Numeri 36:1-13

  • Lamulo lokhudza ukwati wa akazi amene akulandira cholowa (1-13)

36  Atsogoleri a mabanja omwe anachokera mwa Giliyadi mwana wa Makiri,+ mwana wa Manase, ochokera kumabanja a ana a Yosefe, anapita kukalankhula ndi Mose komanso akalonga omwe anali atsogoleri a Aisiraeli.  Iwo anati: “Paja Yehova anakulamulani inu mbuyathu, kuti mugawe dzikoli pochita maere+ kuti likhale cholowa cha Aisiraeli. Yehova anakulamulaninso kuti mupereke cholowa cha mchimwene wathu Tselofekadi kwa ana ake aakazi.+  Ngati ana aakaziwa atakwatiwa ndi amuna a mafuko ena a Aisiraeli, ndiye kuti cholowa chawo chidzachotsedwa ku cholowa cha makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense adzakwatiweko. Zikadzatero ndiye kuti cholowa chathu cha malo chidzachepa.  Ndiye chaka cha Ufulu+ cha Aisiraeli chikadzafika, cholowa cha akaziwa chidzachotsedwa ku cholowa cha fuko la makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense wa iwo adzakwatiweko ndipo chidzakhala cha fukolo mpaka kalekale.”  Ndiyeno Mose anauza Aisiraeli zimene Yehova anamuuza kuti: “Zimene fuko la ana a Yosefe likunena ndi zoona.  Zimene Yehova walamula zokhudza ana aakazi a Tselofekadi nʼzakuti: ‘Iwo angakwatiwe ndi aliyense amene angamukonde. Koma ayenera kukwatiwa ndi amuna a fuko la makolo awo okha.  Cholowa cha Aisiraeli chisamachotsedwe ku fuko lina kupita ku fuko lina. Aliyense wa Aisiraeli ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake.  Choncho, mwana wamkazi aliyense amene walandira nawo cholowa pakati pa mafuko a Aisiraeli, azikwatiwa ndi mwamuna wa mʼbanja la fuko la makolo ake,+ kuti aliyense wa Aisiraeli azisunga cholowa chochokera kwa makolo ake.  Cholowa chilichonse chisachotsedwe ku fuko lina kupita ku fuko lina. Fuko lililonse la Aisiraeli lizisunga cholowa chake.’” 10  Ana aakazi a Tselofekadi anachitadi zimene Yehova analamula Mose.+ 11  Choncho Mala, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, ana aakazi a Tselofekadi,+ anakwatiwa ndi ana a azichimwene a bambo awo. 12  Iwo anakwatiwa ndi amuna ochokera ku mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, kuti cholowa chawo chisachoke ku fuko la banja la bambo awo. 13  Amenewa ndi malamulo ndi zigamulo za Yehova, zimene anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose ku Yeriko, mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.+

Mawu a M'munsi