Numeri 10:1-36
10 Kenako Yehova anauza Mose kuti:
2 “Upange malipenga awiri+ asiliva. Uchite kusula, ndipo uziwagwiritsa ntchito poitanitsa msonkhano komanso posamutsa msasa.
3 Akaliza malipenga onse awiriwo, gulu lonse lizibwera kwa iwe pakhomo la chihema chokumanako.+
4 Koma akaliza lipenga limodzi lokha, akuluakulu amene ndi atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, azibwera kwa iwe.+
5 Mukaliza lipenga lolira mosinthasintha, anthu amene ali mʼmisasa yakumʼmawa+ azinyamuka.
6 Mukaliza kachiwiri lipenga lolira mosinthasintha, anthu amene ali mʼmisasa yakumʼmwera+ azinyamuka. Gulu lililonse likamanyamuka, aziliza lipenga lolira mosinthasintha.
7 Poitanitsa msonkhano wa anthu onse muziliza lipenga,+ koma osati lolira mosinthasintha.
8 Ana a Aroni, omwe ndi ansembe, ndi amene aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kuti muzigwiritsa ntchito malipengawa mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale.
9 Ngati mukufunika kumenya nkhondo mʼdziko lanu polimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipengawo+ posonyeza kuti mukuitanira asilikali kunkhondo. Mukatero, Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndipo adzakupulumutsani kwa adani anuwo.
10 Komanso pa nthawi ya zisangalalo+ zanu, monga pa zikondwerero+ zanu ndi kumayambiriro kwa miyezi, muziliza malipenga popereka nsembe zanu zopsereza+ ndi zamgwirizano.+ Kulira kwa malipengawo kudzachititsa kuti Mulungu akukumbukireni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”+
11 Tsopano mʼchaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20 la mweziwo,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni.
12 Choncho Aisiraeli ananyamuka mʼchipululu cha Sinai potsatira dongosolo lawo lonyamukira,+ ndipo mtambowo unakaima mʼchipululu cha Parana.+
13 Kameneka kanali koyamba kuti iwo asamuke motsatira malangizo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose.+
14 Choncho, gulu la mafuko atatu la ana a Yuda ndi limene linali loyamba kunyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu.
15 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Isakara anali Netaneli,+ mwana wa Zuwara.
16 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Zebuloni anali Eliyabu,+ mwana wa Heloni.
17 Chihema chitapasulidwa,+ ana a Gerisoni+ ndi ana a Merari,+ amene ankanyamula chihemacho, ananyamuka.
18 Kenako, gulu la mafuko atatu la ana a Rubeni linanyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Elizuri,+ mwana wa Sedeuri.
19 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Simiyoni anali Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai.
20 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Gadi anali Eliyasafu,+ mwana wa Deyueli.
21 Kenako Akohati, amene ankanyamula zinthu za mʼmalo opatulika+ ananyamuka, kuti akamakafika akapeze chihema chitamangidwa kale.
22 Ndiyeno gulu la mafuko atatu la ana a Efuraimu linanyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Elisama,+ mwana wa Amihudi.
23 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Manase anali Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri.
24 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Benjamini anali Abidana,+ mwana wa Gidiyoni.
25 Pomaliza, gulu la mafuko atatu la ana a Dani linanyamuka potengera magulu awo.* Iwo ndi amene ankalondera kumbuyo kwa magulu onse a mafukowo. Mtsogoleri wa gululi anali Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai.
26 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Aseri anali Pagiyeli,+ mwana wa Okirani.
27 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Nafitali anali Ahira,+ mwana wa Enani.
28 Dongosolo limene Aisiraeli ndi magulu awo* ankatsatira posamuka ndi limeneli.+
29 Ndiyeno Mose anauza Hobabu mwana wa mpongozi wake Reueli*+ wa ku Midiyani, kuti: “Tikusamukira kumalo amene Yehova anati, ‘Ndidzawapereka kwa inu.’+ Tiyeni tipite limodzi,+ ndipo tidzakuchitirani zabwino, chifukwa Yehova analonjeza Aisiraeli zinthu zabwino.”+
30 Koma iye anamuyankha kuti: “Ayi, sindipita nanu kumeneko. Ndibwerera kudziko lakwathu, kwa abale anga.”
31 Komabe Mose anamupempha kuti: “Chonde musatisiye, chifukwa inu mukudziwa bwino kumene tingamange msasa mʼchipululu muno, ndipo mungamatilondolere.*
32 Ngati mungapite nafe limodzi,+ madalitso amene Yehova adzatipatse inunso mudzalandira nawo.”
33 Choncho iwo ananyamuka kuphiri la Yehova,+ nʼkuyenda ulendo wa masiku atatu. Likasa+ la pangano la Yehova linali patsogolo pawo ulendo wa masiku atatu wonsewo, mpaka atapeza malo oti amangepo msasa.+
34 Akanyamuka pamsasa masana, mtambo wa Yehova+ unkakhala pamwamba pawo.
35 Nthawi zonse Likasa likamanyamuka, Mose ankanena kuti: “Nyamukani, inu Yehova,+ adani anu abalalike. Ndipo amene amadana nanu athawe pamaso panu.”
36 Nthawi zonse likasalo likaima, iye ankanena kuti: “Bwererani inu Yehova, kwa Aisiraeli masauzande osawerengeka.”*+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
^ Kapena kuti, Yetero.
^ Kapena kuti, “mungakhale maso athu.”
^ Kapena kuti, “kwa Aisiraeli miyandamiyanda.”