Numeri 4:1-49
4 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni kuti:
2 “Muwerenge ana onse a Kohati+ mwa ana a Levi, potengera mabanja awo komanso nyumba za makolo awo.
3 Muwerenge onse kuyambira azaka 30+ mpaka 50,+ amene ali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito mʼchihema chokumanako.+
4 Utumiki umene ana a Kohati azigwira mʼchihema chokumanako,+ womwe ndi utumiki wopatulika koposa, ndi uwu:
5 Mukamasamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azilowa mʼchihema nʼkuchotsa katani+ ndipo aziphimba likasa+ la Umboni ndi kataniyo.
6 Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu, nʼkuyalanso nsalu yabuluu pamwamba pake. Kenako azibwezeretsa mʼmalo ake ndodo zake zonyamulira.+
7 Iwo aziyalanso nsalu yabuluu patebulo la mkate wachionetsero,+ nʼkuikapo mbale, makapu, mbale zolowa ndi mitsuko ya nsembe yachakumwa.+ Mkate wachionetsero+ womwe ndi nsembe ya nthawi zonse uzikhalabe pomwepo.
8 Akatero, aziziphimba ndi nsalu yofiira kwambiri, ndiponso aziphimba tebulolo ndi zikopa za akatumbu. Kenako azibwezeretsa mʼmalo mwake ndodo zake zonyamulira.+
9 Ndiyeno azitenga nsalu yabuluu nʼkuphimbira choikapo nyale,+ pamodzi ndi nyale zake,+ zopanira+ zake zozimitsira nyale, zoikamo phulusa la zingwe za nyale ndi ziwiya zake zonse zosungiramo mafuta ogwiritsa ntchito nthawi zonse.
10 Choikapo nyalecho pamodzi ndi zipangizo zake zonse, azizikulunga mʼchikopa cha akatumbu nʼkuziika pandodo yonyamulira.
11 Kenako, aziphimba guwa lansembe lagolide+ ndi nsalu yabuluu. Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu, nʼkubwezeretsa mʼmalo mwake ndodo zake zonyamulira.+
12 Akatero, azitenga ziwiya zonse+ zimene amagwiritsa ntchito pa utumiki wawo nthawi zonse mʼmalo oyera, nʼkuzikuta ndi nsalu yabuluu. Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, nʼkuziika pandodo yonyamulira.
13 Azichotsa phulusa* paguwa lansembe+ nʼkuyalapo nsalu ya ubweya wa nkhosa wapepo.
14 Aziikapo ziwiya zonse zimene amagwiritsa ntchito akamatumikira paguwa lansembe. Aziikapo zoikamo phulusa la zingwe za nyale, mafoloko aakulu, mafosholo, mbale zolowa ndi ziwiya zonse zapaguwa lansembe.+ Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, nʼkubwezeretsa mʼmalo mwake ndodo zake zonyamulira.+
15 Pamene mukusamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azikhala atamaliza kuphimba zinthu za mʼmalo oyera+ ndi ziwiya zonse za mʼmalo oyerawo. Kenako ana a Kohati azibwera nʼkudzazinyamula+ koma iwo asamakhudze zinthu za mʼmalo oyerazo chifukwa akatero adzafa.+ Ana a Kohati ndi amene ali ndi udindo wonyamula zinthu zimenezi pachihema chokumanako.
16 Eleazara+ mwana wa wansembe Aroni ndi amene ali ndi udindo woyangʼanira mafuta a nyale,+ zofukiza zonunkhira,+ nsembe ya nthawi zonse yambewu ndi mafuta odzozera.+ Ali ndi udindo woyangʼanira chihema chonse ndi zinthu zonse za mmenemo, kuphatikizapo malo oyera ndi ziwiya zake.”
17 Yehova analankhulanso ndi Mose ndi Aroni kuti:
18 “Musalole kuti fuko la mabanja a Akohati+ liwonongeke pakati pa Alevi.
19 Koma uchite izi kuti iwo asaphedwe chifukwa choyandikira zinthu zopatulika koposa:+ Aroni ndi ana ake azilowa mʼchihemacho, ndipo munthu aliyense azimugawira ntchito ndi katundu woti anyamule.
