Oweruza 6:1-40

  • Amidiyani ankapondereza Aisiraeli (1-10)

  • Mngelo anatsimikizira woweruza Gidiyoni kuti amuthandiza (11-24)

  • Gidiyoni anagwetsa guwa lansembe la Baala (25-32)

  • Mzimu wa Mulungu unathandiza Gidiyoni (33-35)

  • Kuyesa ndi ubweya wa nkhosa (36-40)

6  Koma Aisiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka 7.+  Amidiyaniwo anayamba kupondereza Aisiraeli.+ Chifukwa cha zimenezi, Aisiraeli anakonza malo oti azibisalako* mʼmapiri, mʼmapanga ndi mʼmalo ena ovuta kufikako.+  Aisiraeli akalima minda yawo, Amidiyani, Aamaleki+ ndi anthu a Kumʼmawa+ ankabwera kudzawaukira.  Ankabwera nʼkuwawonongera zokolola zawo zonse mpaka kukafika ku Gaza. Sankawasiyira chakudya chilichonse ngakhalenso nkhosa, ngʼombe kapena bulu.+  Iwo ankabwera ndi ziweto zawo ndi matenti awo. Ankabwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Ankabwera mʼdzikomo nʼkumaliwononga.  Choncho Aisiraeli ankavutika kwadzaoneni chifukwa cha Amidiyani, ndipo iwo anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+  Aisiraeli atafuulira Yehova kuti awathandize chifukwa cha Amidiyani,+  Yehova anawatumizira mneneri yemwe anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndinakutulutsani mu Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.+  Choncho ndinakupulumutsani kwa Aiguputo ndiponso kwa anthu onse amene ankakuponderezani, ndipo ndinawathamangitsa pamaso panu nʼkukupatsani dziko lawo.+ 10  Komanso ndinakuuzani kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Musamalambire* milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.”+ Koma inu simunamvere mawu anga.’”+ 11  Kenako, kunabwera mngelo wa Yehova+ nʼkukhala pansi pa mtengo waukulu ku Ofira. Mtengo umenewu unali wa Yowasi, Mwabi-ezeri.+ Pa nthawiyi, Gidiyoni+ mwana wa Yowasi, ankapuntha tirigu moponderamo mphesa kuti Amidiyani asaone. 12  Mngelo wa Yehova anafika pamene iye anali, ndipo anati: “Yehova ali nawe,+ msilikali wamphamvu iwe.” 13  Koma Gidiyoni anayankha kuti: “Pepani mbuyanga, ngati Yehova ali nafe, nʼchifukwa chiyani tikukumana ndi mavuto onsewa?+ Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiuza zija zili kuti?+ Iwo anatiuza kuti, ‘Yehova ndi amene anatitulutsa ku Iguputo.’+ Koma tsopano Yehova watisiya,+ ndipo watipereka kwa Amidiyani.” 14  Atatero, Yehova anamuyangʼana nʼkumuuza kuti: “Pita ndi mphamvu zimene uli nazozi, ndipo udzapulumutsa Isiraeli kwa Amidiyani.+ Kodi si ine amene ndakutuma?” 15  Gidiyoni anayankha kuti: “Pepani Yehova. Kodi ndidzapulumutsa bwanji Isiraeli? Pajatu banja lathu ndi lalingʼono kwambiri mʼfuko lonse la Manase, ndipo mʼnyumba ya bambo anga, wamngʼono kwambiri ndine.” 16  Koma Yehova anamuuza kuti: “Chifukwa ndidzakhala nawe,+ udzapha Amidiyani ngati ukupha munthu mmodzi.” 17  Kenako iye anati: “Ngati mwandikomera mtima, mundionetse chizindikiro kuti nditsimikize kuti ndinudi amene mukulankhula nane. 18  Chonde musachoke, mpaka nditabwera nʼkukupatsani mphatso.”+ Choncho iye anati: “Ndikhalabe pompano mpaka utabweranso.” 19  Ndiyeno Gidiyoni analowa mʼnyumba nʼkumuphera mwana wa mbuzi. Anatenganso ufa wokwana muyezo umodzi wa efa*+ nʼkupanga mikate yopanda zofufumitsa. Atatero, anatenga nyamayo nʼkuiika mʼbasiketi, ndipo msuzi anauika mumphika. Kenako anatenga zinthu zimenezi nʼkukamupatsa mngeloyo pansi pa mtengo waukulu uja. 20  Mngelo wa Mulungu woona anamuuza kuti: “Tenga nyamayi ndi mikateyo nʼkuziika pamwala waukuluwo, ndipo ukhuthule msuziwo.” Gidiyoni anachitadi zomwezo. 21  Kenako mngelo wa Yehova anakhudza nyama ndi mikateyo ndi nsonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake. Atatero, moto unayaka pamwalawo nʼkuwotcheratu nyama ndi mkatewo.+ Zitatero mngelo wa Yehovayo anazimiririka. 22  Tsopano Gidiyoni anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.+ Nthawi yomweyo Gidiyoni anati: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Ndaonana ndi mngelo wa Yehova maso ndi maso.”