Numeri 22:1-41

  • Balaki analemba ganyu Balamu (1-21)

  • Bulu wa Balamu analankhula (22-41)

22  Kenako Aisiraeli ananyamuka nʼkukamanga msasa mʼchipululu cha Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko patsidya pa mtsinje wa Yorodano.+  Tsopano Balaki+ mwana wa Zipori, anaona zonse zimene Aisiraeli anachitira Aamori,  ndipo Amowabu anachita mantha kwambiri ndi anthuwo chifukwa anali ambiri. Iwo anagwidwa mantha aakulu chifukwa cha Aisiraeliwo.+  Choncho Amowabuwo anauza akuluakulu a ku Midiyani+ kuti: “Chigulu cha anthuchi chidzadya malo athu onse ngati mmene ngʼombe imadyera msipu kubusa.” Pa nthawi imeneyo, Balaki mwana wa Zipori ndi amene anali mfumu ya Mowabu.  Iye anatumiza anthu kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje* wamʼdziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane kuti: “Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja afika kuno. Iwo adzaza dziko lonse lapansi+ kumene munthu angayangʼane, ndipo akukhala pafupi penipeni ndi dziko langa.  Tsopano tabwerani chonde, mudzatemberere anthuwa+ chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo. Mwina ndingawagonjetse nʼkuwathamangitsa mʼdziko lino, chifukwa ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”  Choncho akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga ndalama zoti akamulipire kuti awawombezere maula, komanso anamuuza zimene Balaki ananena.  Balamu atamva mawuwo anawauza kuti: “Mugone konkuno, ndiyeno ndikuyankhani mogwirizana ndi zimene Yehova angandiuze.” Choncho akalonga a ku Mowabuwo anagonadi kwa Balamu.  Kenako Mulungu anafika kwa Balamu nʼkumufunsa kuti:+ “Kodi anthu uli nawowa ndi ndani?” 10  Balamu anayankha Mulungu woonayo kuti: “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu ndi amene watumiza anthuwa kuti adzandiuze kuti, 11  ‘Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja adzaza dziko lonse lapansi kumene munthu angayangʼane. Tsopano bwerani, mudzatemberere anthuwa.+ Mwina ndingathe kumenyana nawo nʼkuwathamangitsa.’” 12  Koma Mulungu anauza Balamu kuti: “Usapite nawo, ndipo anthuwo usawatemberere chifukwa ndi odalitsidwa.”+ 13  Balamu anadzuka mʼmamawa nʼkuuza akalonga a Balakiwo kuti: “Pitani kudziko lanu, chifukwa Yehova wakana kuti ndipite nanu.” 14  Choncho akalonga a ku Mowabuwo ananyamuka nʼkubwerera kwa Balaki, ndipo anakamuuza kuti: “Balamu wakana kubwera nafe.” 15  Koma Balaki anatumizanso akalonga ena, ochuluka komanso olemekezeka kuposa oyamba aja. 16  Iwo anapita kwa Balamu nʼkukamuuza kuti: “Balaki mwana wa Zipori wanena kuti, ‘Musalole kuti china chilichonse chikulepheretseni kubwera kwa ine, 17  chifukwa ndidzakupatsani mphoto yaikulu, ndipo ndidzachita chilichonse chimene mungandiuze. Chonde tabwerani mudzatemberere anthuwa.’” 18  Koma Balamu anayankha atumiki a Balakiwo kuti: “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse chosemphana ndi zimene Yehova Mulungu wanga angandilamule, kaya chachingʼono kapena chachikulu.+ 19  Bwanji inunso mugone konkuno usiku walero kuti ndimve zinanso zimene Yehova andiuze.”+ 20  Usikuwo Mulungu anafika kwa Balamu nʼkumuuza kuti: “Ngati anthuwa abwera kudzakuitana, pita nawo limodzi. Koma ukalankhule mawu okhawo amene ndikakuuze.”+ 21  Choncho Balamu anadzuka mʼmamawa nʼkumanga chishalo pabulu wake,* ndipo anapita limodzi ndi akalonga a ku Mowabu aja.+ 22  Koma Mulungu ataona kuti Balamu akupita, anapsa mtima ndipo mngelo wa Yehova anaima pamsewu kuti amutchingire njira. Balamuyo anali atakwera bulu wake, ndipo anali ndi anyamata ake awiri. 