Nyimbo ya Solomo 8:1-14

  • Mtsikana (1-4)

    • “Ndikulakalaka ukanakhala mchimwene wanga” (1)

  • Azichimwene ake a mtsikana (5a)

    • ‘Kodi ndi ndani amene wakoleka dzanja mʼkhosi mwa wachikondi wake?’

  • Mtsikana (5b-7)

    • “Mofanana ndi Manda, chikondi sichigonja” (6)

  • Azichimwene ake a mtsikana (8, 9)

    • “Akakhala khoma, . . . koma akakhala chitseko, . . .” (9)

  • Mtsikana (10-12)

    • “Ine ndine khoma” (10)

  • Mʼbusa (13)

    • ‘Ndikufuna ndimve mawu akoʼ

  • Mtsikana (14)

    • “Thamanga ngati insa”

8  “Ndikulakalaka ukanakhala mchimwene wanga,Amene anayamwa mabere a mayi anga. Ndikanakupeza panja, ndikanakukisa,+Ndipo palibe amene akanandinyoza.   Bwenzi nditakutsogolera.Ndikanakulowetsa mʼnyumba mwa mayi anga,+Amene ankandiphunzitsa. Ndikanakupatsa vinyo wothira zonunkhiritsa kuti umwe,Komanso madzi a zipatso za makangaza zongofinya kumene.   Dzanja lake lamanzere likanakhala pansi pa mutu wanga,Ndipo dzanja lake lamanja likanandikumbatira.+   Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu kuti: Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.”+   “Kodi ndi ndani amene akuchokera kuchipululuyu,Atakoleka dzanja lake mʼkhosi mwa wachikondi wake?” “Ine ndinakudzutsa pansi pa mtengo wa maapozi. Pamenepo mʼpamene mayi ako anamva zowawa pokubereka. Mayi amene anakubereka anamva zowawa ali pamenepo.   Undiike pamtima pako ngati chidindo,Ndiponso undiike ngati chidindo padzanja lako,Chifukwa mofanana ndi Manda,* chikondi sichigonja,+Ndipo chimafuna kudzipereka ndi mtima wonse. Chikondi chimenechi chili ngati malawi a moto. Chikondicho ndi lawi la Ya.*+   Madzi osefukira sangazimitse chikondi,+Ndipo mitsinje singachikokolole.+ Ngati munthu atapereka chuma chonse chamʼnyumba mwake kusinthanitsa ndi chikondi,Anthu anganyoze zinthuzo.”*   “Tili ndi mchemwali wathu wamngʼono+Ndipo alibe mabere. Kodi tidzamuchitire chiyani mchemwali wathuyuPa tsiku limene adzafunsiridwe ukwati?”   “Akakhala khoma,Timʼmangira kampanda kasiliva pamwamba pake,Koma akakhala chitseko,Timʼkhomerera ndi thabwa la mkungudza.” 10  “Ine ndine khoma,Ndipo mabere anga ali ngati nsanja. Choncho mʼmaso mwa wokondedwa wanga ndakhalaNgati mkazi amene wapeza mtendere. 11  Solomo anali ndi munda wa mpesa+ ku Baala-hamoni. Munda wa mpesawo anaupereka kwa anthu oti aziusamalira. Ndipo munthu aliyense ankabweretsa ndalama zasiliva zokwana 1,000 zolipirira zipatso za mundawo. 12  Ndili ndi munda wanga wa mpesa umene ndingathe kuchita nawo chilichonse chimene ndikufuna. Ndalama 1,000 zasilivazo ndi zanu inu a Solomo,Ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za anthu amene amasamalira zipatso za mundawo.” 13  “Iwe amene umakhala mʼminda,+Anzanga akufuna amve mawu ako. Inenso ndikufuna ndimve mawu ako.”+ 14  “Fulumira wachikondi wanga,Thamanga ngati insa+Kapena ngati mphoyo yaingʼonoPamapiri amaluwa onunkhira.”

Mawu a M'munsi

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “munthuyo.”