Numeri 1:1-54

  • Kalembera wa amuna oyenera kupita kunkhondo (1-46)

  • Alevi sankayenera kupita nawo kunkhondo (47-51)

  • Dongosolo lomangira matenti mumsasa (52-54)

1  Yehova analankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai,+ mʼchihema chokumanako.+ Analankhula naye pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri mʼchaka chachiwiri, atatuluka mʼdziko la Iguputo.+ Iye anati:  “Uwerenge+ gulu lonse la Aisiraeli* mogwirizana ndi mabanja awo, potengera nyumba za makolo awo, nʼkulemba mayina awo. Uwerenge amuna onse, mmodzi ndi mmodzi.  Iweyo ndi Aroni muwalembe mʼkaundula mogwirizana ndi magulu awo.* Uwerenge onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo,+ amene ali oyenera kupita kunkhondo mu Isiraeli.  Mutenge amuna ena kuti akuthandizeni. Mutenge mwamuna mmodzi pafuko lililonse ndipo akhale mtsogoleri wa nyumba ya makolo ake.+  Mayina a amuna amene akuthandizeni ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Elizuri+ mwana wa Sedeuri,  kuchokera ku fuko la Simiyoni, Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai,  kuchokera ku fuko la Yuda, Naasoni+ mwana wa Aminadabu,  kuchokera ku fuko la Isakara, Netaneli+ mwana wa Zuwara,  kuchokera ku fuko la Zebuloni, Eliyabu+ mwana wa Heloni. 10  Pa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efuraimu,+ Elisama mwana wa Amihudi, kuchokera ku fuko la Manase, Gamaliyeli mwana wa Pedazuri, 11  kuchokera ku fuko la Benjamini, Abidana+ mwana wa Gidiyoni, 12  kuchokera ku fuko la Dani, Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai, 13  kuchokera ku fuko la Aseri, Pagiyeli+ mwana wa Okirani, 14  kuchokera ku fuko la Gadi, Eliyasafu+ mwana wa Deyueli, 15  kuchokera ku fuko la Nafitali, Ahira+ mwana wa Enani. 16  Amenewa ndi amene anasankhidwa pa gulu la anthuwo. Iwo anali atsogoleri+ a mafuko a makolo awo, atsogoleri a anthu masauzande mu Isiraeli.”+ 17  Choncho Mose ndi Aroni anatenga amuna amenewa, amene mayina awo anatchulidwa. 18  Iwo anasonkhanitsa anthu onse pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri kuti munthu aliyense amulembe mʼkaundula mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawalemba mayina kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo+ 19  mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Choncho iye anawerenga anthuwo mʼchipululu cha Sinai.+ 20  Mbadwa za Rubeni, mwana woyamba wa Isiraeli,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 21  Anthu onse a fuko la Rubeni amene analembedwa mayina anakwana 46,500. 22  Mbadwa za Simiyoni,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 23  Anthu onse a fuko la Simiyoni amene analembedwa mayina analipo 59,300. 24  Mbadwa za Gadi+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 25  Anthu onse a fuko la Gadi amene analembedwa mayina analipo 45,650. 26  Mbadwa za Yuda,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 27  Anthu onse a fuko la Yuda amene analembedwa mayina analipo 74,600. 28  Mbadwa za Isakara,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 29  Anthu onse a fuko la Isakara amene analembedwa mayina analipo 54,400. 30  Mbadwa za Zebuloni,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 31  Anthu onse a fuko la Zebuloni amene analembedwa mayina analipo 57,400. 32  Mbadwa za Yosefe za fuko la Efuraimu+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 33  Anthu onse a fuko la Efuraimu amene analembedwa mayina analipo 40,500. 34  Mbadwa za Manase+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 35  Anthu onse a fuko la Manase amene analembedwa mayina analipo 32,200. 36  Mbadwa za Benjamini,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 37  Anthu onse a fuko la Benjamini amene analembedwa mayina analipo 35,400. 38  Mbadwa za Dani,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 39  Anthu onse a fuko la Dani amene analembedwa mayina analipo 62,700. 40  Mbadwa za Aseri,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 41  Anthu onse a fuko la Aseri amene analembedwa mayina analipo 41,500. 42  Mbadwa za Nafitali,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 43  Anthu onse a fuko la Nafitali amene analembedwa mayina analipo 53,400. 44  Awa ndi amuna amene Mose ndi Aroni anawalemba mayina mothandizidwa ndi atsogoleri 12 a Isiraeli. Mtsogoleri aliyense ankaimira nyumba ya makolo ake. 45  Aisiraeli onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo mu Isiraeli, analembedwa mayina mogwirizana ndi nyumba za makolo awo. 46  Anthu onse amene analembedwa mayina anakwana 603,550.+ 47  Koma Alevi,+ mogwirizana ndi fuko la makolo awo, sanawawerenge pamodzi ndi anthu enawo.+ 48  Choncho Yehova anauza Mose kuti: 49  “Anthu a fuko la Levi okha usawalembe mayina, ndipo usaphatikize chiwerengero chawo pamodzi ndi cha Aisiraeli enawo.+ 50  Uike Alevi kuti aziyangʼanira chihema cha Umboni+ ndi ziwiya zake zonse komanso chilichonse cha mmenemo.+ Iwowo ndi amene azinyamula chihemacho ndi ziwiya zake zonse.+ Ndi amenenso azitumikira pachihemapo+ ndipo azimanga misasa yawo mozungulira chihemacho.+ 51  Nthawi zonse mukamasamutsa chihema, Aleviwo azichipasula,+ ndipo mukafika pomanga msasa, Alevi ndi amene azimanga chihemacho. Munthu aliyense amene si Mlevi akayandikira chihemacho aziphedwa.+ 52  Aisiraeli azimanga matenti awo mogwirizana ndi msasa wawo, munthu aliyense mogwirizana ndi gulu lake la mafuko atatu,+ potengera magulu awo.* 53  Alevi azimanga matenti awo mozungulira chihema cha Umboni kuti mkwiyo wa Mulungu usayakire Aisiraeli.+ Aleviwo ndi amene ali ndi udindo wosamalira* chihema cha Umbonicho.”+ 54  Aisiraeli anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Anachitadi zomwezo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “potengera magulu awo a asilikali.”
Kapena kuti, “wolondera; wotumikira pa.”