Numeri 9:1-23
9 Mʼmwezi woyamba wa chaka chachiwiri, Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo, Yehova analankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai.+ Iye anati:
2 “Aisiraeli akonze nsembe ya Pasika+ pa nthawi yake imene inaikidwiratu.+
3 Pa tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo kuli kachisisira,* mudzakonze nsembeyo pa nthawi yake yoikidwiratu. Mudzaikonze motsatira malamulo ake onse ndiponso njira zonse za kakonzedwe kake.”+
4 Choncho Mose anauza Aisiraeli kuti akonze nsembe ya Pasika.
5 Iwo anakonza nsembe ya Pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, madzulo kuli kachisisira,* mʼchipululu cha Sinai. Aisiraeliwo anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
6 Tsopano panali amuna ena amene anadzidetsa chifukwa chokhudza mtembo wamunthu,+ moti sanathe kukonza nsembe ya Pasika pa tsikulo. Choncho amunawo anakaonekera kwa Mose ndi Aroni pa tsikulo,+
7 nʼkunena kuti: “Ife ndife odetsedwa chifukwa takhudza munthu wakufa. Ngakhale kuti zili choncho, kodi tikuyeneradi kuletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pakati pa Aisiraeli pa nthawi imene inaikidwiratu?”+
8 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Dikirani pomwepo, ndimve zimene Yehova angalamule zokhudza inu.”+
9 Kenako Yehova anauza Mose kuti:
10 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu aliyense pakati panu kapena pakati pa mbadwa zanu, amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo,+ kapena amene ali pa ulendo wautali, azikonzabe nsembe ya Pasika yopereka kwa Yehova.
11 Azikonza nsembeyo mʼmwezi wachiwiri+ pa tsiku la 14, madzulo kuli kachisisira.* Azidya nyama ya nsembeyo pamodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa, ndiponso masamba owawa.+
12 Asamasiye nyama iliyonse mpaka mʼmamawa,+ ndipo asamaphwanye fupa lake lililonse.+ Aziikonza motsatira malamulo onse a Pasika.
13 Koma ngati munthu si wodetsedwa kapena sanali pa ulendo, ndipo wanyalanyaza kukonza nsembe ya Pasika, munthuyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake,+ chifukwa sanapereke nsembeyo kwa Yehova pa nthawi imene inaikidwiratu. Munthuyo adzafa chifukwa cha tchimo lake.
14 Ngati pali mlendo amene akukhala pakati panu, iyenso azikonza nsembe ya Pasika yoti apereke kwa Yehova.+ Aziikonza motsatira malamulo onse a Pasika ndiponso kakonzedwe kake ka nthawi zonse.+ Pakhale malamulo ofanana kwa nonsenu, kaya ndi mlendo kapena mbadwa.’”+
15 Pa tsiku limene anamanga chihema,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho. Koma kuyambira madzulo mpaka mʼmamawa, moto unkaoneka pamwamba pa chihemacho.+
16 Zimenezi ndi zomwe zinkachitika nthawi zonse. Mtambo unkaima pamwamba pa chihemacho masana ndipo usiku pankaoneka moto.+
17 Mtambowo ukanyamuka pamwamba pa chihemacho, Aisiraeli ankanyamuka nthawi yomweyo.+ Ndipo pamalo pamene mtambowo waima, mʼpamene Aisiraeli ankamangapo msasa.+
18 Choncho Yehova akalamula, Aisiraeli ankanyamuka, ndipo Yehova akalamula, ankamanga msasa.+ Masiku onse amene mtambo unkakhala pamwamba pa chihemacho, iwo ankakhalabe pamsasapo.
19 Ngakhale mtambowo utakhala masiku ambiri pamwamba pa chihema, Aisiraeli ankamverabe Yehova, ndipo sankachoka pamalopo.+
20 Nthawi zina mtambowo unkangokhala masiku owerengeka pamwamba pa chihemapo. Yehova akalamula, iwo ankakhalabe pamsasapo ndipo Yehova akalamula, iwo ankachokapo.
21 Nthawi zina mtambowo unkangokhalapo kuchokera madzulo mpaka mʼmamawa, ndipo mtambowo ukachoka mʼmamawawo, anthuwo ankanyamuka. Kaya mtambowo uchoke masana kapena usiku, iwo ankanyamuka.+
22 Kaya mtambowo ukhale pamwamba pa chihemacho masiku awiri, mwezi, kapena masiku ambiri, Aisiraeli ankakhalabe pamsasa osachoka. Koma mtambowo ukanyamuka, iwo ankachoka.
23 Yehova akalamula, iwo ankamanga msasa, ndipo Yehova akalamula, iwo ankanyamuka. Ankamvera Yehova potsatira malangizo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose.