Oweruza 15:1-20

  • Samisoni anabwezera Afilisiti (1-20)

15  Kenako, pa nthawi yokolola tirigu, Samisoni anapita kukaona mkazi wake uja ndipo anatenga kamwana ka mbuzi. Atafika anati: “Ndikufuna ndilowe kuchipinda kwa mkazi wanga.” Koma bambo a mkaziyo anamukaniza kulowa.  Iwo anati: “Ine ndinkaganiza kuti unadana naye,+ choncho ndinamʼpereka kwa mmodzi wa anyamata amene ankakhala nawe aja.+ Mngʼono wakeyu ndi wokongola kuposa iyeyu. Bwanji utenge ameneyu mʼmalomwake?”  Koma Samisoni anati: “Ulendo uno sindikhala ndi mlandu ndi Afilisiti ndikawachitira zoipa.”  Choncho Samisoni ananyamuka nʼkukagwira nkhandwe 300. Kenako anatenga nkhandwezo ziwiriziwiri nʼkuzimanga michira. Atatero, anaika muuni umodzi pakati pa michira iwiriyo.  Kenako anayatsa miyuniyo ndi moto, nʼkukusira nkhandwezo mʼminda ya Afilisti ya mbewu zosakolola. Choncho anayatsa chilichonse, kuyambira mitolo ya mbewu, mbewu zosakolola, minda ya mpesa komanso minda ya maolivi.  Zitatero, Afilisiti anafunsa kuti: “Wachita zimenezi ndi ndani?” Ndiyeno anauzidwa kuti: “Ndi Samisoni, mkamwini wa munthu wa ku Timuna uja, chifukwa munthuyu anatenga mkazi wa Samisoni nʼkumupereka kwa mmodzi mwa anyamata amene ankakhala ndi Samisoni ngati anzake a mkwati.”+ Afilisiti atamva zimenezi anapita kukatentha ndi moto mtsikanayo pamodzi ndi bambo ake.+  Koma Samisoni anawauza kuti: “Ngati khalidwe lanu ndi limeneli, ndiye sindikusiyani mpaka ndibwezere.”+  Ndiyeno anayamba kuwapha mmodzimmodzi. Kenako anapita nʼkumakakhala kuphanga la thanthwe la Etami.  Patapita nthawi, Afilisiti anabwera nʼkumanga msasa ku Yuda ndipo ankayendayenda ku Lehi.+ 10  Ndiyeno anthu a ku Yuda anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzatiukira?” Iwo anayankha kuti: “Tabwera kudzagwira* Samisoni kuti timʼchite zimene iye watichitira.” 11  Zitatero, amuna 3,000 a ku Yuda anapita kuphanga la thanthwe la Etami nʼkuuza Samisoni kuti: “Kodi iwe, sukudziwa kuti Afilisiti ndi amene akutilamulira?+ Ndiye nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi?” Iye anawayankha kuti: “Ndawachita zimene iwo anandichitira.” 12  Koma iwo anamuuza kuti: “Tabwera kudzakugwira* kuti tikakupereke kwa Afilisiti.” Samisoni anayankha kuti: “Lumbirani kuti inuyo simundichitira chilichonse choipa.” 13  Iwo anamuyankha kuti: “Ayi, sitikupha. Tingokumanga nʼkukakupereka kwa iwowo.” Choncho anamʼmanga ndi zingwe ziwiri zatsopano nʼkumʼtulutsa kuphangako. 14  Atafika naye ku Lehi, Afilisiti nʼkumuona, anafuula chifukwa chosangalala. Ndiyeno mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu,+ ndipo zingwe zimene anamʼmanga nazo manja zija zinadukaduka ngati ulusi wowauka ndi moto nʼkugwa pansi.+ 15  Zitatero, anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo ndipo analitenga nʼkupha nalo amuna 1,000.+ 16  Kenako Samisoni anati: “Ndi fupa la nsagwada za bulu, milumilu! Ndi fupa la nsagwada za bulu, ndapha anthu 1,000.”+ 17  Atamaliza kulankhula zimenezi, anataya fupalo ndipo malowo anawapatsa dzina lakuti Ramati-lehi.*+ 18  Ndiyeno anamva ludzu koopsa, ndipo anafuulira Yehova kuti: “Ndinu amene mwandipulumutsa ine mtumiki wanu. Ndiye kodi ndife ndi ludzu, nʼkufera mʼmanja mwa anthu osadulidwa?” 19  Choncho Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi ndipo panayamba kutuluka madzi.+ Samisoni atamwa madziwo, ludzu lake linatha ndipo anapezanso mphamvu. Nʼchifukwa chake anapatsa malowo dzina lakuti Eni-hakore.* Malo amenewa ali ku Lehi mpaka lero. 20  Samisoni anaweruza Isiraeli zaka 20 pa nthawi ya Afilisiti.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kudzamanga.”
Kapena kuti, “kudzakumanga.”
Kutanthauza “Malo Okwezeka a Fupa la Nsagwada.”
Kutanthauza “Kasupe wa Munthu Wofuula.”