Numeri 25:1-18

  • Aisiraeli anachimwa ndi akazi a Chimowabu (1-5)

  • Pinihasi sanalekerere zoipa (6-18)

25  Pa nthawi imene Aisiraeli ankakhala ku Sitimu,+ anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+ 2  Akaziwo anaitana Aisiraeliwo kuti azikapereka nsembe kwa milungu yawo+ ndipo Aisiraeliwo anayamba kudya nsembezo komanso kugwadira milungu ya Amowabu.+ 3  Choncho Aisiraeli anayamba kulambira nawo Baala wa ku Peori,+ ndipo Yehova anakwiya kwambiri ndi Aisiraeliwo. 4  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Gwira onse amene akutsogolera anthuwo, ndipo uwaphe nʼkuwapachika pamtengo pamaso pa Yehova dzuwa likuswa mtengo. Uchite zimenezo kuti mkwiyo wa Yehova umene wayakira Aisiraeli uchoke.” 5  Choncho Mose anauza oweruza a mu Isiraeli kuti:+ “Aliyense wa inu aphe anthu ake amene akulambira nawo Baala wa ku Peori.”+ 6  Koma mwadzidzidzi anthuwo anangoona mwamuna wina wa Chiisiraeli akubwera ndi mkazi wa Chimidiyani.+ Anabwera naye kufupi ndi abale ake, pamaso pa Mose ndi gulu lonse la Aisiraeli. Pa nthawiyi nʼkuti Aisiraeliwo akulira pakhomo la chihema chokumanako. 7  Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, ataona zimenezi nthawi yomweyo ananyamuka pakati pa gululo nʼkutenga mkondo* mʼdzanja lake. 8  Iye anathamangira mwamuna wa Chiisiraeli uja mpaka kukalowa mutenti yake ndipo anabaya onse awiriwo ndi mkondowo. Anabaya mwamuna wa Chiisiraeli uja limodzi ndi mkaziyo, mpaka mkondowo unakadutsa kumaliseche kwa mkaziyo. Atatero mliriwo unaleka pakati pa Aisiraeli.+ 9  Amene anafa ndi mliriwo analipo 24,000.+ 10  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11  “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga pa Aisiraeli, chifukwa sanalekerere ngakhale pangʼono kuti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Choncho sindinawononge Aisiraeliwa, ngakhale kuti ndimafuna kuti anthu azikhala odzipereka kwa ine ndekha.+ 12  Pa chifukwa chimenechi, umuuze Pinihasi kuti, ‘Ndikupangana naye pangano la mtendere. 13  Limeneli likhala pangano la unsembe kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale,+ chifukwa sanalekerere zoti anthu azipikisana ndi Mulungu wake+ ndiponso anaphimba machimo a Aisiraeli.’” 14  Dzina la mwamuna wa Chiisiraeli, amene anaphedwa limodzi ndi mkazi wa Chimidiyani uja linali Zimiri mwana wa Salu, ndipo anali mtsogoleri wa nyumba ya makolo a fuko la Simiyoni. 15  Dzina la mkazi wa Chimidiyani amene anaphedwayo linali Kozibi, mwana wa Zuri.+ Zuri anali mtsogoleri wa fuko la nyumba ina ya makolo ku Midiyani.+ 16  Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: 17  “Akhaulitseni Amidiyani ndipo muwaphe,+ 18  chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwaphe ndithu, chifukwanso cha zochita za mchemwali wawo Kozibi, mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mkondo waungʼono.”