Numeri 13:1-33

  • Anatumiza anthu 12 kuti akafufuze zokhudza dziko la Kanani (1-24)

  • Anthu 10 anabweretsa lipoti loipa (25-33)

13  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose kuti:  “Utume amuna kuti akazonde* dziko la Kanani limene ndikulipereka kwa Aisiraeli. Pa fuko lililonse utume mwamuna mmodzi, ndipo akhale mtsogoleri+ wa fuko lawo.”+  Choncho Mose anatumiza amunawo kuchokera kuchipululu cha Parana,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula. Amuna onsewo anali atsogoleri a Aisiraeli.  Mayina awo ndi awa: Wa fuko la Rubeni anali Samuwa, mwana wa Zakuri.  Wa fuko la Simiyoni anali Safati, mwana wa Hori.  Wa fuko la Yuda anali Kalebe,+ mwana wa Yefune.  Wa fuko la Isakara anali Igali, mwana wa Yosefe.  Wa fuko la Efuraimu anali Hoshiya,+ mwana wa Nuni.  Wa fuko la Benjamini anali Paliti, mwana wa Rafu. 10  Wa fuko la Zebuloni anali Gadiyeli, mwana wa Sodi. 11  Wa fuko la Yosefe,+ kuimira fuko la Manase,+ anali Gadidi mwana wa Susi. 12  Wa fuko la Dani anali Amiyeli, mwana wa Gemali. 13  Wa fuko la Aseri anali Seturi, mwana wa Mikayeli. 14  Wa fuko la Nafitali anali Nabi, mwana wa Vopisi. 15  Wa fuko la Gadi anali Geyuweli, mwana wa Maki. 16  Mayina a amuna amene Mose anawatuma kuti akazonde dzikolo ndi amenewa. Mose anapatsa Hoshiya mwana wa Nuni dzina lakuti Yoswa.*+ 17  Powatumiza kuti akazonde dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Mupite kumeneko kudzera ku Negebu, ndipo kenako mukafike kudera lamapiri.+ 18  Mukaone kuti dzikolo ndi lotani.+ Mukaonenso ngati anthu amʼdzikomo ndi amphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ali ochepa kapena ambiri. 19  Mukaone ngati dzikolo lili labwino kapena loipa, ndiponso ngati mizinda imene akukhala ilibe mipanda kapena ngati ili ndi mipanda yolimba kwambiri. 20  Komanso mukaone ngati dzikolo lili lachonde kapena lopanda chonde,+ ngati lili ndi mitengo kapena ayi. Mukalimbe mtima+ nʼkutengako zipatso zamʼdzikomo.” Imeneyi inali nthawi imene mphesa zoyamba zinkapsa.+ 21  Choncho amunawo anapita kukazonda dzikolo, kuyambira kuchipululu cha Zini+ mpaka ku Rehobu,+ kufupi ndi Lebo-hamati.*+ 22  Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ omwe ndi Aanaki.*+ Mzinda wa Heburoni unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani wa ku Iguputo usanamangidwe. 23  Atafika kuchigwa cha Esikolo,*+ anadula nthambi yokhala ndi phava limodzi lalikulu la mphesa, ndipo anthu awiri analinyamula paphewa ndi ndodo yonyamulira. Anatengakonso makangaza* ndi nkhuyu.+ 24  Malowo anawapatsa dzina lakuti chigwa cha Esikolo,*+ chifukwa chakuti Aisiraeliwo anadulapo phava la mphesa. 25  Patatha masiku 40,+ anabwerako kokazonda dziko kuja. 26  Iwo anabwerera kwa Mose ndi Aroni ndiponso gulu lonse la Aisiraeli mʼchipululu cha Parana, ku Kadesi.+ Anafotokozera gulu lonselo za ulendo wawo nʼkuwaonetsa zipatso za kudzikolo. 27  Iwo anauza Mose kuti: “Tinakalowa mʼdziko limene munatituma lija ndipo ndi dziko loyendadi mkaka ndi uchi,+ moti zipatso zake ndi izi.+ 28  Ngakhale zili choncho, anthu okhala kumeneko ndi anthu amphamvu zawo, ndipo ali ndi mizinda ikuluikulu yotchingidwa ndi mipanda yolimba kwambiri. Si zokhazo, taonanso Aanaki kumeneko.+ 29  Aamaleki+ akukhala ku Negebu.+ Ahiti, Ayebusi+ ndi Aamori+ akukhala kudera lamapiri. Akanani+ akukhala mʼmphepete mwa nyanja+ ndi mʼmphepete mwa mtsinje wa Yorodano.” 30  Kenako Kalebe anayesa kukhazika anthuwo mtima pansi pamaso pa Mose ponena kuti: “Tiyeni tipite pompano, tikatenga dzikolo kukhala lathu, chifukwa tingathe kuwagonjetsa anthuwo.”+ 31  Koma amuna amene anapita naye limodzi ananena kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.”+ 32  Ndipo iwo anapitiriza kuuza Aisiraeliwo lipoti loipa+ lokhudza dziko limene anakalizondalo kuti: “Dziko limene tinakalizondalo limameza anthu ake, ndipo anthu onse amene tinawaona kumeneko ndi ziphona zamatupi akuluakulu.+ 33  Tinaonakonso Anefili,* ana a Anaki+ omwe ndi mbadwa za Anefili, moti tikadziyerekezera ndi iwowo, ifeyo timangooneka ngati tiziwala. Iwonso ndi mmene amationera.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akafufuze.”
Kapena kuti, “Yehoswa,” kutanthauza kuti “Yehova Ndi Chipulumutso.”
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Aanaki anali anthu amatupi akuluakulu komanso amphamvu kwambiri.
Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.” Dzinali limatanthauza “Phava la Mphesa.”
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Ogwetsa” kutanthauza amene amagwetsa anthu ena. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.