Obadiya 1:1-21
1 Awa ndi masomphenya a Obadiya:*
Zimene Yehova Ambuye Wamkulu Koposa akunena zokhudza Edomu+ ndi izi:
“Ife tamva uthenga wochokera kwa Yehova,Ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu amitundu ina kukanena kuti:
‘Konzekani! Tiyeni tikamenyane naye.’”+
2 “Taona! Ndakuchititsa kukhala wosafunika pakati pa mitundu ina,Ndipo ikukuona kuti ndiwe wonyozeka kwambiri.+
3 Mtima wako wodzikuza wakupusitsa,+Iwe amene ukukhala mʼmalo obisika amʼthanthwe,Uli pamwamba pa phiri nʼkumanena mumtima mwako kuti,‘Ndani angandigwetsere pansi?’
4 Ngakhale utamakhala mʼmwamba* ngati chiwombankhanga,Kapena utamanga chisa chako pakati pa nyenyezi,Ine ndidzakugwetsapo pamenepo,” akutero Yehova.
5 “Akuba atabwera kwa iwe, kapena mbava zitabwera usiku,Kodi sangabe zokhazo zimene akufuna?
(Koma ndiye udzawonongedwatu!)*
Kapena okolola mphesa atabwera kwa iwe,Kodi sangasiyeko zina zoti munthu nʼkukunkha?+
6 Koma Esau ndiye wafufuzidwatu!
Anthu asakasaka chuma chake chonse chobisika nʼkuchitenga.
7 Anthu amene unachita nawo mgwirizano* akuthamangitsira kumalire.
Onsewo akupusitsa.
Anthu amene unkakhala nawo mwamtendere akugonjetsa.
Anthu amene ukudya nawo limodzi adzakutchera ukonde,Koma iwe sudzazindikira.”
8 Yehova akuti: “Kodi pa tsiku limenelo,Sindidzawononga anthu anzeru mu Edomu,+Komanso anthu ozindikira mʼdera lamapiri la Esau?
9 Iwe Temani,+ asilikali ako adzachita mantha,+Chifukwa aliyense mʼdera lamapiri la Esau adzaphedwa.+
10 Popeza unachitira nkhanza mʼbale wako Yakobo,+Udzachititsidwa manyazi kwambiri.+Udzaphedwa ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.+
11 Pa tsiku limene unangoima nʼkumaonerera,Pa tsiku limene adani* anagwira gulu la asilikali a mʼbale wako nʼkupita nawo ku ukapolo,+Ndiponso pamene anthu akudziko lina analowa mumzinda* wake nʼkuchita maere+ pa Yerusalemu,Iwe unali ngati mmodzi wa adaniwo.
12 Iwe sumayenera kunyadira pa tsiku limene mʼbale wako anakumana ndi tsoka,+Sumayenera kusangalala pa tsiku limene anthu a ku Yuda ankawonongedwa,+Sumayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene ankazunzika.
13 Iwe sumayenera kulowa mumzinda* wa anthu anga pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+Sumayenera kunyadira pamene mʼbale wako ankavutika pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.Ndipo sumayeneranso kutenga chuma chake pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+
14 Iwe sumayenera kuima panjira kuti uzipha anthu ake amene akuthawa.+Sumayeneranso kugwira anthu ake amene apulumuka nʼkuwapereka kwa adani awo pa tsiku limene ankazunzika.+
15 Tsiku la Yehova limene adzalange mitundu yonse ya anthu lili pafupi.+
Zimene wachitira mʼbale wako, iwenso adzakuchitira zomwezo.+
Zimene unachitira anthu ena zidzakubwerera pamutu pako.
16 Mmene wamwera vinyo paphiri langa loyera,Ndi mmenenso mitundu ina yonse ya anthu izidzamwera mkwiyo wanga nthawi zonse.+
Iwo adzamwa ndi kugugudiza mkwiyo wanga,Ndipo zidzakhala ngati sanakhalepo nʼkomwe.
17 Anthu onse opulumuka adzakhala paphiri la Ziyoni+Ndipo phiri limeneli lidzakhala loyera.+Anthu a mʼbanja la Yakobo adzatenganso zinthu zimene zinali zawo.+
18 A mʼbanja la Yakobo adzakhala ngati moto,A mʼbanja la Yosefe adzakhala ngati malawi a moto,Ndipo a mʼbanja la Esau adzakhala ngati mapesi.Moto wawo udzayatsa ndi kunyeketsa mapesiwo,Ndipo palibe aliyense wa mʼbanja la Esau amene adzapulumuke,+Chifukwa Yehova ndi amene wanena.
19 Iwo adzatenga dera la Negebu ndi dera lamapiri la Esau,+Komanso dera la Sefela ndi dera la Afilisiti.+
Adzatenganso madera a Efuraimu ndi Samariya,+Ndipo Benjamini adzatenga dera la Giliyadi.
20 Anthu amene anatengedwa pamalo okwera omenyerapo nkhondowa nʼkupita nawo kudziko lina,+Amene ndi Aisiraeli, adzatenga dziko la Akanani mpaka kukafika ku Zarefati.+
Anthu amene anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu, amene anali ku Sefaradi, adzatenga mizinda ya Negebu.+
21 Opulumutsa adzakwera paphiri la ZiyoniKuti aweruze dera lamapiri la Esau,+Ndipo Yehova adzakhala Mfumu.”+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza “Mtumiki wa Yehova.”
^ Mabaibulo ena amati, “utaulukira mʼmwamba.”
^ Mabaibulo ena amati, “Kodi angawononge zambiri bwanji?”
^ Kapena kuti, “pangano.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu achilendo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pageti.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pageti.”