Numeri 24:1-25
24 Balamu ataona kuti Yehova akufuna* kudalitsa Aisiraeli, sanapitenso kukafunafuna njira yoti awalodzere,+ mʼmalomwake anayangʼana kuchipululu.
2 Balamu atakweza maso ake nʼkuona Aisiraeli ali mʼmisasa mogwirizana ndi mafuko awo,+ mzimu wa Mulungu unafika pa iye.+
3 Kenako analankhula mwa ndakatulo kuti:+
“Mawu a Balamu mwana wa Beori,Mawu a mwamuna amene maso ake atseguka,
4 Mawu a munthu amene wamva mawu a Mulungu,Amene waona masomphenya a Wamphamvuyonse,Amene wagwada pansi, maso ake ali otsegula. Mawu ake akuti:+
5 Akongolerenji matenti ako, iwe Yakobo,Komanso malo ako okhala, iwe Isiraeli!+
6 Andanda kukafika kutali ngati zigwa,*+Ngati minda mʼmphepete mwa mtsinje.Ngati mitengo ya aloye imene Yehova anadzala,Ngati mikungudza mʼmbali mwa madzi.
7 Madzi odzaza mitsuko yake iwiri akutayikirabe pansi,Ndipo mbewu* yake yadzalidwa mʼmbali mwa madzi ambiri.+
Mfumu yakenso+ idzakhala yamphamvu kuposa Agagi,+Ndipo ufumu wake udzakwezedwa.+
8 Mulungu akumutulutsa mu Iguputo.Iye ali ngati nyanga za ngʼombe yamʼtchire yamphongo.
Adzawononga anthu a mitundu ina, amene akumupondereza,+Adzakungudza* mafupa awo, ndipo adzawaswa ndi mivi yake.
9 Iye wagwada pansi, wagona pansi ngati mkango,Ngati mkango, ndani angayese kumʼdzutsa?
Amene akudalitsa iwe adzadalitsidwa,Ndipo amene akukutemberera, adzatembereredwa.”+
10 Kenako Balaki anapsera mtima Balamu. Ndiyeno Balaki anawomba mʼmanja mokwiya nʼkuuza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere adani anga,+ koma iwe wawadalitsa kwambiri maulendo atatu onsewa.
11 Nyamuka pompano uzipita kwanu. Ine ndimafuna ndikupatse mphoto,+ koma taona! Yehova wakulepheretsa kulandira mphoto.”
12 Balamu anayankha Balaki kuti: “Kodi anthu amene munawatuma aja sindinawauze kuti,
13 ‘Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse chimene ndikufuna,* kaya chabwino kapena choipa, chosemphana ndi zimene Yehova walamula? Kodi sindinanene kuti ndikalankhula zokhazo zimene Yehova akandiuzeʼ?+
14 Tsopano ndikupita kwa anthu a mtundu wanga. Koma tabwerani kuti ndikuuzeni zimene anthuwa adzachite kwa anthu anu mʼtsogolo.”
15 Kenako analankhula mwa ndakatulo kuti:+
“Mawu a Balamu mwana wa Beori,Mawu a mwamuna amene maso ake ndi otsegula,+
16 Mawu a munthu amene wamva mawu a Mulungu,Amene akudziwa Wamʼmwambamwamba,Anaona masomphenya a Wamphamvuyonse,Atagwada pansi, maso ake ali otsegula. Mawu ake akuti:
17 Ndidzamuona, koma osati panopa;Ndidzamupenya, koma osati posachedwa.
Nyenyezi+ idzatuluka mwa Yakobo,Ndodo yachifumu+ idzatuluka mu Isiraeli.+
Ndipo iye adzaphwanyadi chipumi cha Mowabu+Ndi mitu ya asilikali onse ankhanza.
18 Edomu adzalandidwa,+Ndithu Seiri+ adzalandidwa ndi adani ake,+Pamene Isiraeli akuonetsa kulimba mtima kwake.
19 Wina adzatuluka mwa Yakobo kukagonjetsa,+Ndipo adzawononga aliyense amene wapulumuka mumzindamo.”
20 Balamu ataona Amaleki, anapitiriza mawu ake a ndakatulo kuti:
“Amaleki anali woyamba pa anthu a mitundu ina,*+Koma mapeto ake adzawonongedwa.”+
21 Ataona Akeni+ anapitiriza kulankhula mwa ndakatulo kuti:
“Mumakhala motetezeka, malo anu okhala ali pathanthwe.
22 Koma Kayini* adzawotchedwa ndi moto.
Kodi padzatenga nthawi yayitali bwanji Asuri asanakugwire nʼkupita nawe kudziko lina?”
23 Anapitiriza kulankhula mwa ndakatulo kuti:
“Mayo ine! Ndani adzapulumuke Mulungu akadzachita zimenezi?
24 Sitima zidzafika kuchokera kudoko la Kitimu,+Ndipo iwo adzazunza Asuri,+Adzazunza Ebere.
Koma iyenso adzawonongedwa kotheratu.”
25 Kenako Balamu+ ananyamuka nʼkubwerera kwawo. Nayenso Balaki anapita kwawo.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ataona kuti ndi zabwino mʼmaso mwa Yehova.”
^ Kapena kuti, “makhwawa.”
^ Kapena kuti, “mbadwa.”
^ “Kukungudza” ndi kuchotseratu mnofu wonse pafupa tikamadya nyama.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chochokera mumtima mwanga.”
^ Kutanthauza kuti anali oyamba kuukira Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo.
^ “Kayini” akuimira fuko la “Akeni.”