20 Ana a Kohatiwo asadzalowe kuti akaone zinthu zopatulikazo ngakhale pangʼono pokha chifukwa akadzatero adzafa.”+
21 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti:
22 “Uwerenge ana onse a Gerisoni+ potengera nyumba za makolo awo komanso mabanja awo.
23 Muwerenge onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene ali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito mʼchihema chokumanako.
24 Anthu amʼmabanja a Agerisoni anapatsidwa ntchito yosamalira ndi kunyamula zinthu izi:+
25 Azinyamula nsalu za chihema kapena kuti chihema chokumanako,+ nsalu yophimba chihema, chophimba cha chikopa cha katumbu chomwe chili pamwamba pake+ ndi nsalu yotchinga pakhomo la chihema chokumanako.+
26 Azinyamulanso nsalu za mpanda wa bwalo,+ nsalu yotchinga khomo la mpanda+ umene wazungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe zolimbitsira mpandawo, ziwiya zake zonse ndi zinthu zina zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumikiwu. Ntchito imene azigwira ndi imeneyi.
27 Aroni ndi ana ake aziyangʼanira ntchito imene ana a Gerisoni+ akuchita komanso katundu amene akunyamula. Aziwauza ntchito zimene azigwira ndi katundu amene azinyamula.
28 Utumiki umene mabanja a ana a Gerisoni azichita mʼchihema chokumanako+ ndi umenewu. Itamara+ mwana wa wansembe Aroni, ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.
29 Ana a Merari+ nawonso uwawerenge potengera mabanja awo komanso nyumba za makolo awo.
30 Muwerenge onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene ali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito mʼchihema chokumanako.
31 Zinthu zimene azinyamula,+ mogwirizana ndi utumiki wawo pachihema chokumanako ndi izi: Mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake ndiponso zitsulo zokhazikapo zipilala ndi mafelemu.+
32 Azinyamulanso zipilala+ zozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo,+ zikhomo+ ndi zingwe zolimbitsira mpandawo limodzi ndi zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumiki umenewu. Munthu aliyense muzimupatsa katundu woti azinyamula.
33 Izi ndi zimene mabanja a ana a Merari+ azichita monga mbali ya utumiki wawo pachihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni,+ ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.”
34 Kenako Mose ndi Aroni pamodzi ndi atsogoleri+ a anthuwo, anawerenga ana a Kohati+ potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo.
35 Anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito pachihema chokumanako.+
36 Onse amene anawerengedwa, mogwirizana ndi mabanja awo, anakwana 2,750.+
37 Amenewa ndi anthu amene anawerengedwa kuchokera mʼmabanja a ana a Kohati, onse amene ankatumikira pachihema chokumanako. Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.+
38 Ana a Gerisoni+ anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo,
39 anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azitumikira pachihema chokumanako.
40 Onse amene anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo, anakwana 2,630.+
41 Amenewa ndi anthu amene anawerengedwa kuchokera mʼmabanja a ana a Gerisoni, onse amene ankatumikira pachihema chokumanako. Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera zimene Yehova analamula.+
42 Ana a Merari anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo,
43 anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito pachihema chokumanako.+
44 Onse amene anawerengedwa mogwirizana ndi mabanja awo anakwana 3,200.+
45 Amenewa ndi anthu amene anawerengedwa kuchokera mʼmabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.+
46 Mose ndi Aroni, limodzi ndi atsogoleri a Isiraeli, anawerenga Alevi onse potengera mabanja awo komanso nyumba za makolo awo.
47 Anawerenga kuyambira azaka 30 mpaka 50, ndipo onse anasankhidwa kuti azitumikira komanso kunyamula katundu wa pachihema chokumanako.+
48 Anthu onse amene anawerengedwa anakwana 8,580.+
49 Anthuwa anawerengedwa pomvera zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose, aliyense mogwirizana ndi utumiki wake komanso katundu amene ankanyamula. Anawerengedwa mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “phulusa la mafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.