Numeri 26:1-65

  • Kalembera wachiwiri wa mafuko a Isiraeli (1-65)

26  Mliri uja utatha,+ Yehova anauza Mose ndi Eleazara mwana wa wansembe Aroni kuti:  “Muwerenge amuna onse oyenera kupita kunkhondo pakati pa gulu lonse la Aisiraeli. Muwerenge kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, potengera nyumba za makolo awo.”+  Choncho Mose ndi wansembe Eleazara+ analankhula ndi Aisiraeliwo mʼchipululu cha Mowabu,+ pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko kuti:+  “Muwerenge Aisiraeli onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.”+ Ana a Isiraeli amene anatuluka mʼdziko la Iguputo anali awa:  Rubeni+ anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli. Ana aamuna a Rubeni+ anali awa: Hanoki amene anali kholo la banja la Ahanoki, Palu amene anali kholo la banja la Apalu,  Hezironi amene anali kholo la banja la Ahezironi ndi Karami amene anali kholo la banja la Akarami.  Amenewa anali mabanja a anthu a fuko la Rubeni ndipo amuna onse amene anawerengedwa analipo 43,730.+  Mwana wamwamuna wa Palu anali Eliyabu.  Ana aamuna a Eliyabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Awiriwa, Datani ndi Abiramu, ndi amene anasankhidwa pa gululo ndipo anagwirizana ndi gulu la Kora+ pokangana ndi Mose+ komanso Aroni pamene ankatsutsana ndi Yehova.+ 10  Zitatero, nthaka inangʼambika* nʼkuwameza. Koma Kora anafa pamene moto unapsereza amuna 250.+ Ndipo iwo anakhala chitsanzo chotichenjeza.+ 11  Koma ana a Kora sanafe.+ 12  Ana aamuna a Simiyoni+ potengera mabanja awo anali awa: Nemueli amene anali kholo la banja la Anemueli, Yamini amene anali kholo la banja la Ayamini, Yakini amene anali kholo la banja la Ayakini, 13  Zera amene anali kholo la banja la Azera ndi Shauli amene anali kholo la banja la Ashauli. 14  Mabanja a anthu a fuko la Simiyoni anali amenewa. Amuna onse pamodzi analipo 22,200.+ 15  Ana aamuna a Gadi+ potengera mabanja awo anali awa: Zefoni amene anali kholo la banja la Azefoni, Hagi amene anali kholo la banja la Ahagi, Suni amene anali kholo la banja la Asuni, 16  Ozini amene anali kholo la banja la Aozini, Eri amene anali kholo la banja la Aeri, 17  Arodi amene anali kholo la banja la Aarodi ndi Areli amene anali kholo la banja la Aareli. 18  Amenewa anali mabanja a ana a Gadi. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 40,500.+ 19  Ana a Yuda+ anali Ere ndi Onani.+ Koma awiriwa anafera mʼdziko la Kanani.+ 20  Choncho ana aamuna a Yuda mwa mabanja awo anali awa: Shela+ amene anali kholo la banja la Ashela, Perezi+ amene anali kholo la banja la Aperezi ndi Zera+ amene anali kholo la banja la Azera. 21  Ana aamuna a Perezi anali Hezironi+ amene anali kholo la banja la Ahezironi ndi Hamuli+ amene anali kholo la banja la Ahamuli. 22  Amenewa anali mabanja a Yuda. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 76,500.+ 23  Ana aamuna a Isakara+ potengera mabanja awo anali awa: Tola+ amene anali kholo la banja la Atola, Puva amene anali kholo la banja la Apuna, 24  Yasubi amene anali kholo la banja la Ayasubi ndi Simironi amene anali kholo la banja la Asimironi. 25  Amenewa anali mabanja a Isakara. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 64,300.+ 26  Ana aamuna a Zebuloni+ anali awa: Seredi amene anali kholo la banja la Aseredi, Eloni amene anali kholo la banja la Aeloni ndi Yahaleeli amene anali kholo la banja la Ayahaleeli. 27  Amenewa anali mabanja a anthu a fuko la Zebuloni. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 60,500.+ 28  Ana aamuna a Yosefe+ potengera mabanja awo anali Manase ndi Efuraimu.+ 29  Ana aamuna a Manase+ anali Makiri+ amene anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anabereka Giliyadi. Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi.+ 30  Ana aamuna a Giliyadi anali awa: Yezeri amene anali kholo la banja la Ayezeri, Heleki amene anali kholo la banja la Aheleki, 31  Asiriyeli amene anali kholo la banja la Aasiriyeli, Sekemu amene anali kholo la banja la Asekemu, 32  Semida amene anali kholo la banja la Asemida ndi Heferi amene anali kholo la banja la Aheferi. 33  Koma Tselofekadi, mwana wamwamuna wa Heferi, analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha.+ Mayina a ana aakazi a Tselofekadi+ anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 34  Amenewa anali mabanja a Manase. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 52,700.