Oweruza 19:1-30

  • Anthu a fuko la Benjamini anagwirira mkazi ku Gibeya (1-30)

19  Pa nthawi imene mu Isiraeli munalibe mfumu,+ Mlevi wina amene ankakhala mʼdera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu,+ anakwatira wantchito wake wa ku Betelehemu,+ ku Yuda.  Koma mkaziyo anali wosakhulupirika ndipo anachoka nʼkupita kwa bambo ake ku Betelehemu wa ku Yuda. Iye anakhala kumeneko miyezi 4.  Zitatero, mwamuna wakeyo anapita kukakambirana naye kuti abwerere. Pa ulendowo anali ndi mtumiki wake komanso abulu awiri. Atafika, mkaziyo analowetsa mwamunayo mʼnyumba ya bambo ake ndipo bambowo atamuona anasangalala kwambiri.  Ndiyeno apongozi akewo, bambo a mtsikanayo, anamupempha kuti akhalebe komweko masiku atatu ndipo ankadya, kumwa komanso kugona konko.  Pa tsiku la 4, anadzuka mʼmawa nʼkukonzeka kuti anyamuke, koma bambo a mtsikanayo anauza mkamwini wawoyo kuti: “Muyambe mwadya kaye kuti mupeze mphamvu, kenako mukhoza kunyamuka.”  Choncho anakhala pansi ndipo onse awiri anayamba kudya ndi kumwa. Kenako bambo a mtsikanayo anauza mwamunayo kuti: “Bwanji lero mugone mupite mawa, ndipo musangalale?”  Mwamunayo ataimirira kuti azipita, bambowo anapitirizabe kumʼchonderera, choncho anagonanso.  Atadzuka mʼmawa tsiku la 5 kuti azipita, bambo a mtsikanayo anati: “Muyambe mwadya kaye kuti mupeze mphamvu.” Choncho iwo anakhalabe mpaka chakumadzulo, ndipo onse awiri anapitirizabe kudya.  Kenako mwamunayo anaimirira kuti azipita pamodzi ndi mkazi wake ndiponso mtumiki wake. Koma bambo a mtsikanayo, anamuuza kuti: “Komatu dzuwa lapendeka. Bwanji mugonenso? Kunjakutu kuda posachedwa. Gonani ndipo musangalale. Mawa mukhoza kudzuka mʼmawa nʼkumapita kunyumba* kwanu.” 10  Koma mwamunayo sanavomere kuti agonenso. Choncho ananyamuka ndipo anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Yebusi yemwenso ndi Yerusalemu.+ Pa ulendowu anali ndi abulu awiri aja, okhala ndi zishalo ndipo analinso ndi mkazi wake komanso mtumiki wake. 11  Pamene ankayandikira Yebusi, dzuwa linali litatsala pangʼono kulowa ndipo mtumiki uja anauza mbuye wake kuti: “Bwanji tipite mumzinda wa Ayebusiwu kuti tikagone kumeneko?” 12  Koma mbuye wakeyo anayankha kuti: “Tisaime mumzinda wa anthu achilendo omwe si Aisiraeli. Tiyeni tipitirire mpaka tikafike ku Gibeya.”+ 13  Anauzanso mtumiki wakeyo kuti: “Tiyeni tiyesetse tikafike ku Gibeya kapena ku Rama+ ndipo tikagone kumeneko.” 14  Choncho anapitiriza ulendo wawo ndipo dzuwa linayamba kulowa atayandikira ku Gibeya, mʼdera la Benjamini. 15  Atafika mumzinda wa Gibeya, anaima kuti agone mmenemo ndipo anakhala pabwalo la mzindawo. Koma palibe amene anawatenga kuti akagone kunyumba kwake.+ 16  Patapita nthawi, bambo wina wachikulire anatulukira madzulowo akuchokera kumunda. Bamboyu kwawo kunali kudera lamapiri la Efuraimu,+ ndipo pa nthawiyi ankakhala ku Gibeya, koma anthu a mumzindawo anali a fuko la Benjamini.