Numeri 17:1-13

  • Ndodo ya Aroni inachita maluwa monga chizindikiro (1-13)

17  Tsopano Yehova anauza Mose kuti:  “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo utenge ndodo imodzi kuchokera ku fuko lililonse, kwa mtsogoleri wa fukolo.+ Zikhalepo ndodo 12 ndipo ulembe dzina la mtsogoleri aliyense pa ndodo yake.  Pandodo ya fuko la Levi ulembepo dzina la Aroni, chifukwa ndodo iliyonse ikuimira mtsogoleri wa fuko.  Ndodozo uziike mʼchihema chokumanako, patsogolo pa Umboni,+ pamene ndimakumana nawe nthawi zonse.+  Ndodo ya munthu amene ndimusankheyo+ idzaphuka, ndipo ndidzathetsa kungʼungʼudza kwa Aisiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine+ komanso motsutsana ndi iwe.”+  Choncho Mose analankhula ndi Aisiraeli ndipo atsogoleri awo onse anapereka ndodo zawo. Mtsogoleri aliyense anapereka ndodo imodzi ya fuko lake. Panali ndodo 12, ndipo imodzi inali ya Aroni.  Ndiyeno Mose anakaika ndodozo pamaso pa Yehova mʼchihema cha Umboni.  Tsiku lotsatira, Mose atalowa mʼchihema cha Umbonicho, anangoona kuti ndodo ya Aroni yoimira nyumba ya Levi yaphuka. Ndodoyo inali itaphuka ndipo inkamasula maluwa komanso kubereka zipatso za amondi zakupsa.  Kenako Mose anatenga ndodo zonse pamaso pa Yehova nʼkupita nazo kwa Aisiraeli onse. Atsogoleri aja anayangʼana ndodozo, ndipo aliyense anatengapo yake. 10  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Bwezera ndodo ya Aroni+ patsogolo pa Umboni. Uisunge kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana opandukawa,+ nʼcholinga chakuti asiye kungʼungʼudza motsutsana ndi ine komanso kuti asafe.” 11  Nthawi yomweyo Mose anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Anachitadi zomwezo. 12  Ndiyeno Aisiraeli anauza Mose kuti: “Tsopano ife tifa. Ndithudi titha ife. Tonse titha basi. 13  Aliyense amene ayerekeze kuyandikira chihema cha Yehova afa.+ Koma zoona ife tife mwa njira imeneyi?”+

Mawu a M'munsi