Oweruza 10:1-18

  • Oweruza Tola ndi Yaeli (1-5)

  • Aisiraeli anasiya Mulungu kenako nʼkulapa (6-16)

  • Aamoni anaopseza Aisiraeli (17, 18)

10  Abimeleki atafa, panabwera Tola, mwana wa Puwa amene anali mwana wa Dodo wa fuko la Isakara ndipo anapulumutsa Isiraeli.+ Iye ankakhala ku Samiri mʼdera lamapiri la Efuraimu.  Tola anaweruza Isiraeli zaka 23. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa ku Samiri.  Tola atamwalira, panabwera Yairi wa ku Giliyadi ndipo anaweruza Isiraeli zaka 22.  Iye anali ndi ana 30 aamuna amene ankayenda pa abulu 30, ndipo iwo anali ndi mizinda 30. Mpaka lero mizinda imeneyi imadziwikabe kuti Havoti-yairi+ ndipo ili ku Giliyadi.  Kenako Yairi anamwalira ndipo anaikidwa ku Kamoni.  Aisiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ mafano a Asitoreti, milungu ya ku Aramu,* milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya Aamoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Iwo anasiya Yehova ndipo sankamutumikira.  Zitatero, Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli moti anawapereka* kwa Afilisiti ndi kwa Aamoni.+  Choncho, anthu amenewa anazunza ndi kupondereza kwambiri Aisiraeli chaka chimenecho. Kwa zaka 18, anapondereza Aisiraeli onse amene anali kumʼmawa kwa Yorodano, mʼdziko la Aamori limene linali ku Giliyadi.  Aamoni ankawolokanso Yorodano kukamenyana ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndi la Efuraimu, moti Aisiraeli ankavutika kwambiri. 10  Zitatero Aisiraeli anapempha Yehova kuti awathandize.+ Iwo anati: “Takuchimwirani inu Mulungu wathu, chifukwa tinakusiyani nʼkuyamba kutumikira Abaala.”+ 11  Koma Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Kodi sindinakupulumutseni pamene Aiguputo,+ Aamori,+ Aamoni, Afilisiti,+ 12  Asidoni, Aamaleki ndi Amidiyani ankakuponderezani? Inu mutandilirira ndinakupulumutsani mʼmanja mwawo. 13  Koma munandisiya nʼkuyamba kutumikira milungu ina.+ Nʼchifukwa chake sindikupulumutsaninso.+ 14  Pitani, mukapemphe thandizo kwa milungu imene mwasankhayo.+ Milungu imeneyoyo ikupulumutseni pa nthawi imene mukuvutikayi.”+ 15  Koma Aisiraeli anauza Yehova kuti: “Tachimwa. Inuyo mutichite chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino. Koma panopa chonde tipulumutseni.” 16  Atatero, iwo anachotsa milungu yonse yachilendo imene anali nayo ndipo anayamba kutumikira Yehova,+ moti iye sanalole kuti Aisiraeli apitirize kuvutika.+ 17  Patapita nthawi, Aamoni+ anasonkhana nʼkumanga msasa wawo ku Giliyadi. Zitatero, Aisiraeli nawonso anasonkhana nʼkumanga msasa wawo ku Mizipa. 18  Ndiyeno anthu ndi akalonga a Giliyadi anayamba kufunsana kuti: “Ndani atitsogolere kukamenyana ndi Aamoni?+ Ameneyo akhale mtsogoleri wa anthu onse okhala mʼGiliyadi.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Siriya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anawagulitsa.”