Numeri 31:1-54

  • Kubwezera Amidiyani (1-12)

    • Balamu anaphedwa (8)

  • Malamulo okhudza zinthu zotengedwa kunkhondo (13-54)

31  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:  “Uwabwezere+ Amidiyani chifukwa cha zimene anachitira Aisiraeli.+ Pambuyo pake udzaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako.”*+  Choncho Mose analankhula ndi anthuwo kuti: “Konzekeretsani amuna pakati panu kuti apite kukamenyana* ndi Amidiyani, ndipo mukapereke chilango cha Yehova kwa Amidiyaniwo pobwezera zimene anachita.  Mutenge amuna 1,000 pa fuko lililonse la mafuko onse a Isiraeli kuti apite kunkhondo.”  Choncho kuchokera pa anthu masauzande a Aisiraeliwo,+ anatenga amuna 1,000 pa fuko lililonse. Amuna onse opita kunkhondo* anakwana 12,000.  Ndiyeno Mose anatumiza amunawo kunkhondo, amuna 1,000 pa fuko lililonse. Anawatumiza limodzi ndi Pinihasi,+ mwana wa wansembe Eleazara. Pinihasi ananyamula ziwiya zopatulika ndi malipenga operekera zizindikiro.+  Amunawo anakamenyana ndi Amidiyani, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose, ndipo anapha mwamuna aliyense.  Anthu amene anaphedwawo akuphatikizapo mafumu 5 a Chimidiyani. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Hura ndi Reba. Komanso anapha Balamu+ mwana wa Beori ndi lupanga.  Koma Aisiraeli anagwira akazi a Chimidiyani ndi ana awo nʼkuwatenga kupita nawo kwawo. Anatenganso ziweto zawo zonse ndi chuma chawo chonse. 10  Mizinda yawo yonse imene ankakhala komanso misasa yawo yonse* anaiwotcha ndi moto. 11  Anatenga zinthu zawo zonse, kuphatikizapo anthu ndi ziweto zomwe. 12  Kenako anatenga anthu amene anawagwirawo limodzi ndi zinthu zina zonse nʼkupita nawo kwa Mose, wansembe Eleazara ndi kugulu la Aisiraeli, kumsasa wawo umene unali mʼchipululu cha Mowabu,+ pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, ku Yeriko. 13  Atafika nawo kumeneko, Mose ndi wansembe Eleazara, limodzi ndi atsogoleri onse a anthuwo, anatuluka kukakumana nawo kunja kwa msasa. 14  Koma Mose anakwiya kwambiri ndi amuna amene ankatsogolera asilikaliwo, atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100, amene ankachokera kunkhondo. 15  Mose anawafunsa kuti: “Kodi akazi onse mwawasiya amoyo? 16  Pajatu akazi amenewa ndi amene anatsatira mawu a Balamu nʼkunyengerera Aisiraeli kuti achimwire Yehova+ pa zimene zinachitika ku Peori,+ moti mliri unagwera gulu la anthu a Yehova.+ 17  Tsopano iphani mwana wamwamuna aliyense pakati pa anawa, ndiponso muphe mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna. 18  Koma ana aakazi onse aangʼono amene sanagonepo ndi mwamuna musawaphe.+ 19  Mumange msasa kunja kwa msasawu, ndipo mukhalemo masiku 7. Aliyense amene wapha munthu komanso aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu wophedwa,+ adziyeretse+ pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku la 7. Mudziyeretse limodzinso ndi anthu amene mwawagwirawo. 20  Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chilichonse chopangidwa ndi ubweya wa mbuzi komanso chilichonse chopangidwa ndi mtengo.” 21  Tsopano wansembe Eleazara anauza asilikali amene anapita kunkhondo aja kuti: “Tamverani zimene Yehova analamula Mose, 22  ‘Zinthu zagolide, zasiliva, zakopa, zachitsulo, zatini ndi zamtovu, 23  chilichonse chimene sichingapse ndi moto, chidutse pamoto kuti chikhale choyera. Kenako muzichiyeretsanso ndi madzi.+ Koma chilichonse chimene chingapse ndi moto muzichiyeretsa ndi madzi. 24  Mudzachape zovala zanu pa tsiku la 7 kuti mudzakhale oyera, pambuyo pake mudzalowe mumsasa.’”+ 25  Kenako Yehova anauza Mose kuti: 26  “Iweyo ndi wansembe Eleazara ndi atsogoleri a gululo, muwerenge zinthu zonse zimene akatenga kunkhondo. Muwerenge anthu ndi ziweto zomwe. 