Oweruza 11:1-40

  • Woweruza Yefita anathamangitsidwa kenako anakhala mtsogoleri (1-11)

  • Yefita anakambirana ndi Aamoni (12-28)

  • Lonjezo la Yefita komanso mwana wake wamkazi (29-40)

    • Mwana wa Yefita sanakwatiwe (38-40)

11  Tsopano Yefita+ wa ku Giliyadi anali msilikali wamphamvu. Mayi ake anali hule, ndipo bambo ake anali Giliyadi.  Koma mkazi wa Giliyadi anamuberekeranso ana aamuna. Anawo atakula, anathamangitsa Yefita nʼkumuuza kuti: “Iwe sudzalandira cholowa mʼnyumba ya bambo athu, chifukwa ndiwe mwana wa mayi wina.”  Choncho Yefita anathawa azichimwene akewo ndipo anakakhala ku Tobu. Kumeneko anthu osowa zochita anagwirizana ndi Yefita ndipo ankapita naye limodzi kukaukira adani awo.  Patapita nthawi, Aamoni anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+  Aamoni atayamba kumenyana ndi Aisiraeli, nthawi yomweyo akulu a ku Giliyadi anapita kukatenga Yefita ku Tobu.  Iwo anauza Yefita kuti: “Tiye ukakhale mtsogoleri wa gulu lathu lankhondo ndipo tikamenyane ndi Aamoni.”  Koma Yefita anauza akulu a ku Giliyadiwo kuti: “Kodi si inu amene munkadana nane kwambiri mpaka kundithamangitsa mʼnyumba ya bambo anga?+ Ndiye lero mwandifuna chifukwa choti mwakumana ndi mavuto?”  Akulu a ku Giliyadi anayankha Yefita kuti: “Zoona, nʼchifukwa chake tabwera kwa iwe. Ngati ungapite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ukhala mtsogoleri wathu ku Giliyadi konse.”+  Ndiyeno Yefita anauza akulu a ku Giliyadiwo kuti: “Ngati mukunditenga kuti tikamenyane ndi Aamoni, ndipo Yehova nʼkukandithandiza kuwagonjetsa, ndidzakhaladi mtsogoleri wanu.” 10  Akulu a ku Giliyadi anayankha Yefita kuti: “Yehova akhale mboni* ngati sitidzachita mogwirizana ndi zimene wanenazi.” 11  Choncho Yefita anapita ndi akulu a ku Giliyadi, ndipo anthu anamuika kukhala mtsogoleri wawo komanso mkulu wa asilikali. Ndiyeno Yefita anabwerezanso kunena mawu ake onse aja pamaso pa Yehova ku Mizipa.+ 12  Kenako Yefita anatumiza uthenga kwa mfumu ya Aamoni+ wakuti: “Ndakuyambani chiyani kuti mubwere kwathu kuno kudzamenyana nane?” 13  Ndiyeno mfumu ya Aamoni inauza anthu amene Yefita anawatumawo kuti: “Nʼchifukwa chakuti Aisiraeli analanda dziko langa atachoka ku Iguputo.+ Analanda dzikoli kuyambira ku Arinoni+ kukafika ku Yaboki mpaka kukafikanso ku Yorodano.+ Ndiye mubweze dzikoli mwamtendere.” 14  Koma Yefita anatumizanso anthu kwa mfumu ya Aamoni 15  kukanena kuti: “Yefita wanena kuti: ‘Aisiraeli sanatenge dziko la Mowabu+ ndi dziko la Aamoni+ 16  chifukwa atachoka ku Iguputo anadutsa mʼchipululu kukafika ku Nyanja Yofiira+ mpaka ku Kadesi.+ 17  Kenako anatumiza uthenga kwa mfumu ya Edomu+ wakuti: “Tiloleni tidutse nawo mʼdziko lanu,” koma mfumu ya Edomu inakana. Anatumizanso uthenga kwa mfumu ya Mowabu,+ koma nayonso sinalole. Choncho Aisiraeli anapitiriza kukhala ku Kadesi.+ 18  Pamene ankadutsa mʼchipululu, analambalala dziko la Edomu+ ndi la Mowabu. Anadutsa chakumʼmawa kwa dziko la Mowabu+ nʼkukamanga misasa mʼchigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu chifukwa Arinoni ndi amene anali malire a Mowabu.+ 19  Kenako Aisiraeli anatumiza uthenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ya ku Hesiboni, kuti: “Tingadutse nawo mʼdziko lanu kupita kumalo athu?”+ 20  Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa mʼdziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkumanga misasa ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+ 21  Zitatero, Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka Sihoni ndi anthu ake onse mʼmanja mwa Aisiraeli. Choncho anawagonjetsa nʼkutenga dziko lonse la Aamori okhala kumeneko.