Nyimbo ya Solomo 2:1-17
2 “Ine ndine duwa wamba lamʼchigwa chamʼmphepete mwa nyanja,Ndine duwa chabe lamʼchigwa.”+
2 “Mofanana ndi duwa limene lili pakati pa minga,Ndi mmene alili wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.”
3 “Mofanana ndi mtengo wa maapozi pakati pa mitengo yamʼnkhalango,Ndi mmene alili wachikondi wanga pakati pa ana aamuna.
Ndikulakalaka kwambiri nditakhala pansi pamthunzi wa wokondedwa wanga.Ndipo chipatso chake ndi chotsekemera.
4 Iye anandipititsa kunyumba ya phwando,*Ndipo chikondi chake kwa ine chinali ngati mbendera yozikidwa pambali panga.
5 Ndipatseni mphesa zouma zoumba pamodzi+ kuti zinditsitsimule.Ndipatseni maapozi kuti ndipeze mphamvu,Chifukwa chikondi chikundidwalitsa.
6 Dzanja lake lamanzere lili pansi pa mutu wanga,Ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.+
7 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu,Pali insa+ ndiponso pali mphoyo zakutchire kuti:
Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.+
8 Ndikumva wachikondi wanga akubwera.
Taonani! Uyo akubwera apoyo,Akukwera mapiri ndipo akudumpha zitunda.
9 Wachikondi wanga ali ngati insa komanso mphoyo yaingʼono.+
Taonani! Iye waima kuseri kwa khoma la nyumba yathu.Akuyangʼana mʼmawindo,Akusuzumira pazotchingira mʼmawindo.
10 Wachikondi wanga wandiuza kuti:
‘Nyamuka wokondedwa wanga,Ndiwe wokongola kwa ine, tiye tizipita.
11 Taona! Nyengo yamvula yadutsa.
Mvula yatha ndipo yapita.
12 Maluwa ayamba kuoneka mʼdziko,+Nthawi yodulira mpesa yakwana,+Ndipo mʼdziko lathu mukumveka kuimba kwa njiwa.+
13 Nkhuyu zoyambirira+ zapsa mumtengo wa mkuyu.Mpesa wachita maluwa ndipo ukununkhira.
Nyamuka bwera kuno,
Wokondedwa wanga wokongola, tiye tizipita.
14 Iwe njiwa yanga, amene uli mʼmalo obisika apathanthwe,+Amene uli mʼmingʼalu yamʼmalo otsetsereka,Ndikufuna ndikuone komanso kumva mawu ako,+Chifukwa mawu ako ndi osangalatsa ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+
15 “Tigwirireni nkhandwe,Nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa,Chifukwa minda yathu ya mpesa yachita maluwa.”
16 “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.+
Iye akudyetsa ziweto msipu+ umene uli pakati pa maluwa.+
17 Mpaka kunja kutayamba kuwomba kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka,Bwerera mwamsanga iwe wachikondi wanga,Kwera mapiri amene akutilekanitsa,* ngati insa+ komanso ngati mphoyo yaingʼono.”+