anga+ ndi alonda amene ankanditsatira, sitinkasintha zovala ndipo aliyense ankanyamula mkondo mʼdzanja lake lamanja.