Numeri 11:1-35

  • Mulungu anawabweretsera moto chifukwa chodandaula (1-3)

  • Anthu anayamba kulirira nyama (4-9)

  • Mose ankadziona kuti ndi wosayenerera (10-15)

  • Yehova anapereka mzimu kwa akulu 70 (16-25)

  • Eledadi ndi Medadi; Yoswa anachita nsanje chifukwa choti ankadera nkhawa Mose (26-30)

  • Anabweretsa zinziri; anthu analangidwa chifukwa cha dyera (31-35)

11  Tsopano anthuwo anayamba kudandaula kwambiri pamaso pa Yehova. Yehova atamva kudandaulako mkwiyo wake unayaka, ndipo moto wochokera kwa Yehova unawayakira nʼkupsereza ena mwa anthuwo kumalire a msasa.  Koma anthuwo atayamba kulirira Mose, iye anapembedzera Yehova+ ndipo motowo unazima.  Choncho malowo anawatchula kuti Tabera,* chifukwa moto wochokera kwa Yehova unawayakira pamalo amenewo.+  Kenako gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ lomwe linali pakati pawo linasonyeza mtima wadyera,+ ndipo Aisiraeli nawonso anayamba kulira nʼkumanena kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye?+  Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!+  Koma pano tilibe ndi mphamvu zomwe. Sitikuonanso chilichonse kupatulapo manawa.”+  Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo ankaoneka ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi.  Anthuwo ankamwazikana kukatola manawo. Akatero, ankawapera pamphero kapena kuwasinja mumtondo. Kenako ankawawiritsa mumphika, kapena kuwapanga makeke ozungulira+ ndipo ankakoma ngati keke yotsekemera yothira mafuta.  Mame akagwa pamsasa usiku, mananso ankagwa.+ 10  Mose anamva anthu akulira mʼbanja lililonse, munthu aliyense pakhomo la tenti yake. Ndipo Yehova anakwiya kwambiri+ komanso Mose anakhumudwa kwambiri. 11  Ndiyeno Mose anauza Yehova kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandivutitsa chonchi ine mtumiki wanu? Nʼchifukwa chiyani mwandiumira mtima chonchi, nʼkundisenzetsa chimtolo cha anthu onsewa?+ 12  Kodi ndine ndinatenga pakati pa anthu onsewa? Ndine kodi ndinawabereka, kuti mundiuze kuti, ‘Uwanyamule pachifuwa chako mmene wantchito yolera mwana amanyamulira mwana woyamwa,’ pa ulendo wopita nawo kudziko limene munalumbira kuti mudzalipereka kwa makolo awo?+ 13  Kodi nyama yoti ndipatse anthu onsewa ndiitenga kuti? Chifukwa iwo akupitirizabe kundilirira kuti, ‘Tipatse nyama yoti tidye!’ 14  Sindingathe kuwasamalira ndekha anthu onsewa. Ntchito imeneyi yandikulira.+ 15  Ngati izi ndi zimene muzindichitira kuli bwino mungondipha pompano.+ Koma ngati mwandikomera mtima, musandionetsenso tsoka lina.” 16  Yehova anayankha Mose kuti: “Undisonkhanitsire akulu 70 pakati pa akulu a Isiraeli, amene umawaona* kuti ndi akulu komanso oyangʼanira pakati pa anthuwo.+ Upite nawo kuchihema chokumanako, ndipo akaime kumeneko limodzi ndi iwe. 17  Ine ndibwera kumeneko+ kudzalankhula nawe+ ndipo ndidzatenga gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe nʼkuuika pa anthuwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyangʼanira anthuwo, kuti usausenze wekha.+ 18  Anthuwo uwauze kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera mawa,+ chifukwa mudya nyama. Paja mwakhala mukulirira Yehova+ kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye? Ku Iguputo zinthu zinkatiyendera bwino.”+ Yehova akupatsanidi nyamayo ndipo mudya.