Numeri 8:1-26

  • Aroni anayatsa nyale 7 (1-4)

  • Alevi anayeretsedwa nʼkuyamba kutumikira (5-22)

  • Zaka zimene Alevi ankayenera kuyamba komanso kusiya utumiki (23-26)

8  Yehova analankhula ndi Mose kuti:  “Lankhula ndi Aroni ndipo umuuze kuti, ‘Ukayatsa nyale, nyale zonse 7 ziziunikira malo apatsogolo pa choikapo nyalecho.’”+  Choncho Aroni anachita izi: Anayatsa nyalezo kuti ziunikire malo apatsogolo pa choikapo nyalecho,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.  Choikapo nyalecho anachipanga chonchi: Chinali chagolide komanso chosula+ kuchokera kutsinde lake mpaka kumaluwa ake. Choikapo nyalecho anachipanga mogwirizana ndi chitsanzo chimene Yehova anaonetsa Mose mʼmasomphenya.+  Yehova analankhulanso ndi Mose kuti:  “Utenge Alevi pakati pa Aisiraeli ndipo uwayeretse.+  Kuti uwayeretse uchite izi: Uwawaze madzi oyeretsera machimo ndipo iwo amete thupi lonse ndi lezala. Komanso achape zovala zawo nʼkudziyeretsa.+  Kenako iwo atenge ngʼombe yaingʼono yamphongo,+ pamodzi ndi nsembe yake yambewu+ ya ufa wosalala wothira mafuta. Iweyo utenge ngʼombe inanso yaingʼono yamphongo ya nsembe yamachimo.+  Ukatero, ubweretse Aleviwo kuchihema chokumanako ndipo usonkhanitse gulu lonse la Aisiraeli.+ 10  Ukamapereka Aleviwo pamaso pa Yehova, Aisiraeliwo aziika manja awo pa Aleviwo.+ 11  Ndiyeno Aroni azipereka Aleviwo kwa Yehova monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku+ yochokera kwa Aisiraeli ndipo iwo azigwira ntchito yotumikira Yehova.+ 12  Kenako Aleviwo aziika manja awo pamitu ya ngʼombe zamphongozo.+ Pambuyo pake, upereke kwa Yehova ngʼombe imodzi monga nsembe yamachimo, ndipo inayo uipereke monga nsembe yopsereza yophimbira machimo+ a Alevi. 13  Uimiritse Aleviwo pamaso pa Aroni ndi ana ake ndipo uwapereke kwa Yehova monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku. 14  Upatule Aleviwo pakati pa Aisiraeli ndipo adzakhala anga.+ 15  Pambuyo pake, Aleviwo azitumikira pachihema chokumanako. Uzichita zimenezi powayeretsa ndi kuwapereka monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku. 16  Amenewa ndi operekedwa. Aperekedwa kwa ine kuchokera pakati pa Aisiraeli. Ine ndikuwatenga kukhala anga mʼmalo mwa onse oyamba kubadwa* pakati pa Aisiraeli.+ 17  Mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli ndi wanga, kaya akhale wa munthu kapena wa nyama.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo, ndinawapatula kuti akhale anga.+ 18  Choncho ndikutenga Alevi kuti akhale anga mʼmalo mwa ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli. 19  Ndidzapereka Alevi kwa Aroni ndi ana ake monga operekedwa kuchokera mwa Aisiraeli. Aleviwo adzatumikira mʼmalo mwa Aisiraeli pachihema chokumanako,+ ndipo aziphimba machimo a Aisiraeli kuti mliri usagwe pakati pawo+ chifukwa Aisiraeliwo ayandikira malo oyera.” 20  Mose ndi Aroni ndi gulu lonse la Aisiraeli, anachita zimenezi kwa Aleviwo. Aisiraeliwo anachitira Aleviwo mogwirizana ndi zonse zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi. 21  Choncho Aleviwo anadziyeretsa nʼkuchapa zovala zawo.+ Pambuyo pake, Aroni anawapereka kwa Yehova monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku.+ Kenako Aroniyo anawaphimbira machimo awo kuti awayeretse.+ 22  Ndiyeno Aleviwo analowa mʼchihema chokumanako nʼkukayamba utumiki wawo pamaso pa Aroni ndi ana ake. Anthu anachitira Aleviwo mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi. 23  Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 24  “Lamulo ili ndi lokhudza Alevi: Kuyambira wazaka 25 kupita mʼtsogolo azilowa mʼgulu la Alevi amene akutumikira mʼchihema chokumanako. 25  Koma akakwanitsa zaka 50, azituluka mʼgululo ndipo asamatumikirenso. 26  Iye azingothandizira abale ake amene akugwira ntchito pachihema chokumanako, koma asamatumikire kuchihemako. Izi ndi zimene uzichita ndi Alevi mogwirizana ndi ntchito zawo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ana onse oyamba kubadwa, otsegula mimba ya mayi awo.”