Oweruza 8:1-35

  • Amuna a ku Efuraimu anakangana ndi Gidiyoni (1-3)

  • Mafumu a ku Midiyani anathamangitsidwa nʼkuphedwa (4-21)

  • Gidiyoni anakana ufumu (22-27)

  • Mbiri ya Gidiyoni (28-35)

8  Kenako amuna a ku Efuraimu anamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi? Bwanji sunatiitane pokamenyana ndi Amidiyani?”+ Ndipo iwo anakangana naye kwambiri.+  Koma iye anawayankha kuti: “Kodi ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu? Kodi zimene Efuraimu wakunkha+ si zabwino kwambiri kuposa mphesa zimene Abi-ezeri wakolola?+  Mulungu anapereka Orebi ndi Zeebi,+ akalonga a Midiyani mʼmanja mwanu. Ndiye ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?” Atanena mawu amenewa, mkwiyo wawo unatha.  Kenako Gidiyoni anafika ku Yorodano nʼkuwoloka mtsinjewo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nawo aja. Anali atatopa koma ankathamangitsabe adaniwo.  Ndiyeno iye anapempha amuna a ku Sukoti kuti: “Agawireni mkate anthu amene akunditsatirawa chifukwa atopa. Ndikuthamangitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.”  Koma akalonga a ku Sukoti anayankha kuti: “Tipatse asilikali ako mkate chifukwa chiyani? Wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?”  Atatero Gidiyoni anawauza kuti: “Chifukwa cha zimene mwanenazi, Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna mʼmanja mwanga, ndidzakukwapulani ndi mitengo yaminga yamʼchipululu komanso ndi zitsamba zaminga.”+  Atachoka kumeneko anapita ku Penueli ndipo anawapemphanso chimodzimodzi, koma amuna a ku Penueli anamuyankha ngati mmene amuna a ku Sukoti aja anamuyankhira.  Choncho anauzanso amuna a ku Penueli kuti: “Ndikabwerako bwino, nsanja yanuyi ndidzaigwetsa.”+ 10  Pa nthawiyi nʼkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori pamodzi ndi asilikali awo pafupifupi 15,000. Asilikaliwa ndi amene anatsala pa gulu lonse la asilikali a Kumʼmawa+ chifukwa asilikali 120,000 anali ataphedwa. 11  Gidiyoni anapitirizabe ulendo wake ndipo anadutsa njira ya anthu okhala mʼmatenti, kumʼmawa kwa Noba ndi Yogebeha+ ndipo anaukira msasa wa adaniwo iwo asanakonzekere. 12  Zeba ndi Zalimuna atayamba kuthawa, iye anawathamangitsa mpaka kuwagwira. Mafumu a Midiyaniwa atagwidwa, gulu lawo lonse linachita mantha. 13  Gidiyoni mwana wa Yowasi anayamba kubwerera kuchokera kunkhondo ndipo anadutsa njira yopita ku Heresi. 14  Ali mʼnjira, anagwira mnyamata wa ku Sukoti nʼkuyamba kumufunsa mafunso. Mnyamatayo analembera Gidiyoni mayina okwana 77 a akalonga ndi akulu a ku Sukoti. 15  Choncho, Gidiyoni anapita kwa amuna amumzinda wa Sukoti nʼkuwauza kuti: “Zeba ndi Zalimuna aja si awa? Amene munandinyoza nawo aja kuti, ‘Ukuti tipatse anyamata ako otopawo mkate chifukwa chiyani? Wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?’”+ 16  Ndiyeno anatenga akulu amumzindawo, nʼkutenganso mitengo yaminga yamʼchipululu ndi zitsamba zaminga ndipo anawakhaulitsa amuna a ku Sukotiwo.+ 17  Anagwetsanso nsanja ya ku Penueli+ ija nʼkupha amuna amumzindawo. 18  Gidiyoni anafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti: “Kodi amuna amene munapha ku Tabori anali otani?” Iwo anayankha kuti: “Anali ngati iweyo. Aliyense ankaoneka ngati mwana wa mfumu.” 