Numeri 27:1-23

  • Ana aakazi a Tselofekadi (1-11)

  • Yoswa anasankhidwa kuti alowe mʼmalo mwa Mose (12-23)

27  Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri ndipo Makiri anali mwana wa Manase. Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewa mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.  Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, wansembe Eleazara, atsogoleri+ komanso gulu lonse, pakhomo la chihema chokumanako nʼkunena kuti:  “Bambo athu anafera mʼchipululu. Koma iwo sanali mʼgulu la anthu amene ankatsatira Kora,+ omwe anasonkhana kuti atsutsane ndi Yehova. Bambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo, ndipo analibe mwana aliyense wamwamuna.  Kodi dzina la bambo athu lisapezekenso ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna? Chonde, tipatseni cholowa pakati pa azichimwene a bambo athu.”  Choncho Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:  “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo kuti akhale cholowa chawo pakati pa azichimwene a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.+  Ndipo uuze Aisiraeli kuti: ‘Ngati mwamuna wamwalira alibe mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi.  Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene ake. 10  Ngati alibe azichimwene, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene a bambo ake. 11  Ngati bambo ake alibe azichimwene awo, muzipereka cholowa chake kwa wachibale wake wapafupi wa ku banja lawo, ndipo azitenga cholowacho kuti chikhale chake. Chigamulo chimenechi chidzakhala lamulo kwa Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova walamula Mose.’” 12  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Kwera phiri ili la Abarimu,+ ukaone dziko limene ndidzalipereke kwa Aisiraeli.+ 13  Ukaliona dzikolo, iwenso udzaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako*+ komanso Aroni mchimwene wako,+ 14  chifukwa pamene gulu lija linakangana nane mʼchipululu cha Zini, inu munapandukira mawu anga ndipo munalephera kundilemekeza pamaso pa gululo pamadzi+ a Meriba+ ku Kadesi,+ mʼchipululu cha Zini.”+ 15  Kenako Mose anauza Yehova kuti: 16  “Inu Yehova, Mulungu amene mumapereka moyo kwa anthu onse,* sankhani munthu woti azitsogolera gululi. 17  Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse, kuti gulu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.” 18  Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu wolimba mtima,* ndipo uike dzanja lako pa iye.+ 19  Kenako umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara komanso pamaso pa gulu lonse, ndipo umuike kuti akhale mtsogoleri pamaso pawo.+ 20  Umupatseko mphamvu zako,*+ kuti gulu lonse la Aisiraeli lizimumvera.+ 21  Yoswayo aziimirira pamaso pa wansembe Eleazara, ndipo Eleazara azifunsira chigamulo cha Yehova mʼmalo mwa Yoswayo pogwiritsa ntchito maere a Urimu.+ Aliyense azitsatira zimene walamula* kaya ndi Yoswayo, Aisiraeli komanso gulu lonse.” 22  Choncho Mose anachitadi mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Anatenga Yoswa nʼkumuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara komanso pamaso pa gulu lonselo. 23  Kenako anaika manja ake pa iye nʼkumuika kukhala mtsogoleri+ mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa Mose.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzagona limodzi ndi makolo ako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu wa mizimu ya zamoyo zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene mwa iye muli mzimu.”
Kapena kuti, “ulemerero wako.”
Kapena kuti, “zimene Mulungu walamula,” mwina kudzera mwa Yoswa kapena Eleazara.