Oweruza 18:1-31
18 Mʼmasiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndipo pa nthawiyi fuko la Dani+ linkafuna malo oti likakhaleko, chifukwa linali lisanalandirebe cholowa pakati pa mafuko a Isiraeli.+
2 Anthu a fuko la Dani anatumiza amuna 5 a mʼbanja lawo, amuna olimba mtima ochokera ku Zora ndi ku Esitaoli+ kuti akafufuze zokhudza malowo. Anawauza kuti: “Pitani mukafufuze zokhudza malowo.” Atafika kudera lamapiri la Efuraimu, kunyumba ya Mika,+ anagona kumeneko.
3 Pamene ankayandikira nyumba ya Mika anamva Mlevi wachinyamata uja akulankhula ndipo anazindikira mawu ake.* Choncho anapita kunyumbako nʼkumufunsa kuti: “Wabwera ndi ndani kuno ndipo ukudzatani? Ukufunako chiyani kuno?”
4 Iye anayankha kuti: “Tinagwirizana ndi Mika kuti andilembe ntchito yoti ndikhale wansembe wake.”+
5 Ndiyeno iwo anamuuza kuti: “Tifunsire kwa Mulungu kuti tidziwe ngati ulendo wathuwu tiyende bwino.”
6 Wansembeyo anawauza kuti: “Pitani, musadandaule. Yehova ali nanu pa ulendowu.”
7 Choncho amuna 5 aja anapitiriza ulendo wawo ndipo anafika mumzinda wa Laisi.+ Anaona kuti anthu amumzindawo ankakhala mosadalira aliyense, ngati mmene ankakhalira Asidoni. Iwo ankakhala mosatekeseka+ ndipo panalibe amene anawagonjetsa nʼkumawalamulira mwankhanza kapena kuwasokoneza. Ankakhala kutali kwambiri ndi Asidoni ndipo sankayenderana ndi anthu ena.
8 Atabwerera kwa abale awo ku Zora ndi ku Esitaoli,+ abale awowo anawafunsa kuti: “Mwayendako bwanji?”
9 Iwo anayankha kuti: “Tiyeni tipite tikamenyane nawo, chifukwa ife taona kuti malowo ndi abwino kwambiri. Tisazengereze. Musachedwe, tiyeni tipite tikatenge malowo kuti akhale athu.
10 Mukakafika, mukapeza anthu okhala mosatekeseka,+ ndipo malo ake ndi aakulu kwambiri. Malo amenewa ndi osasowa kalikonse kopezeka padziko lapansi ndipo Mulungu wakupatsani.”+
11 Zitatero amuna 600 okhala ndi zida zankhondo, ochokera mʼbanja la Dani, ananyamuka ku Zora ndi ku Esitaoli.+
12 Anthuwa anayenda nʼkukamanga msasa ku Kiriyati-yearimu+ ku Yuda. Nʼchifukwa chake malo amenewa, omwe ali kumadzulo kwa Kiriyati-yearimu, amadziwika kuti Mahane-dani*+ mpaka lero.
13 Atachoka pamenepo, anakafika kudera lamapiri la Efuraimu ndipo anapita kunyumba ya Mika.+
14 Kenako amuna 5 amene anapita kukafufuza zokhudza mzinda wa Laisi aja,+ anauza abale awowo kuti: “Kodi mukudziwa kuti mʼnyumba izi muli efodi, aterafi,* chifaniziro chosema ndi chifaniziro chachitsulo?+ Ndiyetu dziwani zochita.”
15 Choncho anakhotera kumeneko nʼkufika panyumba ya Mlevi wachinyamata uja,+ kunyumba ya Mika, ndipo anayamba kumufunsa za moyo wake.
16 Pa nthawiyi nʼkuti amuna 600 okhala ndi zida zankhondo, a fuko la Dani+ aja, ataima pageti.
17 Amuna 5 amene anapita kukafufuza malo aja+ anapita kuti akatenge chifaniziro chosema, efodi,+ aterafi*+ ndi chifaniziro chachitsulo.+ (Wansembe uja+ anali ataima pageti ndi amuna 600 okhala ndi zida zankhondowo.)
18 Iwo analowa mʼnyumba ya Mika nʼkutenga chifaniziro chosema, efodi, aterafi* ndi chifaniziro chachitsulo. Atatero wansembeyo anawafunsa kuti: “Mukutani kodi?”
19 Iwo anamuyankha kuti: “Khala chete. Tseka pakamwa pako, ndipo upite nafe kuti ukakhale mlangizi* ndi wansembe wathu. Chabwino nʼchiyani, kuti ukhale wansembe mʼnyumba ya munthu mmodzi,+ ndi kuti ukakhale wansembe wa banja ndi fuko lonse mu Isiraeli?”+
20 Wansembeyo anagwirizana nazo ndipo anatenga efodi, aterafi* ndi chifaniziro chosema+ nʼkunyamuka ndi anthuwo.
21 Atatero anapitiriza ulendo wawo ndipo anaika patsogolo ana, ziweto ndi zinthu zamtengo wapatali.
22 Atayenda kamtunda ndithu kuchokera panyumba ya Mika, anthu a mʼnyumba zoyandikana ndi nyumba ya Mika anasonkhana nʼkuyamba kutsatira anthu a fuko la Dani mpaka kuwapeza.
23 Atawaitana, anthu a fuko la Daniwo anatembenuka nʼkufunsa Mika kuti: “Vuto lako nʼchiyani? Nʼchifukwa chiyani mwatengana gulu chonchi?”
24 Iye anayankha kuti: “Mwatenga milungu yanga imene ndinapanga komanso mwatenga wansembe. Nanga ine nditsala ndi chiyani? Ndiye mungandifunse bwanji kuti, ‘Vuto lako nʼchiyani?’”
25 Anthu a fuko la Dani anamuuza kuti: “Khala chete! Tisamvenso mawu ako, chifukwa anthu okwiya angakuvulazeni, ndipo mwinanso akhoza kukupha iweyo komanso anthu a mʼnyumba yako.”
26 Zitatero anthu a fuko la Dani anapitiriza ulendo wawo, ndipo Mika ataona kuti anali amphamvu kuposa iyeyo, anangotembenuka nʼkumapita kunyumba kwake.
27 Anthu a fuko la Dani atatenga zimene Mika anapanga komanso wansembe wake, anapitiriza ulendo wawo wa ku Laisi+ kukaukira anthu osatekeseka aja.+ Atafika kumeneko anapha anthuwo ndi lupanga nʼkuwotcha mzindawo.
28 Iwo analibe owalanditsa chifukwa mzindawo unali kutali ndi Sidoni ndipo sankayenderana ndi anthu ena. Komanso mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-rehobu.+ Choncho anthu a fuko la Dani anamanganso mzindawo nʼkumakhalamo.
29 Kuwonjezera apo, mzindawu anaupatsa dzina loti Dani,+ kutengera dzina la bambo awo lakuti Dani, amene anali mwana wa Isiraeli.+ Koma dzina loyamba la mzindawu linali Laisi.+
30 Kenako anthu a fuko la Dani anaimika chifaniziro chosema+ chija. Yonatani+ mwana wa Gerisomu,+ mwana wa Mose, komanso ana ake anakhala ansembe a fuko la Dani mpaka tsiku limene anthu okhala kumeneku anatengedwa kupita ku ukapolo.
31 Ndipo chifaniziro chosema chimene Mika anapanga chinakhalabe pomwepo pa nthawi yonse imene nyumba ya Mulungu woona inali ku Silo.+