19  Gidiyoni atamva zimenezi anati: “Anali abale anga, ana a amayi anga. Ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, mukanapanda kuwapha, inenso sindikanakuphani.” 20  Ndiyeno anauza Yeteri mwana wake woyamba kuti: “Nyamuka uwaphe.” Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake chifukwa anachita mantha, poti anali adakali wamngʼono. 21  Choncho Zeba ndi Zalimuna anati: “Nyamuka iweyo utiphe wekha. Munthu amaweruzidwa mogwirizana ndi mphamvu zake.” Ndiyeno Gidiyoni ananyamuka nʼkupha Zeba ndi Zalimuna,+ ndipo anatenga zokongoletsa zooneka ngati mwezi zimene zinali pamakosi a ngamila zawo. 22  Kenako amuna a Isiraeli anauza Gidiyoni kuti: “Ukhale wolamulira wathu, iweyo, mwana wako ndi mdzukulu wako, chifukwa watipulumutsa kwa Amidiyani.”+ 23  Koma Gidiyoni anawayankha kuti: “Ineyo sindikhala wokulamulirani, ngakhalenso mwana wanga sakhala wokulamulirani. Yehova ndi amene azikulamulirani.”+ 24  Ndipo anawauzanso kuti: “Ndikupempheni chinthu chimodzi: Aliyense andipatse ndolo yapamphuno kuchokera pa zimene watenga kunkhondo.” (Ogonjetsedwawo anali ndi ndolo zapamphuno zagolide, chifukwa anali Aisimaeli.)+ 25  Iwo anayankha kuti: “Tikupatsani.” Atatero anayala mkanjo, ndipo aliyense anaponyapo ndolo yapamphuno kuchokera pa zimene anatenga kunkhondo. 26  Ndolo zapamphuno zagolide zimene anamupatsa zinali zolemera masekeli* agolide 1,700, osawerengera zokongoletsa zooneka ngati mwezi, zovala mʼkhosi komanso zovala zaubweya wa nkhosa zamtundu wapepo zimene mafumu a Midiyani aja anavala, osawerengeranso mikanda imene inali mʼkhosi mwa ngamila zawo.+ 27  Gidiyoni anatenga golideyo nʼkupanga chovala cha efodi,+ ndipo anachiika pamalo oonekera mumzinda wakwawo wa Ofira.+ Aisiraeli onse anayamba kuchilambira,*+ moti chinakhala msampha kwa Gidiyoni ndi anthu a mʼbanja lake.+ 28  Choncho, Aisiraeli anagonjetsa Amidiyani,+ ndipo Amidiyaniwo anasiya kulimbana nawo.* Zitatero, dziko linakhala pa mtendere zaka 40 mʼmasiku a Gidiyoni.+ 29  Yerubaala+ mwana wa Yowasi, anabwerera kunyumba kwawo nʼkumakhala komweko. 30  Gidiyoni anali ndi ana 70,* chifukwa anali ndi akazi ambiri. 31  Analinso ndi mkazi wamngʼono ku Sekemu, amene anamuberekera mwana wamwamuna, ndipo anamʼpatsa dzina lakuti Abimeleki.+ 32  Kenako Gidiyoni mwana wa Yowasi anamwalira atakalamba komanso atakhala ndi moyo wabwino, ndipo anamuika mʼmanda a Yowasi bambo ake, mumzinda wa Ofira wa Aabi-ezeri.+ 33  Gidiyoni atangomwalira, Aisiraeli anayambanso kulambira Abaala,+ moti anaika Baala-beriti kukhala mulungu wawo.+ 34  Aisiraeliwo sanakumbukire Yehova Mulungu wawo+ amene anawapulumutsa kwa adani awo onse owazungulira,+ 35  ndipo sanasonyeze chikondi chokhulupirika kwa anthu a mʼbanja la Yerubaala, kapena kuti Gidiyoni, pa zabwino zonse zimene iye anachitira Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anayamba kuchita nacho chiwerewere mwauzimu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sanakwezenso mutu wawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhala ndi ana 70 otuluka mʼchiuno mwake.”