Numeri 16:1-50
16 Kenako Kora+ mwana wa Izara,+ mwana wa Kohati,+ mwana wa Levi,+ anagwirizana ndi adzukulu a Rubeni,+ omwe ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliyabu,+ komanso Oni mwana wa Pelete, kuti aukire.
2 Iwo limodzi ndi amuna a Chiisiraeli okwana 250 anaukira Mose. Amunawa anali atsogoleri a anthuwo, amuna osankhidwa pakati pa Aisiraeli, amuna otchuka.
3 Choncho iwo anasonkhana nʼkuyamba kutsutsana+ ndi Mose ndi Aroni kuti: “Tatopa nanu tsopano. Gulu lonseli ndi loyera,+ ndipo Yehova ali pakati pawo.+ Nanga nʼchifukwa chiyani inu mukudzikweza pa mpingo wa Yehova?”
4 Mose atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.
5 Ndiyeno Mose anauza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti: “Mawa mʼmamawa, Yehova adzasonyeza munthu amene ali wake+ ndiponso amene ali woyera, amene ali woyenera kuyandikira pamaso pake.+ Ndipo amene ati adzamusankheyo+ adzayandikira pamaso pake.
6 Mudzachite izi: Iweyo Kora ndi anthu onse amene akukutsatira+ mudzatenge zofukizira.+
7 Mʼzofukizirazo mudzaikemo moto komanso zofukiza nʼkubwera nazo pamaso pa Yehova mawa. Munthu amene Yehova adzamusankhe,+ ndi amene ali woyera. Inu ana a Levi+ mwawonjeza kwambiri.”
8 Ndiyeno Mose anauza Kora kuti: “Tamverani, inu ana a Levi.
9 Kodi mukuyesa nʼchinthu chachingʼono kuti Mulungu wa Isiraeli anakupatulani pakati pa Aisiraeli,+ nʼkukulolani kuti muzifika pamaso pa Yehova kuti muzimutumikira pachihema chake komanso kutumikira gulu lonselo?+
10 Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti Mulungu anakubweretsani pafupi ndi iye limodzi ndi abale anu onse, ana a Levi? Kodi tsopano mukufunanso udindo waunsembe?+
11 Chifukwa cha zimene mukuchitazi, iweyo limodzi ndi anthu onse amene akukutsatira, mukuukira Yehova. Kunena za Aroni, kodi iyeyo ndi ndani kuti mumudandaule?”+
12 Pambuyo pake, Mose anatuma munthu kuti akaitane Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu. Koma iwo anayankha kuti: “Ife sitibwerako kumeneko!
13 Kodi ukuyesa nʼchinthu chachingʼono kuti unatichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphere mʼchipululu muno?+ Kodi tsopano ukufunanso kuti ukhale mfumu yomatilamulira?
14 Si izi nanga, sunatifikitse kudziko lililonse loyenda mkaka ndi uchi+ kapena kutipatsa malo ndiponso minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuti amunawo uwakolowole maso? Tatitu kumeneko sitibwerako!”
15 Mose atamva zimenezi anakwiya kwambiri ndipo anauza Yehova kuti: “Nsembe zawo zambewu musaziyangʼane. Ine sindinawalande ngakhale bulu mmodzi, kapena kuchitira aliyense wa anthuwo chinthu choipa.”+
16 Kenako Mose anauza Kora kuti: “Mawa, iweyo ndi anthu onse amene akukutsatira mukaonekere pamaso pa Yehova. Mukaonekere, iweyo, anthuwo komanso Aroni.
17 Aliyense adzatenge chofukizira chake nʼkuikamo zofukiza, ndipo aliyense adzabweretse chofukizira chake pamaso pa Yehova. Zofukizirazo zidzakhale zokwana 250, komanso iweyo ndi Aroni aliyense adzakhale ndi chake.”
18 Choncho aliyense wa iwo anatenga chofukizira chake nʼkuikamo moto ndi zofukiza. Atatero, anakaima pakhomo la chihema chokumanako limodzi ndi Mose ndi Aroni.
19 Kora atasonkhanitsa anthu onse omutsatira+ kuti atsutsane nawo pakhomo la chihema chokumanako, ulemerero wa Yehova unaonekera ku gulu lonselo.+
20 Tsopano Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti:
21 “Chokani pakati pa gululi, kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.”+
22 Anthuwo atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, nʼkunena kuti: “Chonde Mulungu, inu Mulungu amene amapereka moyo kwa anthu onse,*+ kodi mukupsera mtima gulu lonseli+ chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi yekha?”
23 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:
24 “Uza gulu lonselo kuti, ‘Musayandikire matenti a Kora, Datani ndi Abiramu!’”+
25 Kenako Mose ananyamuka nʼkupita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akulu+ a Isiraeli anapita naye limodzi.
26 Atafika anauza gululo kuti: “Chonde, chokani kumatenti a anthu oipawa, ndipo musakhudze chinthu chawo chilichonse, kuti musaphedwe nawo limodzi chifukwa cha tchimo lawo.”
