Numeri 21:1-35

  • Mfumu ya ku Aradi inagonjetsedwa (1-3)

  • Njoka yakopa (4-9)

  • Aisiraeli anayenda mozungulira Mowabu (10-20)

  • Sihoni Mfumu ya Aamori inagonjetsedwa (21-30)

  • Ogi Mfumu ya Aamori inagonjetsedwa (31-35)

21  Mfumu ya Akanani ya ku Aradi+ yomwe inkakhala ku Negebu itamva kuti Aisiraeli akubwera kudzera njira ya ku Atarimu, inapita kukamenyana nawo ndipo inagwira Aisiraeli ena nʼkupita nawo kudziko lake.  Aisiraeli ataona zimenezo, analonjeza Yehova kuti: “Mukapereka anthuwa mʼmanja mwathu, ndithu ifenso tidzawononga mizinda yawo.”  Choncho Yehova anamva mawu a Aisiraeli ndipo anapereka Akananiwo mʼmanja mwawo. Aisiraeli anawononga Akananiwo limodzi ndi mizinda yawo. Nʼchifukwa chake malowo anawatchula kuti Horima.*+  Pamene Aisiraeliwo ankapitiriza ulendo wawo kuchokera kuphiri la Hora+ kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira, pofuna kulambalala dziko la Edomu,+ anthuwo anatopa ndi ulendowo.  Choncho iwo anayamba kudandaula motsutsana ndi Mulungu komanso Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani munatitulutsa mʼdziko la Iguputo kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya komanso madzi,+ ndipo chakudya chonyansachi chafika potikola.”+  Ndiyeno Yehova anatumiza njoka zapoizoni* pakati pawo, ndipo zinayamba kuwaluma moti Aisiraeli ambiri anafa.+  Choncho anthuwo anapita kwa Mose nʼkumuuza kuti: “Tachimwa ife chifukwa cholankhula modandaula potsutsana ndi Yehova ndiponso inuyo.+ Tipepesereni kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Zitatero Mose anawapepesera kwa Mulungu.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Upange chifanizo cha njoka yapoizoni* ndipo uchiike pamtengo. Ndiye munthu aliyense akalumidwa, aziyangʼana chifanizocho kuti akhalebe ndi moyo.”  Nthawi yomweyo Mose anapanga njoka yakopa+ nʼkuiika pamtengo.+ Ndiye munthu akalumidwa ndi njoka nʼkuyangʼana njoka yakopayo, ankakhalabe ndi moyo.+ 10  Pambuyo pake Aisiraeli anasamuka nʼkukamanga msasa ku Oboti.+ 11  Kenako anasamuka ku Oboti nʼkukamanga msasa ku Iye-abarimu,+ mʼchipululu choyangʼanizana ndi dziko la Mowabu, chakumʼmawa. 12  Atachoka kumeneko anakamanga msasa mʼchigwa cha Zeredi.*+ 13  Atasamuka kumeneko anakamanga msasa mʼdera la chigwa cha Arinoni, mʼchipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni+ chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori. 14  Nʼchifukwa chake buku la Nkhondo za Yehova limanena za “Vahebi ku Sufa ndi zigwa za Arinoni.* 15  Mitsinje ya mʼzigwazo* imakafika ku Ari ndipo imayenda mʼmalire a dziko la Mowabu.” 16  Atachoka kumeneko anapita ku Beere. Kumeneku ndi kumene kunali chitsime chimene Yehova anauza Mose kuti: “Sonkhanitsa anthuwo kuti ndiwapatse madzi.” 17  Pa nthawi imeneyo Aisiraeli anaimba nyimbo yakuti: “Tulutsa madzi, chitsime iwe! Vomerezani* nyimboyi! 18  Chitsimechi chinakumbidwa ndi akalonga, chinafukulidwa ndi anthu olemekezeka,Anachifukula ndi ndodo ya mtsogoleri wa asilikali komanso ndodo zawo.” Kenako anachoka kuchipululuko nʼkupita ku Matana. 19  Atachoka ku Matana anapita ku Nahaliyeli ndipo atachoka ku Nahaliyeli anapita ku Bamoti.+ 20  Atachoka ku Bamoti anapita kuchigwa chimene chili mʼdziko la Mowabu,+ pafupi ndi chitunda cha Pisiga+ chimene chinayangʼanizana ndi dera la Yesimoni.*+ 21  Tsopano Aisiraeli anatuma anthu kuti apite kwa Sihoni mfumu ya Aamori kukanena kuti:+ 22  “Tiloleni tidutse mʼdziko lanu. Sitikhotera mʼmunda uliwonse kapena mʼmunda wa mpesa. Sitimwa madzi pachitsime chilichonse. Tizingoyenda mu Msewu wa Mfumu mpaka titadutsa mʼdziko lanu.”+ 23  Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adutse mʼdziko lake. Mʼmalomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkupita kukamenyana ndi Aisiraeli mʼchipululumo. Anakafika ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+ 24  Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ nʼkuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi Aamoni, chifukwa Yazeri+ anachita malire ndi Aamoni.+ 25  Choncho Aisiraeli analanda mizinda yonseyi nʼkuyamba kukhala mʼmizinda yonse ya Aamori+ ku Hesiboni ndi mʼmidzi yake yonse yozungulira. 26  Anayamba kukhala kumeneko chifukwa Hesiboni unali mzinda wa Sihoni, mfumu ya Aamori, amene anamenyana ndi mfumu ya Mowabu nʼkulanda dziko lake lonse mpaka kukafika kuchigwa cha Arinoni. 27  Nʼchifukwa chake pali ndakatulo yonyoza yakuti: “Bwerani ku Hesiboni. Mzinda wa Sihoni umangidwe nʼkukhala wolimba. 28  Chifukwa moto unatuluka ku Hesiboni, lawi lamoto linatuluka mʼtauni ya Sihoni. Wawotcha Ari mzinda wa ku Mowabu, wawotcha olamulira amʼmalo okwezeka a ku Arinoni. 29  Tsoka iwe Mowabu! Mudzawonongedwa, inu anthu a Kemosi!+ Iye adzapangitsa ana ake aamuna kukhala othawa kwawo, ndipo adzasandutsa ana ake aakazi kukhala akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori. 30  Tiyeni tiwalase.Hesiboni adzawonongedwa mpaka ku Diboni.+Tiyeni timusandutse bwinja mpaka ku Nofa,Moto udzafalikira mpaka ku Medeba.”+ 31  Choncho Aisiraeli anayamba kukhala mʼdziko la Aamori. 32  Kenako Mose anatumiza anthu ena kuti akazonde mzinda wa Yazeri.+ Atatero, Aisiraeliwo analanda midzi yozungulira mzindawo, nʼkuthamangitsa Aamori amene anali kumeneko. 33  Pambuyo pake, anatembenuka nʼkulowera Njira ya ku Basana. Ndiyeno Ogi+ mfumu ya ku Basana anabwera limodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nawo ku Edirei.+ 34  Yehova anauza Mose kuti: “Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndipereka iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse komanso dziko lake mʼmanja mwako+ ndipo umuchitire zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni.”+ 35  Choncho Aisiraeliwo anapha iyeyo, ana ake ndi anthu ake onse, moti palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka,+ ndipo analanda dziko lake.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Chinthu chimene chaperekedwa kuti chiwonongedwe.”
Kapena kuti, “njoka zamoto.”
Kapena kuti, “njoka yamoto.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa la Zeredi.”
Kapena kuti, “makhwawa a Arinoni.”
Kapena kuti, “mʼmakhwawamo.”
Kapena kuti, “Imbani.”
Mabaibulo ena amati, “chipululu.”