Oweruza 7:1-25

  • Gidiyoni ndi anthu ake 300 (1-8)

  • Asilikali a Gidiyoni anagonjetsa Amidiyani (9-25)

    • “Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!” (20)

    • Chipwirikiti mumsasa wa Amidiyani (21, 22)

7  Kenako Yerubaala,+ kapena kuti Gidiyoni, ndi anthu onse amene anali naye, anadzuka mʼmawa nʼkumanga msasa pa Kasupe wa Harodi. Msasa wa Amidiyani unali chakumpoto, mʼchigwa, kuphiri la More.  Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene uli nawowa ndi ambiri kuti ndipereke Amidiyani mʼmanja mwawo,+ chifukwa Isiraeli angadzitame pamaso panga nʼkumanena kuti, ‘Ndinadzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.’+  Tsopano lengeza kwa anthu onse kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha kapena kunjenjemera abwerere kunyumba.’”+ Choncho Gidiyoni anayesa anthuwo ndipo anthu 22,000 anabwerera nʼkutsala anthu 10,000.  Komabe, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene atsalawa adakali ambiri. Pita nawo kumadzi kuti ndikawayese kumeneko. Amene ndikakuuze kuti, ‘Uyu apite nawe,’ ukapite naye, koma amene ndikakuuze kuti, ‘Uyu asapite,’ usakapite naye.”  Choncho Gidiyoni anauza anthuwo kuti apite kumadzi. Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Aliyense amene akamwe madzi potunga madziwo ndi manja, ukamuike kumbali ina. Ndipo aliyense amene akamwe madzi atagwada nʼkuwerama, ukamuike kumbali inanso.”  Ndipo anthu amene anamwa madzi ndi manja analipo 300. Koma ena onse anamwa atagwada nʼkuwerama.  Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Ndidzakupulumutsani pogwiritsa ntchito amuna 300 amene amwa madzi ndi manja awo, ndipo ndidzapereka Amidiyani mʼmanja mwanu.+ Koma ena onsewo abwerere kunyumba.”  Choncho, iye anabweza amuna ena onse a Isiraeli nʼkutsala ndi amuna 300 aja. Iwo anatenga chakudya ndi malipenga a nyanga ya nkhosa kwa anthu amene ankabwererawo. Msasa wa Amidiyani unali kumunsi kwawo, mʼchigwa.+  Usiku umenewo Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Nyamuka, pita kumsasa wa Amidiyani kukamenyana nawo, chifukwa ndawapereka mʼmanja mwako.+ 10  Koma ngati ukuchita mantha kupita kukamenyana nawo, upiteko kaye ndi mtumiki wako, Pura. 11  Ukakafika, ukamvetsere zolankhula zawo. Ukakatero ukalimba mtima* ndipo udzapitadi kumsasawo kukamenyana nawo.” Kenako Gidiyoni ndi mtumiki wake Pura, anatsetserekera kumunsi pafupi kwambiri ndi asilikali amene anali mumsasawo. 12  Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kumʼmawa+ anadzaza mʼchigwa chonse chifukwa anali ambiri ngati dzombe. Ngamila zawo zinali zosawerengeka,+ zambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 13  Gidiyoni atafika kumsasawo, anamva wina akufotokozera mnzake zimene analota kuti: “Tamvera zimene ndalota ine. Ndalota mkate wa balere wozungulira ukugubuduzika kubwera mumsasa wa Amidiyani. Mkatewo unafika nʼkuwomba tenti ina moti tentiyo inagwa.+ Mkatewo unagadabuza tentiyo mpaka kuphwasuka.” 14  Pamenepo mnzakeyo anayankha kuti: “Si china ayi. Imeneyi ndi nkhondo ya Gidiyoni+ mwamuna wa ku Isiraeli, mwana wa Yowasi. Mulungu wapereka Amidiyani ndi msasa wathu wonse mʼmanja mwake.”+ 15  Gidiyoni atangomva malotowo ndi tanthauzo lake,+ analambira Mulungu. Kenako anabwerera kumsasa wa Isiraeli nʼkunena kuti: “Tiyeni, Yehova wapereka msasa wa Amidiyani mʼmanja mwanu.” 16  Ndiyeno amuna 300 aja anawagawa mʼmagulu atatu. Aliyense anamupatsa lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi mtsuko waukulu wopanda kanthu, ndipo mʼmitsukomo anaikamo zounikira. 17  Kenako anawauza kuti: “Muone zimene ndikuchita, ndipo nanunso muchite zomwezo. Ndikakafika mʼmalire a msasa, zimene ine ndikachite, nanunso mukachite zomwezo. 18  Ndikakaliza lipenga la nyanga ya nkhosa pamodzi ndi anthu onse a mʼgulu langa, nanunso mukalize malipenga anu kuzungulira msasa wonse, ndipo mukafuule kuti, ‘Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!’” 19  Gidiyoni ndi amuna 100 amene anali naye anafika kumalire a msasa ulonda wapakati pa usiku* ukungoyamba kumene. Pa nthawiyi nʼkuti atangosintha kumene alonda ena apamsasa. Ndiyeno analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ nʼkuphwanya mitsuko yaikulu imene inali mʼmanja mwawo.+ 20  Atatero magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa nʼkuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Ananyamula zounikira kudzanja lawo lamanzere ndipo ankaliza malipenga omwe anali kudzanja lawo lamanja, nʼkuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova komanso ya Gidiyoni!” 21  Pa nthawi yonseyi nʼkuti aliyense ataimirira pamalo ake kuzungulira msasawo ndipo asilikali onse a Amidiyani anayamba kuthawa kwinaku akufuula.+ 22  Amuna 300 aja anapitiriza kuliza malipenga, ndipo Yehova anachititsa Amidiyani kuukirana okhaokha mumsasa wonsewo.+ Asilikaliwo anathawa mpaka kukafika ku Beti-sita ndi ku Zerera mpaka kumalire kwa mzinda wa Abele-mehola+ pafupi ndi Tabati. 23  Komanso, anasonkhanitsa amuna a mu Isiraeli kuchokera mʼmafuko a Nafitali, Aseri ndi Manase yense,+ ndipo anathamangitsa Amidiyani. 24  Gidiyoni anatumiza uthenga kudera lonse lamapiri la Efuraimu, wakuti: “Pitani ku Beti-bara ndi kumtsinje wa Yorodano, ndipo mukaike amuna mʼmalo owolokera kuti Amidiyani asadutse.” Choncho, amuna onse a Efuraimu anasonkhana ndipo anatseka malo owolokera Yorodano ndi mitsinje yake ingʼonoingʼono mpaka ku Beti-bara. 25  Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi. Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitiriza kuthamangitsa Amidiyani+ ndipo anabweretsa mutu wa Orebi ndi wa Zeebi kwa Gidiyoni mʼchigawo cha Yorodano.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “manja ako akakhala amphamvu.”
“Ulonda wapakati pa usiku” unkayamba 10 koloko usiku mpaka 2 koloko usiku.