27 Nthawi yomweyo anthuwo anachoka kumbali zonse za matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Zitatero, Datani ndi Abiramu anatuluka nʼkuima pamakomo a matenti awo, limodzi ndi akazi awo, ana awo aamuna komanso ana awo angʼonoangʼono.
28 Ndiyeno Mose anati: “Mudziwira izi kuti Yehova ndi amene wandituma kuti ndichite zonsezi, ndiponso kuti si zamʼmaganizo mwanga:*
29 Ngati anthuwa angafe mmene anthu onse amafera, ndiponso ngati chilango chawo chingakhale chofanana ndi chimene anthu onse amapatsidwa, ndiye kuti Yehova sananditume.+
30 Koma ngati Yehova angawachitire chinthu chachilendo, kuti nthaka ingʼambike* nʼkuwameza ndi zonse zimene ali nazo, moti iwo nʼkutsikira ku Manda* ali amoyo, zikatero mudziwa ndithu kuti amunawa anyoza Yehova.”
31 Mose atangomaliza kulankhula mawu amenewa, nthaka imene iwo anapondapo inangʼambika.+
32 Nthakayo inangʼambika* nʼkuwameza limodzi ndi mabanja awo komanso anthu ena onse amene anali kumbali ya Kora+ pamodzi ndi katundu wawo yense.
33 Choncho iwo pamodzi ndi onse amene anali kumbali yawo analowa mʼManda* ali amoyo. Nthaka inawakwirira, moti iwo anawonongedwa pakati pa mpingo wonse.+
34 Aisiraeli onse amene anali pamalopo anayamba kuthawa atamva kufuula kwawo, ndipo anati: “Tikuopa kuti nthaka ingatimeze!”
35 Kenako moto unachokera kwa Yehova+ ndipo unapsereza amuna 250 omwe ankapereka nsembe zofukiza aja.+
36 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:
37 “Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse pamoto zofukizirazo+ chifukwa nʼzopatulika. Umuuzenso kuti amwaze motowo kutali.
38 Zofukizira za amuna amene anafa chifukwa cha kuchimwa kwawo azisule kuti zikhale timalata topyapyala ndipo mukutire guwa lansembe.+ Zofukizirazo zinakhala zopatulika chifukwa anafika nazo pamaso pa Yehova. Ndiye timalatato tikhale chikumbutso kwa Aisiraeli.”+
39 Choncho wansembe Eleazara anatenga zofukizira zakopa zimene anthu amene anapsa ndi moto aja anabweretsa, ndipo anazisula nʼkupanga timalata tokutira guwa lansembe,
40 mogwirizana ndi zimene Yehova anamuuza kudzera mwa Mose. Timalatato tinali chikumbutso kwa Aisiraeli kuti munthu wamba* amene si mbadwa ya Aroni asayandikire kwa Yehova kuti akapereke nsembe zofukiza.+ Anachita zimenezi kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi anthu amene ankamutsatira anachita.+
41 Koma tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisiraeli linayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose komanso Aroni+ kuti: “Mwapha anthu a Yehova inu.”
42 Anthuwo anasonkhana pamodzi kuti aukire Mose ndi Aroni, kenako anatembenuka nʼkuyangʼana kuchihema chokumanako. Atatero anangoona kuti mtambo waphimba chihemacho ndipo ulemerero wa Yehova wayamba kuonekera.+
43 Ndiyeno Mose ndi Aroni anakaima patsogolo pa chihema chokumanako,+
44 ndipo Yehova anauza Mose kuti:
45 “Amuna inu, chokani pakati pa anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.”+ Atamva zimenezi, iwo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
46 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Tenga chofukizira ndipo uikemo moto wochokera paguwa lansembe.+ Uikemonso nsembe yofukiza nʼkupita kwa anthuwo mofulumira kuti ukawaphimbire machimo awo.+ Chita zimenezi chifukwa Yehova wakwiya kwambiri ndipo mliri wayamba kale!”
47 Nthawi yomweyo Aroni anatenga chofukiziracho mogwirizana ndi zimene Mose anamuuza, nʼkuthamanga kukalowa pakati pa mpingowo. Koma mliri unali utayamba kale pakati pawo. Choncho Aroni anaika nsembe yofukiza ija pachofukiziracho nʼkuyamba kuphimbira anthuwo machimo.
48 Aroni anaimabe pakati pa akufa ndi amoyo, ndipo patapita nthawi mliriwo unaleka.
49 Amene anafa ndi mliriwo anakwana 14,700, osawerengera amene anafa chifukwa cha zochita za Kora aja.
50 Pa nthawi imene Aroni ankabwerera kwa Mose pakhomo la chihema chokumanako, mliriwo unali utaleka.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu wa mizimu ya zamoyo zonse.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “si zamumtima mwanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “itsegule pakamwa pake.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “inatsegula pakamwa pake.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo.”