Nyimbo ya Solomo 6:1-13

  • Ana aakazi a ku Yerusalemu (1)

  • Mtsikana (2, 3)

    • “Wachikondi wanga, ine ndi wake ndipo iye ndi wanga” (3)

  • Mfumu (4-10)

    • “Ndiwe wokongola ngati Tiriza” (4)

    • Mawu a akazi (10)

  • Mtsikana (11, 12)

  • Mfumu (ndi anthu ena) (13a)

  • Mtsikana (13b)

  • Mfumu (ndi anthu ena) (13c)

6  “Kodi wachikondi wako wapita kuti,Iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse? Kodi wachikondi wako wadzera njira iti? Tiye tikuthandize kumufunafuna.”   “Wachikondi wanga wapita kumunda wake,Kumabedi amʼmunda a mbewu zonunkhira,Kuti akadyetse ziweto kuminda,Ndiponso kuti akathyole maluwa.+   Wachikondi wanga, ine ndi wakeNdipo iye ndi wanga.+ Iye akudyetsera ziweto msipu umene uli pakati pa maluwa.”+   “Wokondedwa wangawe,+ ndiwe wokongola ngati Tiriza,*+Ndiwe wooneka bwino ngati Yerusalemu,+Ndipo ndiwe wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera.+   Yangʼana kumbali kuti maso ako+ asandiyangʼanitsitse,Chifukwa akundichititsa mantha. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuziZimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+   Mano ako ali ngati gulu la nkhosaZimene zikuchokera kosambitsidwa,Zonse zabereka mapasa,Ndipo palibe imene ana ake afa.   Masaya ako munsalu yako yophimba kumutuyoAli ngati khangaza* logamphula pakati.   Ngakhale patakhala mafumukazi 60Komanso adzakazi* 80Ndi atsikana osawerengeka,+   Koma mmodzi yekha ndi amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema. Iye ndi mwana wapadera kwambiri kwa mayi ake. Ndi mwana amene amakondedwa ndi* mayi amene anamubereka. Ana aakazi akamuona, amamunena kuti ndi wosangalala.Mafumukazi ndi adzakazi amamutamanda. 10  ‘Kodi mkazi amene akuwala* ngati mʼbandakuchayu ndi ndani,Amene ndi wokongola ngati mwezi wathunthu,Wosadetsedwa ngati kuwala kwa dzuwa,Wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera?’”+ 11  “Ine ndinapita kumunda wa mitengo ya zipatso zokhala ndi mtedza,+Kuti ndikaone ngati yaphuka masamba atsopano mʼchigwa,*Kuti ndikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,Ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa. 12  Mosazindikira,Chifukwa cholakalaka kuona zinthu zimenezi, ndinakafikaKumene kunali magaleta a anthu olemekezeka* a mtundu wanga.” 13  “Bwerera, bwerera iwe Msulami! Bwerera, bwereraKuti tione kukongola kwako!” “Nʼchifukwa chiyani mukuyangʼanitsitsa Msulami?”+ “Iye ali ngati gule wa magulu awiri a anthu.”*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mzinda Wosangalatsa.”
“Khangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi mwana woyera kwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akuyangʼana pansi.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa.”
Kapena kuti, “odzipereka.”
Kapena kuti, “gule wa Mahanaimu.”