Oweruza 13:1-25

  • Mngelo anapita kwa Manowa ndi mkazi wake (1-23)

  • Kubadwa kwa Samisoni (24, 25)

13  Aisiraeli anayambiranso kuchita zoipa pamaso pa Yehova+ ndipo Yehova anawapereka mʼmanja mwa Afilisiti+ kwa zaka 40.  Pa nthawiyi panali mwamuna wina wa ku Zora+ wa fuko la Dani,+ dzina lake Manowa.+ Mkazi wake anali wosabereka, moti analibe mwana.+  Ndiyeno tsiku lina, mngelo wa Yehova anaonekera kwa mkaziyo nʼkumuuza kuti: “Tamvera, ndiwe wosabereka ndipo ulibe mwana. Koma udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna.+  Choncho uonetsetse kuti usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa+ ndipo usadye chilichonse chodetsedwa.+  Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Mʼmutu mwake musadzadutse lezala+ chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri* wa Mulungu kuchokera tsiku limene adzabadwe.* Iye adzatsogolera populumutsa Isiraeli mʼmanja mwa Afilisiti.”+  Kenako mkaziyo anapita kukauza mwamuna wake kuti: “Munthu wa Mulungu woona anabwera kwa ine, ndipo amaoneka ngati mngelo wa Mulungu woona, amaoneka mochititsa mantha kwambiri. Koma sindinamʼfunse kumene wachokera ndiponso sanandiuze dzina lake.+  Koma iye wandiuza kuti, ‘Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Ndiye usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo usadye chilichonse chodetsedwa, chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri wa Mulungu kuchokera tsiku limene adzabadwe* mpaka tsiku limene adzafe.’”  Manowa anachonderera Yehova kuti: “Yehova, tikupempha kuti munthu wa Mulungu woona amene munamutuma uja, abwerenso kuti adzatilangize zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”  Mulungu woona anamva zimene Manowa anapempha, moti mngelo wa Mulungu woona uja anabweranso kwa mkaziyo, ndipo anamʼpeza atakhala pansi panja. Pa nthawiyi sanali limodzi ndi mwamuna wake Manowa. 10  Nthawi yomweyo, mkaziyo anathamanga nʼkukauza mwamuna wake kuti: “Munthu amene anabwera kwa ine tsiku lijali, wabweranso.”+ 11  Atatero, Manowa ananyamuka nʼkupitira limodzi ndi mkazi wakeyo kwa munthuyo ndipo anamʼfunsa kuti: “Kodi ndinu amene munalankhula ndi mkazi wangayu?” Iye anayankha kuti: “Inde ndi ineyo.” 12  Ndiyeno Manowa anati: “Mawu anu akwaniritsidwe. Koma kodi mwanayo adzakhala wotani, nanga ntchito yake idzakhala yotani?”+ 13  Mngelo wa Yehova anauza Manowa kuti: “Mkazi wakoyu apewe kuchita zonse zimene ndamuletsa.+ 14  Asadye chilichonse chochokera ku mphesa, asamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa+ komanso asadye chilichonse chodetsedwa.+ Atsatire zonse zimene ndamuuza.” 15  Tsopano Manowa anauza mngelo wa Yehova kuti: “Dikirani pangʼono tikukonzereni kamwana ka mbuzi.”+ 16  Koma mngelo wa Yehova anauza Manowa kuti: “Ngakhale nditati ndidikire sikuti ndidya chakudya chanu. Koma ngati mungakonde kupereka kwa Yehova nsembe yopsereza, perekani.” Manowa sanadziwe kuti anali mngelo wa Yehova. 17  Ndiyeno Manowa anafunsa mngelo wa Yehova kuti: “Dzina lanu ndi ndani?+ Tikufuna tidzakulemekezeni zimene mwanena zikadzachitika.” 18  Koma mngelo wa Yehovayo anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukufunsa dzina langa? Dzina langa ndi lodabwitsatu.” 19  Kenako Manowa anatenga kamwana ka mbuzi ndi nsembe yambewu nʼkuzipereka nsembe kwa Yehova pathanthwe. Pamene ankachita zimenezi, Mulungu ankachita zodabwitsa Manowa ndi mkazi wake akuona. 20  Pamene malawi a moto ankakwera mʼmwamba kuchokera paguwa lansembelo, mngelo wa Yehova nayenso anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo, Manowa ndi mkazi wake akuona. Nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi. 21  Zitatero Manowa anadziwa kuti anali mngelo wa Yehova.+ Mngelo wa Yehovayo sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. 22  Ndiyeno Manowa anauza mkazi wake kuti: “Ife tifa basi, chifukwa taona Mulungu.”+ 23  Koma mkazi wakeyo anati: “Yehova akanakhala kuti akufuna kutipha, sakanalandira nsembe yathu yopsereza+ ndiponso nsembe yathu yambewu. Komanso sakanationetsa ndiponso kutiuza zinthu zonsezi.” 24  Patapita nthawi, mkaziyo anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina lakuti Samisoni.+ Pamene mnyamatayo ankakula, Yehova anapitiriza kumudalitsa. 25  Kenako mzimu wa Yehova unayamba kumupatsa mphamvu+ ku Mahane-dani+ pakati pa Zora ndi Esitaoli.+

Mawu a M'munsi

MʼChiheberi na·zir′, kutanthauza “Wosankhidwa; Wodzipereka; Wopatulidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmimba.”