Numeri 29:1-40

  • Kaperekedwe ka nsembe zosiyanasiyana (1-40)

    • Tsiku loliza lipenga (1-6)

    • Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo (7-11)

    • Chikondwerero cha Misasa (12-38)

29  “‘Pa tsiku loyamba la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.+ Tsiku limeneli lizikhala tsiku loliza lipenga.+  Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa amphongo 7, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.  Muziperekanso ufa wosalala wothira mafuta monga nsembe zake zambewu. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pa ngʼombe yamphongoyo, magawo awiri mwa magawo 10 pa nkhosa yamphongoyo  ndi gawo limodzi mwa magawo 10 pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7 amenewo.  Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi yamphongo, monga nsembe yamachimo yophimbira machimo anu.  Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo mogwirizana ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zowotcha pamoto zakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.  Pa tsiku la 10 la mwezi wa 7 umenewu, muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu.* Musamagwire ntchito iliyonse.+  Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Nyama zonsezo zizikhala zopanda chilema.+  Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Popereka ngʼombe yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 10  Popereka aliyense mwa ana a nkhosa 7 amphongowo, muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 11  Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo. Muziipereka kuwonjezera pa nsembe yamachimo pa tsiku lophimba machimo,+ ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe zake zambewu ndiponso zachakumwa. 12  Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. Muzichita chikondwerero posonyeza kulemekeza Yehova masiku 7.+ 13  Pa tsiku limeneli muzipereka nsembe yopsereza+ yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe 13 zazingʼono zamphongo, nkhosa zamphongo ziwiri ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 14  Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Iliyonse ya ngʼombe 13 zamphongozo muziiperekera ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Iliyonse ya nkhosa zamphongo ziwirizo muziiperekera ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 15  Aliyense wa ana a nkhosa 14 amphongowo, muzimuperekera ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 16  Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 17  Pa tsiku lachiwiri, muzipereka ngʼombe 12 zazingʼono zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 18  Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 19  Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo. Muziipereka kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu, limodzi ndi nsembe zake zachakumwa.+ 20  Pa tsiku lachitatu, muzipereka ngʼombe 11 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 21  Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 22  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 23  Pa tsiku la 4, muzipereka ngʼombe 10 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 24  Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 25  Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 26  Pa tsiku la 5, muzipereka ngʼombe 9 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 27  Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 28  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 29  Pa tsiku la 6, muzipereka ngʼombe 8 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 30  Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 31  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 32  Pa tsiku la 7, muzipereka ngʼombe 7 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 33  Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse la nsembezi. 34  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 35  Pa tsiku la 8, muzichita msonkhano wapadera. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.+ 36  Pa tsikuli, muzipereka nsembe yopsereza yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 37  Popereka ngʼombe yamphongo, nkhosa yamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 38  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 39  Muzipereka zimenezi kwa Yehova pa zikondwerero zanu,+ kuwonjezera pa nsembe zimene mukupereka chifukwa cha lonjezo limene munapanga,+ nsembe zanu zaufulu+ zimene mumapereka kuti zikhale nsembe zanu zopsereza,+ nsembe zanu zambewu,+ nsembe zanu zachakumwa+ ndi nsembe zanu zamgwirizano.’”+ 40  Mose anauza Aisiraeli zonse zimene Yehova anamulamula.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zakafungo kokhazika mtima pansi.”
Ankasonyeza chisoni chimenechi posala kudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”