+ 23  Koma Yehova anamuuza kuti: “Mtendere ukhale nawe. Usachite mantha.+ Suufa.” 24  Choncho, Gidiyoni anamangira Yehova guwa lansembe pamalowo, ndipo limatchedwa Yehova-salomu*+ mpaka pano. Guwalo lili ku Ofira, mzinda wa Aabi-ezeri, mpaka pano. 25  Usiku womwewo, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Tenga ngʼombe yaingʼono yamphongo ya bambo ako, ngʼombe yachiwiri yazaka 7 ija. Kenako ugwetse guwa lansembe la Baala la bambo ako ndipo udule mzati wopatulika* umene uli pafupi ndi guwalo.+ 26  Umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe poyala miyala pamwamba pa malo otetezekawa. Ukatero, utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo yachiwiri ija nʼkuipereka monga nsembe yopsereza pankhuni za mzati wopatulika* umene udulewo.” 27  Choncho Gidiyoni anatenga amuna 10 pa atumiki ake ndi kuchita zonse zimene Yehova anamuuza. Koma chifukwa choti ankaopa kwambiri anthu amʼnyumba ya bambo ake ndi anthu a mumzindawo, anachita zimenezi usiku osati masana. 28  Amuna amumzindawo atadzuka mʼmawa, anaona kuti guwa lansembe la Baala lagwetsedwa, ndipo mzati wopatulika* umene unali pambali pake wadulidwa. Anaonanso kuti paguwa limene lamangidwa, panali pataperekedwa nsembe ngʼombe yaingʼono yamphongo yachiwiri ija. 29  Ndiyeno anayamba kufunsana kuti: “Ndani wachita zimenezi?” Atafufuza ananena kuti: “Wachita zimenezi ndi Gidiyoni, mwana wa Yowasi.” 30  Zitatero amuna a mumzindawo anauza Yowasi kuti: “Bweretsa mwana wako timuphe, chifukwa wagwetsa guwa lansembe la Baala nʼkudula mzati wopatulika* umene unali pambali pake.” 31  Koma Yowasi+ anauza onse amene anamuukirawo kuti: “Kodi inu mukuyenera kuteteza Baala? Kodi mukuyenera kumʼpulumutsa? Aliyense wofuna kumuteteza ayenera kuphedwa mʼmawa womwe uno.+ Ngati Baalayo ndi mulungu, adziteteze yekha+ chifukwa munthu wina wamugwetsera guwa lake lansembe.” 32  Pa tsikuli Yowasi anapatsa Gidiyoni dzina lakuti Yerubaala* nʼkunena kuti: “Baala adziteteze yekha, chifukwa munthu wina wamugwetsera guwa lake lansembe.” 33  Amidiyani+ ndi Aamaleki onse,+ pamodzi ndi anthu onse a Kumʼmawa anasonkhanitsa asilikali awo+ ndipo anawoloka mtsinje nʼkukamanga msasa mʼchigwa cha Yezereeli. 34  Zitatero, Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova,+ moti analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndipo Aabi-ezeri+ anasonkhana pamodzi nʼkuyamba kumutsatira. 35  Iye anatumiza uthenga kwa anthu amʼdera lonse la fuko la Manase, ndipo nawonso anasonkhana pamodzi nʼkuyamba kumutsatira. Anatumizanso uthenga mʼmadera onse a mafuko a Aseri, Zebuloni ndi Nafitali, ndipo nawonso anabwera kudzakumana naye. 36  Kenako Gidiyoni anauza Mulungu woona kuti: “Kuti ndidziwe kuti mudzagwiritsa ntchito ine populumutsa Isiraeli, ngati mmene mwalonjezera,+ 37  ndiika ubweya wa nkhosa pansi, pamalo opunthira mbewu. Ngati mame angagwe pa ubweya wokhawu, koma nthaka yonse nʼkukhala youma, ndidzadziwa kuti mudzapulumutsadi Isiraeli pogwiritsa ntchito ineyo, ngati mmene mwalonjezera.” 38  Ndipo zinachitikadi choncho. Atadzuka mʼmawa tsiku lotsatira nʼkufinya ubweya wa nkhosawo, ubweyawo unatulutsa madzi oti akhoza kudzaza mbale yolowa yaikulu. 39  Komabe, Gidiyoni anauza Mulungu woona kuti: “Musandikwiyire chonde, ndiloleni ndipemphenso kamodzi kokha. Chonde ndiloleni ndikuyeseninso kamodzi kokha ndi ubweyawu. Ubweya wokhawu ukhale wouma, koma nthaka yonse inyowe ndi mame.” 40  Choncho Mulungu anachitadi zimenezi usiku umenewo. Ubweya wokhawo unali wouma koma nthaka yonse inanyowa ndi mame.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “malo apansi osungiramo zinthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Musamaope.”
Pafupifupi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Kutanthauza “Yehova ndi Mtendere.”
Kutanthauza “Baala Adziweruzire Yekha Mlandu.”