Numeri 30:1-16

  • Malumbiro a amuna (1, 2)

  • Malumbiro a akazi ndi ana aakazi (3-16)

30  Ndiyeno Mose analankhula ndi atsogoleri+ a mafuko a Isiraeli kuti: “Tamverani zimene Yehova walamula: 2  Munthu akalonjeza+ kwa Yehova kapena akachita lumbiro+ lodzimana, asalephere kukwaniritsa mawu ake.+ Azichita zonse zimene walonjezazo.+ 3  Mtsikana amene akukhala mʼnyumba ya bambo ake akalonjeza zinazake kwa Yehova, kapena akachita lumbiro lodzimana, 4  bambo ake nʼkumumva akulonjeza kapena akuchita lumbiro lodzimanalo, koma osamutsutsa, malonjezo ake onsewo akhale momwemo ndipo lumbiro lake lililonse lodzimana likhale momwemo. 5  Koma ngati bambo ake amukaniza atamva zimene walonjeza kapena lumbiro lake lodzimana, malonjezowo akhale opanda ntchito. Yehova adzamukhululukira chifukwa bambo ake anamukaniza.+ 6  Koma ngati mtsikanayo wakwatiwa atalumbira kale kapena atalonjeza mosaganiza bwino, 7  ndiyeno mwamuna wake nʼkumva koma osamuletsa pa tsiku limene wamva zimene analonjezazo, malonjezo ake kapena malumbiro akudzimana amene anachitawo azikhala momwemo. 8  Koma mwamuna wake akamukaniza pa tsiku limene wamva zimene analonjezazo, ndiye kuti wafafaniza lonjezo kapena lumbiro limene mkaziyo anachita mosaganiza bwino+ ndipo Yehova adzamukhululukira mkaziyo. 9  Koma mkazi wamasiye kapena amene banja lake linatha akachita lonjezo, lonjezo lililonse limene wachita lizikhala momwemo. 10  Komabe ngati mkazi walonjeza, kapena ngati wachita lumbiro lodzimana, akukhala mʼnyumba ya mwamuna wake, 11  mwamuna wake nʼkumva koma osamutsutsa kapena kumukaniza, malonjezo ake onse, kapena lumbiro lililonse lodzimana limene wachita lizikhala momwemo. 12  Koma mwamuna wake akafafaniza malonjezowo pa tsiku limene wamva zimene mkaziyo analonjeza kapena malumbiro ake odzimana amene anachita, malonjezowo azikhala opanda ntchito.+ Mwamuna wake wawafafaniza ndipo Yehova adzamukhululukira mkaziyo. 13  Pa nkhani yokhudza lonjezo lililonse kapena lumbiro lokhudza kudzimana kapenanso kulolera kuvutika, mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana kuti mkaziyo akwaniritse lonjezolo. 14  Koma ngati mwamunayo sanatsutse zimene mkazi wakeyo walonjeza, masiku nʼkumapita, ndiye kuti mwamunayo wavomereza malonjezo onse a mkaziyo kapena malumbiro onse odzimana amene mkaziyo anachita. Iye wavomereza chifukwa sanamukanize mkaziyo pa tsiku limene anamva akulonjeza. 15  Koma ngati mwamunayo wafafaniza malonjezowo patapita nthawi kuchokera pa tsiku limene anamva malonjezowo, mwamunayo ndi amene aziyankha mlandu mʼmalo mwa mkazi wakeyo.+ 16  Awa ndi malamulo amene Yehova anapatsa Mose okhudza mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso bambo ndi mwana wake wachitsikana amene akukhala mʼnyumba mwake.”

Mawu a M'munsi