Nehemiya 6:1-19

  • Anthu ankatsutsabe ntchito yomanga (1-14)

  • Mpanda unamalizidwa mʼmasiku 52 (15-19)

6  Ndiyeno Sanibalati,+ Tobia, Gesemu Muluya+ komanso adani athu onse atangouzidwa kuti ndamanganso mpanda,+ ndipo ndatseka mipata yonse (ngakhale kuti pa nthawiyo ndinali ndisanaike zitseko mʼmageti),+  nthawi yomweyo Sanibalati ndi Gesemu ananditumizira uthenga wakuti: “Bwera tidzapangane nthawi yoti tikakumane mʼmudzi wina mʼchigwa cha Ono.”+ Koma ankandikonzera chiwembu.  Choncho ndinatumiza anthu kuti akawauze kuti: “Ntchito imene ndikugwirayi ndi yaikulu ndipo sindingathe kubwera. Kodi ntchitoyi iime chifukwa chakuti ine ndabwera kumeneko?”  Koma iwo ananditumizira uthenga womwewo maulendo 4, ndipo ine ndinkawayankha chimodzimodzi.  Kenako Sanibalati ananditumizira uthenga womwewo ulendo wa 5 kudzera mwa mtumiki wake. Mtumikiyo anali ndi kalata yosatseka mʼmanja mwake.  Mʼkalatayo analembamo kuti: “Pali mphekesera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo Gesemu+ akunenanso zomwezo, kuti iwe ndi Ayuda mukufuna kupanduka.+ Nʼchifukwa chake ukumanga mpandawo ndipo mogwirizana ndi zimene anthu akunenazi, iweyo ukufuna kukhala mfumu yawo.  Komanso waika aneneri kuti azilengeza za iwe mu Yerusalemu monse kuti, ‘Dziko la Yuda lili ndi mfumu!’ Mfumu ikhoza kumva mphekesera zimenezi. Choncho bwera tidzakambirane.”  Koma ine ndinamutumizira uthenga wakuti: “Palibe amene wachita zimene ukunenazi, koma wangozipeka mumtima mwako.”  Onsewo ankangofuna kutichititsa mantha, ndipo ankanena kuti: “Manja awo afooka ndipo asiya kugwira ntchitoyi, moti siitha.”+ Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.+ 10  Kenako ndinapita kunyumba kwa Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene anali atadzitsekera mʼnyumba. Iye anandiuza kuti: “Tiye tigwirizane nthawi yoti tikakumane kunyumba ya Mulungu woona, mʼkachisi ndipo tikatseke zitseko za kachisiyo. Chifukwa akubwera kudzakupha, akubwera kudzakupha usiku.” 11  Koma ndinamuyankha kuti: “Kodi mwamuna ngati ine ndingathawe? Kodi munthu ngati ine angalowe mʼkachisi nʼkukhala ndi moyo?+ Ine sindikalowamo!” 12  Kenako ndinazindikira kuti sanatumidwe ndi Mulungu, koma Tobia ndi Sanibalati+ ndi amene anamulemba ganyu kuti andinamize ndi ulosi wabodzawu. 13  Iwo anamulemba ganyu kuti andiopseze komanso kuti ndichite tchimo nʼcholinga choti apeze zifukwa zondiipitsira mbiri kuti azindinyoza. 14  Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobia+ ndi Sanibalati komanso zimene anachitazi. Mukumbukirenso Nowadiya mneneri wamkazi ndi aneneri onse amene ankafuna kundiopseza. 15  Choncho ntchito yomanga mpanda inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli* ndipo inatenga masiku 52. 16  Adani athu onse atangomva zimenezi komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi kwambiri+ ndipo anazindikira kuti ntchitoyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu. 17  Mʼmasiku amenewo, anthu olemekezeka+ a mu Yuda ankalemba makalata ambiri opita kwa Tobia ndipo Tobiayo ankawayankha. 18  Anthu ambiri mu Yuda anamulumbirira kuti akhala kumbali yake chifukwa anali mkamwini wa Sekaniya, mwana wa Ara.+ Ndipo Yehohanani mwana wa Tobia anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu,+ mwana wa Berekiya. 19  Komanso anthu amenewa nthawi zonse ankandiuza zinthu zabwino za Tobia. Kenako ankatenga zimene ine ndanena nʼkukamuuza Tobiayo ndipo iye ankanditumizira makalata ondiopseza.+

Mawu a M'munsi