+ 22  Anatenga chigawo cha Aamori kuchokera ku Arinoni kukafika ku Yaboki ndiponso kuchokera kuchipululu kukafika ku Yorodano.+ 23  Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi amene anagonjetsa Aamori+ pamaso pa anthu ake Aisiraeli, ndiye iwe ukufuna kuwathamangitsa? 24  Kodi chilichonse chimene mulungu wako Kemosi+ wakupatsa, si chimene umakhala nacho? Choncho aliyense amene Yehova Mulungu wathu wamuthamangitsa pamaso pathu ndi amenenso ife timamuthamangitsa.+ 25  Ndiye iweyo wasiyana pati ndi Balaki+ mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu? Kodi iye anakwanitsa kulimbana ndi Aisiraeli, kapena anayesa nʼkomwe kumenyana nawo? 26  Pamene Aisiraeli ankakhala ku Hesiboni ndi mʼmidzi yake yozungulira,+ ku Aroweli ndi mʼmidzi yake yozungulira ndi mʼmizinda yonse yamʼmbali mwa nyanja ku Arinoni kwa zaka 300, nʼchifukwa chiyani simunawalande mizindayo pa nthawi imeneyo?+ 27  Inetu sindinakuchimwire, koma iwe ukulakwa chifukwa ukundiyamba. Yehova amene ndi Woweruza,+ aweruze lero pakati pa Aisiraeli ndi Aamoni.’” 28  Koma mfumu ya Aamoni siinamvere uthenga umene Yefita anatumiza. 29  Mzimu wa Yehova unapatsa mphamvu Yefita+ ndipo anadutsa mʼdera la Giliyadi ndi la Manase nʼkukafika mʼdera la Mizipe wa ku Giliyadi.+ Atafika mʼdera la Mizipe wa ku Giliyadi anapitirira mpaka kukafika kwa Aamoni. 30  Ndiyeno Yefita analonjeza+ Yehova kuti: “Mukapereka Aamoni mʼmanja mwanga, 31  aliyense amene adzatuluka mʼnyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere kuchokera kwa Aamoni, ndidzamʼpereka kwa inu Yehova+ kuti akhale nsembe yopsereza.”+ 32  Zitatero Yefita anapita kukamenyana ndi Aamoni ndipo Yehova anawapereka mʼmanja mwake. 33  Iye anapha Aamoni ambirimbiri mʼmizinda 20, kuyambira ku Aroweli mpaka ku Miniti ndipo anakafikanso ku Abele-kerami. Choncho Aisiraeli anagonjetsa Aamoni. 34  Kenako Yefita anabwerera kwawo ku Mizipa+ ndipo akufika anangoona mwana wake wamkazi akubwera kudzamʼchingamira, akuimba maseche komanso akuvina. Iye anali mwana yekhayo amene anali naye. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35  Atangomuona, anangʼamba zovala zake nʼkunena kuti: “Mayine mwana wanga! Ndikumva chisoni kwambiri chifukwa ndikukuchotsa pakhomo. Ndalonjeza kwa Yehova ndipo sindingathe kubweza mawu anga.”+ 36  Koma iye anati: “Bambo, ngati mwalonjeza kwa Yehova, ndichitireni mogwirizana ndi zimene mwanenazo,+ chifukwa Yehova wakumenyerani nkhondo pobwezera adani anu, Aamoni.” 37  Kenako anauzanso bambo akewo kuti: “Ndikungopempha kuti mundilole ndichoke kwa miyezi iwiri, ineyo ndi atsikana anzanga, ndipite kumapiri kukalirira unamwali wanga.”* 38  Yefita anamuyankha kuti: “Pita!” Choncho anamulola kuti achoke kwa miyezi iwiri. Iye ndi anzakewo anapita kumapiri kukalirira unamwali wake. 39  Ndiyeno miyezi iwiri itatha anabwerera kwa bambo ake ndipo bambo akewo anakwaniritsa lonjezo lawo lokhudza iyeyo.+ Mtsikanayo sanagonepo ndi mwamuna. Tsopano zimene zinkachitika mu Isiraeli ndi zakuti, 40  chaka chilichonse atsikana a mu Isiraeli ankapita kukayamikira mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo 4 pa chaka.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amamva.”
Kapena kuti, “ndikalire ndi anzanga chifukwa sindidzakwatiwa.”