Numeri 23:1-30

  • Ndakatulo yoyamba ya Balamu (1-12)

  • Ndakatulo yachiwiri ya Balamu (13-30)

23  Kenako Balamu anauza Balaki kuti: “Mumange maguwa ansembe okwanira 7+ pamalo ano. Mukatero mundikonzere ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.” 2  Nthawi yomweyo Balaki anachita zimene Balamu anamuuza. Kenako Balaki ndi Balamu anapereka nsembe. Anapereka ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 3  Ndiyeno Balamu anauza Balaki kuti: “Mukhale pompano pafupi ndi nsembe yanu yopsereza ndipo ine ndichoka. Mwina Yehova alankhula nane ndipo zimene andiuzezo ndikuuzani.” Choncho Balamu anapita pamwamba pa phiri. 4  Kenako Mulungu anakumana ndi Balamu+ ndipo iye anauza Mulunguyo kuti: “Ndamanga maguwa ansembe 7 mʼmizere, ndipo ndapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.” 5  Yehova anauza Balamu+ zoti akanene.* Kenako anamuuza kuti: “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze mawu amenewa.” 6  Iye anabwerera kwa Balaki ndipo anapeza kuti Balakiyo limodzi ndi akalonga onse a ku Mowabu aima pafupi ndi nsembe yake yopsereza. 7  Kenako Balamu ananena ndakatulo yakuti:+ “Balaki mfumu ya Mowabu wandibweretsa kuno kuchokera ku Aramu,+Kuchokera kumapiri akumʼmawa kuti: ‘Bwera, udzanditembererere Yakobo. Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+  8  Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere? Ndipo ndingathe bwanji kuitanira tsoka anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka?+  9  Ndikutha kuwaona kuchokera pamwamba pa matanthwe pano,Ndipo ndikuwaona kuchokera pamwamba pa mapiri pano. Anthu amenewa akukhala paokhaokha.+Iwo akudziona kuti ndi osiyana ndi mitundu ina.+ 10  Ndani angathe kuwerenga mtundu wa Yakobo, womwe ndi wochuluka ngati fumbi+Kapena kuwerenga gawo limodzi mwa magawo 4 a Isiraeli? Ndisiyeni ndife imfa ya munthu wolungama,Ndipo mapeto anga akhale ngati awo.” 11  Kenako Balaki anauza Balamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandichitira zimenezi? Ndakubweretsani kuno kuti mudzatemberere adani anga, koma inu mwawadalitsa.”+ 12  Koma iye anamuyankha kuti: “Kodi sindikuyenera kulankhula zimene Yehova wandiuza?”*+ 13  Balaki anauza Balamu kuti: “Tiyeni tipite kumalo ena kumene mungathe kuwaona anthuwo. Simukaona onse, koma mukangoona ochepa. Mukatemberere amenewo.”+ 14  Choncho anamutengera ku Zofimu, pamwamba pa phiri la Pisiga.+ Kumeneko anamanga maguwa ansembe 7, nʼkupereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 15  Ndiyeno Balamu anauza Balaki kuti: “Mukhale pano, pafupi ndi nsembe yanu yopserezayi, koma ine ndikukalankhula ndi Mulungu uko.” 16  Kumeneko Yehova analankhuladi ndi Balamu nʼkumuuza zoti akanene kuti:*+ “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuuze zimene ndakuuza.” 17  Choncho Balamu anabwerera kwa Balaki, ndipo anamupeza akudikirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, akalonga a ku Mowabu ali naye limodzi. Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi Yehova wanena chiyani?” 18  Kenako Balamu anayambanso kulankhula mwa ndakatulo kuti:+ “Nyamuka, Balaki iwe, tamvera. Ndimvetsere, iwe mwana wa Zipori. 19  Mulungu sali ngati munthu amene amanena mabodza,+Sali ngati mwana wa munthu amene amasintha maganizo.*+ Akanena kanthu, kodi angalephere kuchita? Akalankhula, kodi angalephere kukwaniritsa?+ 20  Ine ndabwera kudzadalitsa,Tsopano Iye wadalitsa,+ ndipo sindingathe kusintha zimenezo.+ 21  Iye sangalole kuti mphamvu zilizonse zamatsenga zivulaze Yakobo,Ndipo sangalole kuti Isiraeli akumane ndi vuto lililonse. Mulungu wake Yehova ali naye,+Ndipo amamutamanda mofuula monga mfumu yawo. 22  Mulungu akuwatulutsa ku Iguputo.+ Kwa iwo, Iye ali ngati nyanga za ngʼombe yamʼtchire yamphongo.*+ 23  Palibe amene angalodze Yakobo,+Kapena kuombeza maula polimbana ndi Isiraeli.+ Panopa anthu anganene zokhudza Yakobo kapena kuti Isiraeli kuti: ‘Taonani zimene Mulungu wachita!’ 24  Uwu ndi mtundu wa anthu umene udzadzuka ngati mkango,Udzanyamuka ngati mkango.+ Sudzagona pansi mpaka utadya nyamaNdi kumwa magazi a nyama zophedwazo.” 25  Atatero Balaki anauza Balamu kuti: “Ngati simungathe kuwatemberera ngakhale pangʼono, ndiye musawadalitsenso.” 26  Balamu anayankha Balaki kuti: “Kodi sindinakuuzeni kuti, ‘Ndichita zonse zimene Yehova wanenaʼ?”+ 27  Balaki anauza Balamu kuti: “Chonde tabwerani. Tiyeni tipite kumalo enanso. Mwina kumeneko Mulungu woona angalole kuti mutemberere anthuwa.”+ 28  Choncho Balaki anatenga Balamu nʼkupita naye pamwamba pa phiri la Peori, limene linayangʼanizana ndi Yesimoni.*+ 29  Kenako Balamu anauza Balaki kuti: “Mumange maguwa ansembe 7 pamalo ano ndipo mundikonzere ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.”+ 30  Choncho Balaki anachita zimene Balamu ananena ndipo anapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anaika mawu mʼkamwa mwa Balamu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu amene Yehova waika mʼkamwa mwangamu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkumuika mawu awa mʼkamwa.”
Kapena kuti, “amene amadziimba mlandu.”
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.
Mabaibulo ena amati, “chipululu.”