Nehemiya 7:1-73
7 Mpanda utangotha kumangidwanso,+ ndinaika zitseko zake.+ Kenako ndinaika pa udindo alonda amʼmageti,+ oimba+ ndi Alevi.+
2 Kenako ndinaika Haneni mʼbale wanga+ ndi Hananiya, mkulu wa mʼNyumba ya Chitetezo Champhamvu,+ kuti aziyangʼanira Yerusalemu. Hananiya anali munthu wodalirika ndiponso woopa Mulungu woona+ kuposa anthu ena ambiri.
3 Choncho ndinawauza kuti: “Mageti a Yerusalemu sayenera kutsegulidwa mpaka dzuwa litakwera. Alonda amʼmageti aime pafupi ndipo atseke zitseko nʼkuzikhoma ndi anamphatika. Muikenso alonda a anthu a ku Yerusalemu, ena muwaike pamalo awo olondera ndipo ena muwaike kutsogolo kwa nyumba zawo.”
4 Mzindawo unali wotakasuka ndiponso waukulu. Munali anthu ochepa+ ndipo nyumba zinali zisanamangidwenso.
5 Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina motsatira mndandanda wa makolo awo.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti mʼbukumo analembamo izi:
6 Awa ndi anthu amʼchigawo amene anachoka ku ukapolo, anthu omwe Nebukadinezara+ mfumu ya ku Babulo anawatenga nʼkupita nawo ku ukapolo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense mumzinda wakwawo.+
7 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,+ Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredikayi, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu ndi Bana.
Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+
8 Ana a Parosi, 2,172.
9 Ana a Sefatiya, 372.
10 Ana a Ara,+ 652.
11 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,818.
12 Ana a Elamu,+ 1,254.
13 Ana a Zatu, 845.
14 Ana a Zakai, 760.
15 Ana a Binui, 648.
16 Ana a Bebai, 628.
17 Ana a Azigadi, 2,322.
18 Ana a Adonikamu, 667.
19 Ana a Bigivai, 2,067.
20 Ana a Adini, 655.
21 Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98.
22 Ana a Hasumu, 328.
23 Ana a Bezai, 324.
24 Ana a Harifi, 112.
25 Ana a Gibiyoni,+ 95.
26 Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, 188.
27 Amuna a ku Anatoti,+ 128.
28 Amuna a ku Beti-azimaveti, 42.
29 Amuna a ku Kiriyati-yearimu,+ Kefira ndi ku Beeroti,+ 743.
30 Amuna a ku Rama ndi ku Geba,+ 621.
31 Amuna a ku Mikemasi,+ 122.
32 Amuna a ku Beteli+ ndi ku Ai,+ 123.
33 Amuna a ku Nebo wina, 52.
34 Ana a Elamu wina, 1,254.
35 Ana a Harimu, 320.
36 Ana a Yeriko, 345.
37 Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono,+ 721.
38 Ana a Senaya, 3,930.
39 Ansembe:+ Ana a Yedaya, a mʼbanja la Yesuwa, 973.
40 Ana a Imeri, 1,052.
41 Ana a Pasuri,+ 1,247.
42 Ana a Harimu,+ 1,017.
43 Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodeva, 74.
44 Oimba:+ ana a Asafu,+ 148.
45 Alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, 138.
46 Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,
47 ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni,
48 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai,
49 ana a Hanani, ana a Gideli, ana a Gahara,
50 ana a Reyaya, ana a Rezini, ana a Nekoda,
51 ana a Gazamu, ana a Uziza, ana a Paseya,
52 ana a Besai, ana a Meyuni, ana a Nefusesimu,
53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,
54 ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa,
55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,
56 ana a Neziya komanso ana a Hatifa.
57 Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,
58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,
59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Amoni.
60 Atumiki apakachisi*+ onse ndiponso ana a atumiki a Solomo analipo 392.
61 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera, komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi,+ ndi awa:
62 Ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 642.
63 Ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi+ ndiponso ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo.
64 Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+
65 Bwanamkubwa*+ anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+
66 Anthu onse analipo 42,360.+
67 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi akapolo awo aakazi+ amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi 245.+
68 Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu* 245.
69 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.
70 Atsogoleri ena a nyumba za makolo anapereka zinthu zothandizira pa ntchito.+ Bwanamkubwa* anapereka kumalo osungira chuma ndalama za dalakima* zagolide 1,000, mbale zolowa 50 ndi mikanjo ya ansembe 530.+
71 Panalinso atsogoleri ena a nyumba za makolo amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchitoyo kumalo osungira chuma. Iwo anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000 ndi ndalama za mina* zasiliva 2,200.
72 Ndipo anthu ena onse anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndalama za mina zasiliva 2,000 ndi mikanjo ya ansembe 67.
73 Ndiyeno ansembe, Alevi, alonda apageti, oimba,+ anthu ena, atumiki apakachisi* ndiponso Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7,+ Aisiraeli anali atakhala mʼmizinda yawo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “anawachotsa pa udindo wokhala ansembe chifukwa anali odetsedwa.”
^ Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
^ “Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
^ Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
^ “Dalakima” imeneyi inali yofanana ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inkalemera magalamu 8.4. Koma si yofanana ndi dalakima yomwe imatchulidwa mʼMalemba a Chigiriki. Onani Zakumapeto B14.
^ “Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”