+ 17  Atakweza maso, anaona mwamuna wapaulendo uja ali mʼbwalo la mzinda. Ndiyeno bambo wachikulireyo anamufunsa kuti: “Ukupita kuti, nanga ukuchokera kuti?” 18  Iye anayankha kuti: “Tikuchokera ku Betelehemu wa ku Yuda ndipo tikupita kudera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu. Kumeneko ndiye kwathu. Ndinapita ku Betelehemu wa ku Yuda+ ndipo panopa ndikupita kunyumba ya Yehova,* koma palibe amene wanditenga kuti ndikagone kunyumba kwake. 19  Tili ndi udzu wokwanira komanso chakudya china cha abulu+ athu ndipo tilinso ndi mkate+ ndi vinyo zokwanira ineyo, mkaziyu komanso mtumiki wathuyu. Chilichonse tili nacho.” 20  Koma bambo wachikulireyo anati: “Mtendere ukhale nawe! Ine ndikupatsa chilichonse chimene ungafunikire. Koma usagone pabwalo la mzindali.” 21  Atatero anatengera Mlevi uja kunyumba kwake ndipo anapatsa abulu akewo chakudya. Kenako anasamba mapazi awo nʼkuyamba kudya ndi kumwa. 22  Ali mkati mosangalala, amuna opanda pake amumzindawo, anazungulira nyumbayo nʼkuyamba kumenya chitseko. Iwo ankauza bambo wachikulireyo, mwiniwake wa nyumbayo, kuti: “Tulutsa mwamuna amene wabwera mʼnyumba yako kuti tigone naye.”+ 23  Mwini nyumbayo anatuluka nʼkuwauza kuti: “Ayi abale anga, musachite zoipa zimenezo, chifukwatu munthuyu ndi mlendo wanga. Musachite zinthu zochititsa manyazi chonchi. 24  Ndili ndi mwana wamkazi amene ndi namwali ndiponso pali wantchito wamkazi wa mwamunayu. Bwanji ndikutulutsireni amenewa kuti muwachite chipongwe chimene mukufunacho?+ Koma mwamunayu musamʼchitire zinthu zochititsa manyazi ngati zimenezo.” 25  Koma anthuwo sanamumvere, moti Mleviyo anatenga mkazi wakeyo+ nʼkumupereka kwa anthuwo. Anthuwo anayamba kumugwiririra ndiponso kumuzunza usiku wonse mpaka mʼbandakucha. Kenako kutayamba kucha anamusiya kuti azipita. 26  Mkaziyo atafika panyumba ya bambo wachikulire uja, mmene munali mbuye wake, anagwera pakhomo, ndipo anakhala pomwepo mpaka kutayera. 27  Mbuye wake atadzuka mʼmawa nʼkutsegula zitseko za nyumbayo, kuti apitirize ulendo wake, anaona mkazi uja atagona panja pa nyumbayo manja ake ali pakhomo. 28  Ndiyeno anauza mkaziyo kuti: “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe. Zitatero, anamukweza pabulu nʼkumapita. 29  Atafika kwawo, analowa mʼnyumba nʼkutenga mpeni wophera nyama. Atatero anaduladula mkazi uja mapisi 12 ndipo anatumiza pisi imodzi mʼchigawo chilichonse cha Isiraeli. 30  Zitatero, aliyense amene anaona zimenezo anati: “Zoterezi sizinachitikepo kapena kuoneka kuchokera pa tsiku limene Aisiraeli anachoka kudziko la Iguputo mpaka lero. Nkhani imeneyi muiganizire mofatsa, muikambirane+ ndipo mutiuze zochita.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nʼkumapita kutenti.”
Mabaibulo ena amati, “ndipo ndimatumikira panyumba ya Yehova.”