27  Zinthuzo muzigawe pawiri. Hafu iperekedwe kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, ndipo hafu inayo iperekedwe kwa gulu lonse la anthuwo.+ 28  Pa zinthu zimene zaperekedwa kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 500 zilizonse, pa anthu, ngʼombe, abulu ndi nkhosa kuti zikhale msonkho woperekedwa kwa Yehova. 29  Zimenezi muzitenge pa hafu imene iwo alandire, ndipo muzipereke kwa wansembe Eleazara monga chopereka kwa Yehova.+ 30  Pa hafu imene Aisiraeli alandira, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa ndi pa ziweto zamtundu uliwonse. Muzipereke kwa Alevi,+ amene amagwira ntchito zokhudzana ndi utumiki wapachihema cha Yehova.”+ 31  Choncho Mose ndi wansembe Eleazara anachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 32  Pa zinthu zonse zimene anthu amene anapita kunkhondowo anabweretsa panali nkhosa 675,000, 33  ngʼombe 72,000 34  ndi abulu 61,000. 35  Akazi amene anali asanagonepo ndi mwamuna+ analipo 32,000. 36  Pa hafu imene inaperekedwa kwa amuna omwe anapita kunkhondo panali nkhosa 337,500. 37  Nkhosa zimene anazipereka kwa Yehova monga msonkho zinalipo 675. 38  Ngʼombe zinalipo 36,000, ndipo pa ngʼombe zimenezi, 72 anazipereka kwa Yehova monga msonkho. 39  Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anawapereka kwa Yehova monga msonkho. 40  Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anaperekedwa kwa Yehova monga msonkho. 41  Ndiyeno Mose anapereka msonkhowo kwa wansembe Eleazara+ ngati chopereka kwa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 42  Pa hafu imene Mose anapereka kwa Aisiraeli, ya zinthu zimene anthu anabweretsa kuchokera kunkhondo, 43  panali nkhosa zokwana 337,500, 44  ngʼombe 36,000, 45  abulu 30,500, 46  ndipo anthu analipo 16,000. 47  Ndiyeno pa hafu imene anapereka kwa Aisiraeliwo, Mose anatengapo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu ndi pa ziweto. Zinthu zimenezi anazipereka kwa Alevi+ amene ankatumikira pachihema cha Yehova,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 48  Kenako atsogoleri a masauzande a asilikali+ anafika kwa Mose. Iwowa anali atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100. 49  Iwo anauza Mose kuti: “Ife atumiki anu tawerenga amuna onse ankhondo amene tikuwayangʼanira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene akusowapo.+ 50  Choncho tiloleni kuti aliyense wa ife apereke zinthu zimene wabwera nazo monga chopereka kwa Yehova. Tabwera ndi zinthu zagolide, matcheni ovala mʼmiyendo, zibangili, mphete zachifumu, ndolo ndi zodzikongoletsera zina. Tipereka zimenezi kwa Yehova kuti ziphimbe machimo athu.” 51  Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira golideyo kwa iwo, kutanthauza zodzikongoletsera zonse zamtengo wapatali. 52  Golide yense amene anamupereka kwa Yehova anakwana masekeli* 16,750. Ameneyu ndi golide amene atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 komanso atsogoleri a magulu a asilikali 100 anapereka. 53  Aliyense wa amuna amene anapita kunkhondowo anabwerako ndi zinthu. 54  Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira zinthu zagolidezo kwa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100. Ndipo zinthu zagolidezo anakaziika mʼchihema chokumanako, kuti zikhale chikumbutso kwa Aisiraeli pamaso pa Yehova.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzagona limodzi ndi makolo ako.”
Kapena kuti, “kuti akhale mʼgulu la asilikali lokamenyana.”
Kapena kuti, “amene anali mʼgulu la asilikali.”
Kapena kuti, “misasa yawo yonse yokhala ndi mpanda.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.