Numeri 34:1-29

  • Malire a dziko la Kanani (1-15)

  • Amuna amene anawapatsa ntchito yogawa malo (16-29)

34  Yehova analankhulanso ndi Mose kuti:  “Upereke malangizo awa kwa Aisiraeli: ‘Awa ndi malire a dziko la Kanani, dziko limene ndidzakupatseni kuti likhale cholowa chanu.+  Malire a dziko lanu mbali yakumʼmwera adzayambire kuchipululu cha Zini, malire ndi Edomu. Malire anu akumʼmwera, mbali yakumʼmawa, adzayambire kumene Nyanja Yamchere* yathera.+  Malirewo adzakhota nʼkukadutsa kumʼmwera kwa chitunda cha Akirabimu+ kulowera ku Zini, nʼkukathera kumʼmwera kwa Kadesi-barinea.+ Kenako akakhotere ku Hazara-adara+ nʼkukafika ku Azimoni.  Ndiyeno kuchokera ku Azimoni, malirewo akalowere kuchigwa cha Iguputo* mpaka kukathera ku Nyanja Yaikulu.*+  Malire anu a mbali yakumadzulo akakhale gombe la Nyanja Yaikulu.* Amenewa akakhale malire anu a mbali yakumadzulo.+  Malire anu akumpoto akayende motere: Mukalembe malirewo kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kuphiri la Hora.+  Kuchokera kuphiri la Hora, mukalembe malirewo mpaka kukafika ku Lebo-hamati,*+ ndipo malirewo akathere ku Zedadi.+  Malirewo akafike ku Zifironi, mpaka kukathera ku Hazara-enani.+ Malire anu a mbali yakumpoto akakhale amenewa. 10  Ndiyeno mukalembe malire anu a kumʼmawa kuyambira ku Hazara-enani mpaka ku Sefamu. 11  Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kumʼmawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akadutse pamalo otsetsereka akumʼmawa kwa Nyanja ya Kinereti.*+ 12  Malirewo akatsike ndithu mpaka kumtsinje wa Yorodano, ndipo akathere ku Nyanja Yamchere.+ Limeneli ndi limene lidzakhale dziko lanu+ ndi malire ake olizungulira.’” 13  Choncho Mose anauza Aisiraeli kuti: “Limeneli ndi dziko limene ligawidwe kwa inu pogwiritsa ntchito maere kuti likhale cholowa chanu.+ Lidzagawidwa kwa inu mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kuti liperekedwe kwa mafuko 9 ndi hafu. 14  Fuko la Rubeni potengera mabanja a makolo awo, fuko la Gadi potengera mabanja a makolo awo komanso hafu ya fuko la Manase, analandira kale cholowa chawo.+ 15  Mafuko awiri ndi hafuwo analandira kale cholowa chawo kudera lakumʼmawa kwa Yorodano, moyangʼanizana ndi Yeriko.”+ 16  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17  “Amuna amene akakugawireni malo kuti akhale cholowa chanu, mayina awo ndi awa: Wansembe Eleazara+ ndi Yoswa+ mwana wa Nuni. 18  Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse kuti akathandize kugawa malowo kuti akhale cholowa chanu.+ 19  Amunawo mayina awo ndi awa: pa fuko la Yuda,+ Kalebe+ mwana wa Yefune, 20  pa fuko la ana a Simiyoni,+ Semuyeli mwana wa Amihudi, 21  pa fuko la Benjamini,+ Elidadi mwana wa Kisiloni, 22  pa fuko la ana a Dani,+ mtsogoleri Buki mwana wa Yogili, 23  pa ana a Yosefe+ ku fuko la ana a Manase,+ mtsogoleri Hanieli mwana wa Efodi, 24  pa fuko la ana a Efuraimu,+ mtsogoleri Kemueli mwana wa Sipitana, 25  pa fuko la ana a Zebuloni,+ mtsogoleri Elizafana mwana wa Paranaki, 26  pa fuko la ana a Isakara,+ mtsogoleri Palitiyeli mwana wa Azani, 27  pa fuko la ana a Aseri,+ mtsogoleri Ahihudi mwana wa Selomi, 28  ndipo pa fuko la ana a Nafitali,+ mtsogoleri Pedaheli mwana wa Amihudi.” 29  Amenewa ndi amuna amene Yehova anawalamula kuti akagawe malo kwa Aisiraeli mʼdziko la Kanani.+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
Kapena kuti, “kukhwawa la Iguputo.”
Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.
Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti, kapena kuti Nyanja ya Galileya.