23  Ndiyeno buluyo ataona mngelo wa Yehova ataima pamsewu lupanga lake lili mʼmanja, anayesa kuchoka mumsewu nʼkupatukira kutchire. Koma Balamu anayamba kumʼkwapula kuti abwerere mumsewu. 24  Kenako mngelo wa Yehovayo anakaima panjira yopanikiza imene inali pakati pa minda iwiri ya mpesa ndipo njirayo inali ndi khoma lamiyala uku ndi uku. 25  Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anayamba kudzikanikizira kukhoma, moti anakanikiziranso phazi la Balamu kukhomako. Ndipo Balamu anayamba kumʼkwapulanso buluyo. 26  Tsopano mngelo wa Yehova anasunthiranso patsogolo nʼkukaima pamalo ena opanikiza, pomwe panalibiretu mpata woti nʼkudutsira kudzanja lamanja kapena lamanzere. 27  Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anangokhala pansi, Balamu ali pamsana pake. Choncho Balamu anapsa mtima koopsa, ndipo anapitiriza kumukwapula ndi ndodo yake. 28  Potsirizira pake, Yehova anachititsa kuti buluyo alankhule,*+ ndipo anafunsa Balamu kuti: “Kodi ndakulakwirani chiyani kuti mundikwapule katatu konseka?”+ 29  Balamu anayankha buluyo kuti: “Chifukwa wandipusitsa kwambiri. Moti ndikanakhala ndi lupanga mʼdzanja langa, bwenzi pano nʼtakupha!” 30  Buluyo anafunsanso Balamu kuti: “Kodi si ine bulu wanu amene mwakhala mukukwera moyo wanu wonse mpaka lero? Kodi ndinayamba ndachitapo zimenezi kwa inu?” Iye anayankha kuti: “Ayi!” 31  Kenako Yehova anatsegula maso a Balamu,+ ndipo anaona mngelo wa Yehova ataima panjirapo, lupanga lili mʼmanja. Nthawi yomweyo, Balamu anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi. 32  Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa ukupita kukachita zinthu zotsutsana ndi zimene ine ndikufuna.+ 33  Buluyu anandiona ndipo anayesa kundipatukira maulendo atatu onsewa.+ Akanapanda kundipatukira, bwenzi pano nʼtakupha. Koma buluyu nʼkanamusiya kuti akhale ndi moyo.” 34  Balamu anauza mngelo wa Yehovayo kuti: “Ndachimwa, sindinadziwe kuti inuyo munaima pamsewu kudzakumana nane. Koma ngati sizinakusangalatseni, ndikhoza kubwerera.” 35  Koma mngelo wa Yehovayo anauza Balamu kuti: “Pita nawo limodzi anthuwa, koma ukanene zokhazo zimene ndikuuze.” Choncho Balamu anapitiriza ulendo wake limodzi ndi akalonga a Balakiwo. 36  Balaki atamva kuti Balamu wafika, nthawi yomweyo ananyamuka kukamulandira kumzinda wa Mowabu. Mzindawu uli mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni, umene uli mʼmalire a dzikolo. 37  Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi sindinatumize anthu kuti adzakuitaneni? Nanga nʼchifukwa chiyani simunabwere? Kodi mukuganiza kuti ineyo sindingathe kukupatsani mphoto yaikulu?”+ 38  Balamu anayankha Balaki kuti: “Si ine ndabwerane! Koma kodi ndikuloledwa kunena chilichonse? Inetu ndilankhula mawu okhawo amene Mulungu angandiuze.”*+ 39  Choncho Balamu anatengana ndi Balaki, nʼkupita ku Kiriyati-huzoti. 40  Kumeneko Balaki anapereka nsembe zanyama ya ngʼombe ndi nkhosa, nʼkutumiza ina kwa Balamu ndi akalonga amene anali nawo limodzi. 41  Mʼmawa kutacha, Balaki anakatenga Balamu nʼkupita naye ku Bamoti-baala. Anapita naye kumeneko kuti akathe kuliona bwino gulu lonse la Aisiraeli.+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pabulu wamkazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatsegula pakamwa pa bulu wamkaziyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu okhawo amene Mulungu angaike mʼkamwa mwangamu.”