Numeri 2:1-34

  • Msasa anaugawa mʼmagulu a mafuko atatu (1-34)

    • Gulu la mafuko atatu la Yuda linali mbali yakumʼmawa (3-9)

    • Gulu la mafuko atatu la Rubeni linali mbali yakumʼmwera (10-16)

    • Msasa wa Alevi unali pakati (17)

    • Gulu la mafuko atatu la Efuraimu linali mbali yakumadzulo (18-24)

    • Gulu la mafuko atatu la Dani linali mbali yakumpoto (25-31)

    • Chiwerengero cha amuna onse amene analembedwa (32-34)

2  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni kuti:  “Aisiraeli azikhoma matenti awo, pamalo amene gulu lawo la mafuko atatu+ lapatsidwa, munthu aliyense azikhala pafupi ndi chizindikiro cha nyumba ya makolo ake. Iwo azikhoma matenti awo mozungulira chihema chokumanako komanso moyangʼana chihemacho.  Amene azimanga msasa wawo kumʼmawa kotulukira dzuwa ndi gulu la mafuko atatu la Yuda ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Yuda ndi Naasoni,+ mwana wa Aminadabu.  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 74,600.+  Pafupi ndi fuko limeneli kuzikhala fuko la Isakara. Mtsogoleri wa ana a Isakara ndi Netaneli,+ mwana wa Zuwara.  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 54,400.+  Kenako pazibwera fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa ana a Zebuloni ndi Eliyabu,+ mwana wa Heloni.  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 57,400.+  Asilikali onse a gulu la Yuda amene analembedwa mayina alipo 186,400. Amenewa azikhala oyamba kunyamuka.+ 10  Amene azimanga msasa wawo kumʼmwera ndi gulu la mafuko atatu la Rubeni+ ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Rubeni ndi Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 11  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 46,500.+ 12  Pafupi ndi fuko limeneli pazikhala fuko la Simiyoni. Mtsogoleri wa ana a Simiyoni ndi Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 13  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 59,300.+ 14  Kenako pazibwera fuko la Gadi. Mtsogoleri wa ana a Gadi ndi Eliyasafu,+ mwana wa Reueli. 15  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 45,650.+ 16  Asilikali onse a gulu la Rubeni amene analembedwa mayina alipo 151,450. Amenewa azikhala achiwiri kunyamuka.+ 17  Posamutsa chihema chokumanako,+ gulu la Alevi lizikhala pakati pa magulu enawo. Dongosolo limene azitsatira posamuka,+ ndi limenenso azitsatira pomanga misasa yawo, aliyense pamalo ake, mogwirizana ndi gulu lawo la mafuko atatu. 18  Amene azimanga msasa wawo kumadzulo ndi gulu la mafuko atatu la Efuraimu ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Efuraimu ndi Elisama,+ mwana wa Amihudi. 19  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 40,500.+ 20  Pafupi ndi fuko limeneli pazibwera fuko la Manase.+ Mtsogoleri wa ana a Manase ndi Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 21  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 32,200.+ 22  Kenako pazibwera fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa ana a Benjamini ndi Abidana,+ mwana wa Gidiyoni. 23  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 35,400.+ 24  Asilikali onse a gulu la Efuraimu amene anawalemba mayina alipo 108,100. Amenewa azikhala achitatu kunyamuka.+ 25  Amene azimanga msasa wawo kumpoto ndi gulu la mafuko atatu la Dani ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Dani ndi Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 62,700.+ 27  Pafupi ndi fuko limeneli pazibwera fuko la Aseri. Mtsogoleri wa ana a Aseri ndi Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 28  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 41,500.+ 29  Kenako pazibwera fuko la Nafitali. Mtsogoleri wa ana a Nafitali ndi Ahira,+ mwana wa Enani. 30  Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 53,400.+ 31  Asilikali onse a gulu la Dani amene analembedwa mayina alipo 157,600. Amenewa azikhala omalizira kunyamuka,+ mogwirizana ndi magulu a Aisiraeli a mafuko atatuatatu.” 32  Amenewa ndi Aisiraeli amene mayina awo analembedwa, mogwirizana ndi nyumba ya makolo awo. Asilikali onse amene analembedwa mayina mʼmagulu onse, analipo 603,550.+ 33  Koma Alevi sanawawerenge+ pamodzi ndi Aisiraeli enawo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 34  Aisiraeli anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Dongosolo limene analitsatira pomanga misasa yawo mʼmagulu a mafuko atatu,+ ndi limenenso anatsatira posamuka,+ aliyense mʼbanja lake mogwirizana ndi nyumba ya makolo ake.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”