Numeri 3:1-51

  • Ana aamuna a Aroni (1-4)

  • Alevi anasankhidwa kuti azitumikira (5-39)

  • Kuwombola ana oyamba kubadwa (40-51)

3  Iyi ndi mbiri ya mbadwa za* Aroni ndi Mose pa nthawi imene Yehova analankhula ndi Mose mʼphiri la Sinai.+  Mayina a ana a Aroni anali awa: woyamba Nadabu kenako Abihu,+ Eleazara+ ndi Itamara.+  Ana a Aroni mayina awo anali amenewa. Iwo anali ansembe odzozedwa amene anaikidwa* kuti akhale ansembe.+  Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova atapereka moto wosaloledwa kwa Yehova+ mʼchipululu cha Sinai, ndipo iwo anafa opanda ana. Pomwe Eleazara+ ndi Itamara+ anapitiriza kutumikira monga ansembe limodzi ndi Aroni bambo awo.  Kenako Yehova anauza Mose kuti:  “Itanitsa fuko la Levi+ ndipo uwapereke kwa wansembe Aroni kuti azimutumikira.+  Iwo azikwaniritsa udindo wawo pomuthandiza komanso potumikira gulu lonse pa ntchito zapachihema chokumanako.  Azisamalira ziwiya zonse+ zapachihema chokumanako, komanso kukwaniritsa udindo wawo wotumikira Aisiraeli pogwira ntchito zapachihema.+  Upereke Alevi kwa Aroni ndi ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera kwa Aisiraeli.+ 10  Uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, ndipo azigwira ntchito zawo zaunsembe.+ Munthu wamba* aliyense amene wayandikira malowo, aziphedwa.”+ 11  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12  “Ine ndasankha Alevi pakati pa Aisiraeli mʼmalo mwa ana onse oyamba kubadwa* a Aisiraeli+ ndipo Aleviwo adzakhala anga. 13  Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo,+ ndinapatula mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli kuti akhale wanga, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.” 14  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai+ kuti: 15  “Uwerenge ana a Levi potengera nyumba ya makolo awo komanso mabanja awo. Uwerenge mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kupita mʼtsogolo.”+ 16  Choncho Mose anawerenga Aleviwo pomvera zimene Yehova anamulamula. 17  Mayina a ana a Levi anali awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ 18  Mayina a ana a Gerisoni, potengera mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simeyi.+ 19  Ana a Kohati, potengera mabanja awo, anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ 20  Ana a Merari, potengera mabanja awo, anali Mali+ ndi Musi.+ Mabanja a Alevi anali amenewa potengera nyumba za makolo awo. 21  Mabanja a Alibini+ ndi Asimeyi anachokera mwa Gerisoni. Amenewa ndi amene anali mabanja a Agerisoni. 22  Amuna onse amene anawerengedwa kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo anakwana 7,500.+ 23  Mabanja a Agerisoni ankamanga misasa yawo kumbuyo kwa chihema,+ mbali yakumadzulo. 24  Mtsogoleri wa nyumba ya Agerisoni anali Eliyasafu, mwana wa Layeli. 25  Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema+ ndi nsalu yoyala pachihemacho, nsalu yake yophimba,+ nsalu yotchinga pakhomo,+ 26  nsalu+ za mpanda wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe za chinsalu chake, komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi. 27  Mabanja a Aamuramu, Aizara, Aheburoni ndi Auziyeli anachokera mwa Kohati.+ Amenewa ndi amene anali mabanja a Akohati. 28  Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, analipo 8,600. Amenewa ntchito yawo inali kutumikira pamalo oyera.+ 29  Mabanja a ana a Kohati ankamanga msasa wawo kumʼmwera kwa chihema.+ 30  Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31  Ntchito yawo inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ziwiya+ zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼmalo oyerawo, nsalu yotchinga+ komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 32  Mkulu wa atsogoleri onse a Alevi anali Eleazara,+ mwana wa wansembe Aroni. Iye ndi amene ankayangʼanira anthu onse amene ankatumikira pamalo oyera. 33  Mabanja a Amali ndi Amusi anachokera mwa Merari. Amenewa ndi amene anali mabanja a Amerari.+ 34  Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo analipo 6,200.+ 35  Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Merari anali Zuriyeli, mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga msasa wawo kumpoto kwa chihema.+ 36  Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake, zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi zipilala, ziwiya zake zonse+ ndi ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 37  Ankasamaliranso zipilala za mpanda wozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo+ komanso zikhomo ndi zingwe zake. 38  Amene ankamanga msasa wawo kumʼmawa kwa chihema, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira mʼmalo opatulika, mʼmalo mwa Aisiraeli. Munthu wamba aliyense* amene wayandikira malowo, ankayenera kuphedwa.+ 39  Amuna onse afuko la Levi amene Mose ndi Aroni anawawerenga, pomvera lamulo la Yehova analipo 22,000. Anawerenga amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo potengera mabanja awo. 40  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uwerenge ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo+ ndipo ulembe mayina awo. 41  Unditengere Alevi kuti akhale anga mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli.+ Unditengerenso ziweto zonse za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zoyamba kubadwa za Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova.” 42  Mose anawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. 43  Ana onse aamuna oyamba kubadwa amene anawawerenga, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, anakwana 22,273. 44  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 45  “Utenge Alevi mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli. Utengenso ziweto za Alevi mʼmalo mwa ziweto za Aisiraeli. Aleviwo akuyenera kukhala anga. Ine ndine Yehova. 46  Monga dipo*+ la ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli okwana 273 omwe apitirira chiwerengero cha Alevi,+ 47  utenge masekeli* 5 pa munthu aliyense,+ mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera.* Sekeli imodzi ndi yokwana magera* 20.+ 48  Ndalamazo uzipereke kwa Aroni ndi ana ake. Zikhale dipo* lowombolera Aisiraeli amene apitirira chiwerengero cha Alevi.” 49  Choncho Mose analandira ndalama zowombolera Aisiraeli amene chiwerengero chawo chinaposa cha Alevi. 50  Kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, analandira ndalama zokwana masekeli 1,365, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera. 51  Ndiyeno Mose anapereka ndalama za dipozo kwa Aroni ndi ana ake pomvera mawu a Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mibadwo ya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene manja awo anadzazidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana onse oyamba kubadwa, otsegula mimba ya mayi awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo aliyense,” kutanthauza munthu amene si Mlevi.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
Gera imodzi inali yofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.