Numeri 12:1-16

  • Miriamu ndi Aroni anakangana ndi Mose (1-3)

    • Mose anali wofatsa kuposa munthu aliyense (3)

  • Yehova anaikira kumbuyo Mose (4-8)

  • Miriamu anachita khate (9-16)

12  Tsopano Miriamu ndi Aroni anayamba kumunena Mose chifukwa cha mkazi wa Chikusi+ amene anamukwatira.  Iwo ankanena kuti: “Kodi Yehova walankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sanalankhulenso kudzera mwa ife?”+ Koma Yehova ankamvetsera.+  Mose anali munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse*+ amene anali padziko lapansi.  Kenako mwadzidzidzi Yehova anauza Mose, Aroni ndi Miriamu kuti: “Nonse atatu nyamukani, mupite kuchihema chokumanako.” Choncho onse atatu ananyamuka nʼkupita.  Ndiyeno Yehova anatsika mʼchipilala chamtambo+ nʼkuima pakhomo la chihema chokumanako. Kenako anaitana Aroni ndi Miriamu ndipo onse anapita.  Iye anawauza kuti: “Mvetserani mawu anga. Pakanakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndikanamudziwitsa za ine mʼmasomphenya,+ ndipo ndikanalankhula naye mʼmaloto.+  Koma sindinachite zimenezo ndi mtumiki wanga Mose. Ndaika anthu anga onse Aisiraeli mʼmanja mwake.*+  Ndimalankhula naye pamasomʼpamaso,*+ kumuuza zinthu momveka bwino osati mophiphiritsa, ndipo amaona maonekedwe a Yehova. Ndiye nʼchifukwa chiyani inu simunaope kumunena Mose mtumiki wanga?”  Choncho Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuchokapo. 10  Mtambo uja unachoka pamwamba pa chihemacho. Pomwepo, Miriamu anagwidwa ndi khate loyera kwambiri.+ Kenako Aroni atatembenuka nʼkumuyangʼana Miriamu, anaona kuti wachita khate.+ 11  Nthawi yomweyo Aroni anachonderera Mose kuti: “Pepani mbuyanga, chonde, musatilange chifukwa cha tchimo limene tachitali. Zimene tachitazi ndi zinthu zopusa. 12  Chonde, musamusiye Miriamu kuti akhale ngati mwana wobadwa wakufa, amene mnofu wake ndi wowola mbali ina.” 13  Ndiyeno Mose anayamba kufuulira Yehova kuti: “Chonde Mulungu wanga, muchiritseni chonde!”+ 14  Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanamulavulira malovu kumaso, sakanakhala wonyozeka kwa masiku 7? Ndiye mʼtulutseni akakhale kunja kwa msasa+ kwa masiku 7, pambuyo pake mumulowetsenso mumsasamo.” 15  Choncho Miriamu anatulutsidwa kukakhala kunja kwa msasa kwa masiku 7,+ ndipo anthuwo sanasamuke mpaka Miriamu atamubweretsanso mumsasa. 16  Kenako anthuwo anachoka ku Hazeroti,+ nʼkukamanga msasa mʼchipululu cha Parana.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anali wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye wasonyeza kuti ndi wokhulupirika mʼnyumba mwanga monse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwamʼpakamwa.”