+ 35  Ana aamuna a Efuraimu+ potengera mabanja awo anali awa: Sutela+ amene anali kholo la banja la Asutela, Bekeri amene anali kholo la banja la Abekeri ndi Tahani amene anali kholo la banja la Atahani. 36  Ana aamuna a Sutela anali Erani amene anali kholo la banja la Aerani. 37  Amenewa anali mabanja a ana a Efuraimu. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 32,500.+ Awa anali ana aamuna a Yosefe potengera mabanja awo. 38  Ana aamuna a Benjamini+ potengera mabanja awo anali awa: Bela+ amene anali kholo la banja la Abela, Asibeli amene anali kholo la banja la Aasibeli, Ahiramu amene anali kholo la banja la Aahiramu, 39  Sefufamu amene anali kholo la banja la Asefufamu ndi Hufamu amene anali kholo la banja la Ahufamu. 40  Ana aamuna a Bela anali Aridi ndi Namani.+ Aridi anali kholo la banja la Aaridi. Namani anali kholo la banja la Anamani. 41  Amenewa anali ana aamuna a Benjamini potengera mabanja awo. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 45,600.+ 42  Ana aamuna a Dani+ potengera mabanja awo anali ochokera kwa Suhamu amene anali kholo la banja la Asuhamu. Awa anali mabanja a Dani potengera fuko lawo. 43  Amuna onse amene anawerengedwa mʼmabanja a Asuhamu analipo 64,400.+ 44  Ana aamuna a Aseri+ potengera mabanja awo anali awa: Imuna amene anali kholo la banja la Aimuna, Isivi amene anali kholo la banja la Aisivi ndi Beriya amene anali kholo la banja la Aberiya. 45  Ana aamuna a Beriya anali Hiberi amene anali kholo la banja la Ahiberi ndi Malikieli amene anali kholo la banja la Amalikieli. 46  Mwana wamkazi wa Aseri anali Sera. 47  Amenewa anali mabanja a ana aamuna a Aseri. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 53,400.+ 48  Ana aamuna a Nafitali+ potengera mabanja awo anali awa: Yahazeeli amene anali kholo la banja la Ayahazeeli, Guni amene anali kholo la banja la Aguni, 49  Yezera amene anali kholo la banja la Ayezera ndi Silemu amene anali kholo la banja la Asilemu. 50  Amenewa anali mabanja a Nafitali potengera fuko lawo. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 45,400.+ 51  Amuna onse amene anawerengedwa pakati pa Aisiraeli ndi amenewa ndipo onse pamodzi analipo 601,730.+ 52  Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: 53  “Anthu amenewa uwagawire dzikoli kuti likhale cholowa chawo, potengera mndandanda wa mayinawo.*+ 54  Amene ali ndi anthu ambiri apatsidwe dziko lalikulu monga cholowa chake, ndipo amene ali ndi anthu ochepa apatsidwe dziko lalingʼono monga cholowa chake.+ Aliyense apatsidwe cholowacho mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu ake. 55  Koma dzikolo uligawe pochita maere.+ Onse alandire cholowa chawo potengera mayina a mafuko a makolo awo. 56  Muchite maere kuti mudziwe cholowa cha fuko lililonse, kaya lili ndi anthu ambiri kapena ochepa.” 57  Tsopano awa ndi mayina a amuna amene anawerengedwa pakati pa Alevi+ potengera mabanja awo: Agerisoni, a banja la Gerisoni, Akohati, a banja la Kohati+ ndi Amerari, a banja la Merari. 58  Mabanja a Alevi ndi awa: banja la Alibini,+ banja la Aheburoni,+ banja la Amali,+ banja la Amusi+ ndi banja la Akora.+ Kohati anabereka Amuramu.+ 59  Mkazi wa Amuramu anali Yokebedi,+ mwana wa Levi. Mkazi wa Levi anamuberekera mwana ameneyu ku Iguputo. Yokebedi anaberekera Amuramu ana awa: Aroni, Mose ndi mchemwali wawo Miriamu.+ 60  Kenako Aroni anabereka Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+ 61  Koma Nadabu ndi Abihu anafa chifukwa chopereka moto wosaloleka pamaso pa Yehova.+ 62  Onse amene anawerengedwa pakati pa Alevi analipo 23,000. Amenewa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita mʼtsogolo.+ Iwo sanawerengedwe limodzi ndi Aisiraeli,+ chifukwa sanafunikire kulandira cholowa pakati pa Aisiraeli.+ 63  Awa ndi anthu amene Mose ndi wansembe Eleazara anawawerenga pakati pa Aisiraeli. Anawawerengera mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko. 64  Koma pakati pa anthu amenewa, panalibe munthu aliyense amene anali mʼgulu la anthu omwe anawerengedwa mʼchipululu cha Sinai, nthawi imene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga Aisiraeli.+ 65  Zinakhala choncho chifukwa ponena za iwo, Yehova anati: “Ndithu anthu amenewa adzafera mʼchipululu.”+ Choncho, palibe amene anatsala kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “inatsegula pakamwa pake.”
Kapena kuti, “mogwirizana ndi chiwerengero cha mayina amene analembedwa.”