+ 19  Nyamayo simuidya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku 5, kapena masiku 10, kapenanso masiku 20 ayi, 20  koma mudzaidya kwa mwezi wonse wathunthu, mpaka idzatulukira mʼmphuno mwanu, ndipo mudzachita kunyansidwa nayo.+ Zidzatero chifukwa mwakana Yehova amene ali pakati panu, ndipo mumamulirira kuti: “Tinachokeranji ku Iguputo?”’”+ 21  Ndiyeno Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo alipo 600,000,+ koma inu mwanena kuti, ‘Ndiwapatsa nyama yokwanira kudya mwezi wonse wathunthu.’ 22  Kodi titapha ziweto zonse zingawakwanire? Kapena titapha nsomba zonse zamʼnyanja, kodi zingawakwanire?” 23  Ndiyeno Yehova anayankha Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?+ Tsopano uona ngati zimene ndanenazi zichitike kapena ayi.” 24  Choncho Mose anapita kukauza anthuwo mawu a Yehova. Iye anasonkhanitsa amuna 70 kuchokera pakati pa akulu a anthuwo, nʼkuwauza kuti aimirire mozungulira chihema chokumanako.+ 25  Kenako Yehova anatsika mumtambo+ nʼkulankhula naye.+ Anatengako gawo lina la mzimu+ umene unali pa Mose nʼkuuika pa aliyense wa akulu 70 amenewo. Ndipo mzimuwo utangokhala pa iwo, anayamba kuchita zinthu ngati aneneri,*+ koma anangochita zimenezi kamodzi kokhaka. 26  Ndiyeno panali amuna awiri amene anatsalira mumsasa. Mayina awo anali Eledadi ndi Medadi. Amenewanso analandira mzimuwo chifukwa anali mʼgulu la anthu amene analembedwa mayina, koma sanapite nawo kuchihema. Choncho iwonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri mumsasamo. 27  Ndiye mnyamata wina anathamanga kukanena kwa Mose kuti: “Eledadi ndi Medadi akuchita zinthu ngati aneneri mumsasa.” 28  Kenako Yoswa+ mwana wa Nuni, yemwe anali mtumiki wa Mose kuyambira ali mnyamata, anayankhira kuti: “Mbuyanga Mose, kawaletseni amenewo!”+ 29  Koma Mose anayankha kuti: “Kodi ukuchita nsanje chifukwa chondidera nkhawa? Ayi usatero. Ndikanakonda anthu onse a Yehova akanakhala aneneri komanso Yehova akanaika mzimu wake pa iwo!” 30  Pambuyo pake, Mose limodzi ndi akulu a Isiraeliwo anabwerera kumsasa. 31  Kenako Yehova anabweretsa mphepo yamphamvu kuchokera kunyanja. Mphepoyo inabweretsa zinziri, ndipo inazimwaza kuzungulira msasawo+ mpaka pamtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali zonse za msasawo. Inazimwaza kuzungulira msasawo, moti zinaunjikana mulu wokwana pafupifupi masentimita 90* kuchokera pansi. 32  Ndiyeno anthuwo anayamba kugwira zinzirizo. Anazigwira masana onse, usiku wonse, mpakanso tsiku lotsatira osapuma. Palibe amene anagwira zosakwana mahomeri* 10 ndipo ankaziyanika paliponse, moti zinangoti mbwee, pamsasa wonsewo. 33  Koma nyamayo idakali mʼkamwa mwawo, asanaitafune nʼkomwe, mkwiyo wa Yehova unayakira anthuwo. Ndipo Yehova anayamba kuwalanga moti anthu ambiri anaphedwa.+ 34  Malo amenewo anawatchula kuti Kibiroti-hatava,*+ chifukwa anakwirirapo anthu amene anasonyeza mtima wadyera.+ 35  Anthuwo atachoka pa Kibiroti-hatava, anasamukira ku Hazeroti,+ ndipo anakhala kumeneko.

Mawu a M'munsi

Dzina limeneli limatanthauza “Kuyaka; moto walawilawi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “njere ya koriyanda.” Koriyanda ndi chomera chimene ena amati “masala,” ndipo njere yake ndi yoyera ngati mapira.
Kapena kuti, “amene ukuwadziwa.”
Kapena kuti, “anayamba kunenera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono iwiri.” Onani Zakumapeto B14.
Homeri imodzi inali yofanana ndi malita 220. Onani Zakumapeto B14.
Kutanthauza kuti, “Manda a Anthu Adyera.”