Nyimbo ya Solomo 3:1-11

  • Mtsikana (1-5)

    • ‘Usiku ndinaganizira za munthu amene ndimamukonda’ (1)

  • Ana aakazi a Ziyoni (6-11)

    • Gulu la anthu limene linkayenda ndi Solomo

3  “Ndili pabedi panga usiku,Ndinaganizira za munthu amene ndimamukonda.+ Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.+   Choncho ndinati: ‘Ndidzuka nʼkukazungulira mumzinda,Mʼmisewu ndi mʼmabwalo amumzinda,Kuti ndikafunefune munthu amene ndimamukonda.’ Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.   Alonda amene ankazungulira mumzindawo anandipeza.+ Ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi mwamuonako munthu amene ndimamukonda?’   Nditangowapitirira pangʼono,ndinamʼpeza munthu amene ndimamukonda. Ndinamugwira ndipo sindinafune kumʼsiyaMpaka nditamubweretsa mʼnyumba ya mayi anga,+Mʼchipinda chamkati cha mayi amene anali ndi pakati kuti ine ndibadwe.   Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu,Pali insa ndiponso pali mphoyo zakutchire kuti: Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.”+   “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi nʼchiyani, chooneka ngati utsi wokwera mʼmwamba,Chonunkhira mafuta a mule ndi lubani,*Komanso ndi zonunkhira zonse za ufa za munthu wamalonda?”+   “Taonani! Ndi bedi la Solomo. Lazunguliridwa ndi amuna 60 amphamvu,Ochokera mwa amuna amphamvu a mu Isiraeli,+   Onsewo atenga malupanga,Ndipo onse ndi ophunzitsidwa nkhondo,Aliyense wamangirira lupanga lake mʼchiunoKuti adziteteze ku zinthu zoopsa za usiku.”   “Ndi bedi* lachifumu la Mfumu SolomoLimene anapanga yekha ndi mitengo ya ku Lebanoni.+ 10  Zipilala zake ndi zasiliva,Motsamira mwake ndi mwagolide. Chokhalira chake ndi chopangidwa ndi ubweya wa nkhosa wapepo.Mkati mwake, ana aakazi a ku YerusalemuAnakongoletsamo posonyeza chikondi.” 11  “Tulukani, inu ana aakazi a Ziyoni,Pitani mukaone Mfumu SolomoItavala nkhata yamaluwa, imene mayi ake+ anailukiraKuti ivale pa tsiku la ukwati wake,Pa tsiku limene mtima wa mfumuyo unasangalala.”

Mawu a M'munsi

Limeneli linali bedi lochita kunyamula limene ankanyamulirapo munthu wolemekezeka.