Nyimbo ya Solomo 1:1-17

  • Nyimbo yoposa nyimbo zonse (1)

  • Mtsikana (2-7)

  • Ana aakazi a ku Yerusalemu (8)

  • Mfumu (9-11)

    • “Ife tikupangira zokongoletsa zagolide” (11)

  • Mtsikana (12-14)

    • ‘Wachikondi wanga ali ngati kathumba konunkhira ka mule’ (13)

  • Mʼbusa (15)

    • “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga”

  • Mtsikana (16, 17)

    • “Iwenso ndiwe wooneka bwino, wachikondi wanga” (16)

1  Nyimbo yoposa nyimbo zonse, nyimbo ya Solomo:+   “Undikise ndi milomo yako,Chifukwa chikondi chimene umandisonyeza chimaposa vinyo.+   Kununkhira kwa mafuta ako ndi kosangalatsa.+ Dzina lako lili ngati mafuta onunkhira amene athiridwa pamutu.+ Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda.   Nditenge, tiye tithawe. Chifukwatu mfumu yandipititsa mʼzipinda zake zamkati. Tiye tikondwere komanso kusangalalira limodzi. Tiye titamande* chikondi chimene umandisonyeza kuposa kutamanda vinyo. Mpake kuti atsikana amakukonda.   Inu ana aakazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda koma wokongola,Ngati matenti a ku Kedara+ komanso nsalu za matenti+ a Solomo.   Musandiyangʼanitsitse chifukwa chakuti ndada,Ndi dzuwatu landidetsali. Ana aamuna a mayi anga anandikwiyira.Choncho anandiika kuti ndiziyangʼanira minda ya mpesaMoti sindinathe kusamalira munda wanga wa mpesa.   Tandiuze, iwe amene ndimakukonda kwambiri,Ndiuze kumene umakadyetsera ziweto zako,+Kumene umakagonetsa ziweto masana. Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu kumutu*Pakati pa magulu a ziweto za anzako?”   “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,Tsatira mapazi a ziwetoNdipo ukadyetse mbuzi zako zingʼonozingʼono pafupi ndi matenti a abusa.”   “Iwe wokondedwa wanga, kwa ine uli ngati hatchi yaikazi yapamagaleta a Farao.+ 10  Masaya ako amaoneka bwino ukavala zodzikongoletsera,*Ndipo khosi lako limaoneka bwino ukavala mikanda. 11  Ife tikupangira zokongoletsa* zagolideZokhala ndi mikanda yasiliva.” 12  “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira,Mafuta anga onunkhira*+ akutulutsa kafungo kosangalatsa. 13  Wachikondi wanga ali ngati kathumba konunkhira ka mule* kwa ine.+Iye amakhala pakati pa mabere anga usiku wonse. 14  Kwa ine, wachikondi wanga ali ngati maluwa a hena+Mʼminda ya mpesa ya ku Eni-gedi.”+ 15  “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga. Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+ 16  “Iwenso ndiwe wooneka bwino,* wachikondi wanga komanso ndiwe wosangalatsa.+ Bedi lathu ndi lamasamba ofewa. 17  Nyumba yathu* inamangidwa ndi mitengo ya mkungudza,Ndipo kudenga kwake kuli mitengo ya junipa.”*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Tiye tikambirane za.”
Kapena kuti, “nsalu yovala kumutu polira maliro.”
Mabaibulo ena amati, “Masaya ako ndi okongola ndi nkhata zatsitsi.”
Kapena kuti, “zovala kumutu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nado wanga.”
Kapena kuti, “ndiwe wokongola.”
Kapena kuti, “Nyumba yathu yabwino kwambiri.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.