Oweruza 9:1-57

  • Abimeleki anakhala mfumu ku Sekemu (1-6)

  • Mwambi wa Yotamu (7-21)

  • Ulamuliro wankhanza wa Abimeleki (22-33)

  • Abimeleki anapha anthu ku Sekemu (34-49)

  • Mzimayi anavulaza Abimeleki ndipo anafa (50-57)

9  Patapita nthawi, Abimeleki+ mwana wa Yerubaala, anapita ku Sekemu kwa azichimwene awo a mayi ake. Ndipo anauza amalume akewo komanso banja lonse la bambo a mayi ake kuti:  “Chonde funsani atsogoleri* onse a ku Sekemu kuti, ‘Chabwino nʼchiyani kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala+ azikulamulirani, ndi kuti azikulamulirani munthu mmodzi? Ndipo musaiwale kuti ine ndi inu ndife magazi amodzi.’”*  Choncho azichimwene awo a mayi ake anakauza atsogoleri onse a Sekemu zimenezi, ndipo mitima yawo inayamba kutsatira Abimeleki, chifukwa anati: “Ndi mchimwene wathu ameneyu.”  Kenako iwo anatenga ndalama zasiliva 70 mʼkachisi wa Baala-beriti+ nʼkumupatsa. Ndalama zimenezi Abimeleki analembera ganyu anthu osowa zochita ndi achipongwe kuti azimʼtsatira.  Atatero anapita kunyumba kwa bambo ake ku Ofira+ nʼkupha abale ake,+ ana aamuna 70 a Yerubaala, ndipo anawaphera pamwala umodzi. Amene anapulumuka anali Yotamu yekha, mwana wamngʼono mwa ana aamuna a Yerubaala, chifukwa anabisala.  Kenako atsogoleri onse a ku Sekemu ndi anthu onse a ku Beti-milo anasonkhana kumene kunali chipilala pafupi ndi mtengo waukulu ku Sekemu. Kumeneko anamuika Abimeleki kukhala mfumu.+  Yotamu atauzidwa zimene zinachitikazo, nthawi yomweyo anapita pamwamba pa phiri la Gerizimu+ nʼkulankhula mofuula kuti: “Ndimvereni, inu atsogoleri a ku Sekemu, ndipo mukatero Mulungu akumverani.  Panali mitengo imene inkafuna kudzoza mfumu yawo. Choncho inauza mtengo wa maolivi kuti, ‘Ukhale mfumu yathu.’+  Koma mtengo wa maoliviwo unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye kutulutsa mafuta amene amawagwiritsa ntchito potamanda Mulungu ndi anthu nʼkupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’ 10  Kenako mitengoyo inauza mtengo wa mkuyu kuti, ‘Bwera ukhale mfumu yathu.’ 11  Koma mtengo wa mkuyuwo unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye kukoma kwanga ndi zipatso zanga zabwinozi nʼkupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’ 12  Ndiyeno mitengoyo inauza mtengo wa mpesa kuti, ‘Bwera ukhale mfumu yathu.’ 13  Poyankha mtengo wa mpesawo unati, ‘Kodi ndisiye vinyo wanga watsopano amene amasangalatsa Mulungu ndi anthu nʼkupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’ 14  Pomaliza, mitengo ina yonse inauza kamtengo kaminga kuti, ‘Bwera ukhale mfumu yathu.’+ 15  Kamtengo kamingako kanauza mitengoyo kuti, ‘Ngati mukufunadi kundidzoza kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mubisale mumthunzi wanga. Koma ngati si choncho, moto utuluke mwa ine nʼkuwotcha mikungudza ya ku Lebanoni.’ 16  Kodi mukuona kuti mwachita bwino kuika Abimeleki kukhala mfumu?+ Kodi mwachita zimenezi kuchokera pansi pa mtima? Nanga Yerubaala ndi banja lake mwamuchitira zabwino? Kodi zimene mwamuchitira ndi zogwirizana ndi zimene iye anachita? 17  Pamene bambo anga anakumenyerani nkhondo,+ anaika moyo wawo pangozi kuti akulanditseni kwa Amidiyani.+ 18  Koma inu lero mwaukira banja la bambo anga ndipo mwapha ana awo aamuna 70 pamwala umodzi.+ Kenako mwaika Abimeleki, mwana wa kapolo wake wamkazi,+ kukhala mfumu ya atsogoleri a ku Sekemu chifukwa chongoti ndi mchimwene wanu. 19  Ngati mwachitira zimenezi Yerubaala kuchokera pansi pa mtima ndipo mukuona kuti mwachita bwino, sangalalani ndi Abimeleki ndipo nayenso asangalale nanu. 20  Koma ngati si choncho, moto utuluke mwa Abimeleki nʼkuwotcha atsogoleri a ku Sekemu ndi ku Beti-milo,+ komanso moto utuluke mwa atsogoleri a ku Sekemu ndi ku Beti-milo nʼkuwotcha Abimeleki.”+ 21  Kenako Yotamu+ anathawira ku Beere, ndipo anakhala kumeneko chifukwa choopa mʼchimwene wake Abimeleki. 22  Abimeleki analamulira Aisiraeli kwa zaka zitatu. 23  Ndiyeno Mulungu analola kuti pakhale chidani pakati pa Abimeleki ndi atsogoleri a ku Sekemu, moti atsogoleriwo anayamba kuchitira Abimeleki zachinyengo. 24  Zimenezi zinachitika kuti anthu amene anali ndi mlandu wa magazi abwezeredwe nkhanza zimene anachitira ana aamuna 70 a Yerubaala. Zinachitikanso kuti Abimeleki alangidwe chifukwa chopha azichimwene ake+ ndiponso kuti atsogoleri a ku Sekemu alangidwe chifukwa chothandiza Abimeleki kuti aphe azichimwene akewo. 25  Choncho, atsogoleri a ku Sekemu anatumiza anthu kuti akamubisalire pamwamba pa mapiri, ndipo anthuwo ankalanda katundu munthu aliyense wodutsa njira imeneyo. Patapita nthawi, Abimeleki anauzidwa zimenezi. 26  Kenako Gaala mwana wa Ebedi anabwera ku Sekemu+ pamodzi ndi abale ake ndipo atsogoleri a ku Sekemu anayamba kumʼkhulupirira. 27  Iwo anapita mʼmunda nʼkukathyola mphesa, kuziponda ndipo kenako anachita chikondwerero. Atatero analowa mʼnyumba ya mulungu wawo+ nʼkuyamba kudya, kumwa ndi kutemberera Abimeleki. 28  Ndiyeno Gaala mwana wa Ebedi anati: “Abimeleki ndi ndani, ndipo Sekemu ndi ndani kuti timʼtumikire? Kodi iye si mwana wa Yerubaala,+ ndipo mtumiki wake si Zebuli? Zitumikirani ana a Hamori, bambo a Sekemu. Koma ifeyo tizitumikira Abimeleki chifukwa chiyani? 29  Zikanakhala kuti ineyo ndikuwalamulira anthu awa, ndikanamʼchotsa Abimeleki.” Ndiyeno anauza Abimeleki kuti: “Wonjezera asilikali ako ndipo ubwere tidzamenyane.” 30  Zebuli, kalonga wa mzindawo, atamva mawu a Gaala mwana wa Ebedi, anakwiya koopsa. 31  Choncho anatumiza anthu mobisa kuti akauze Abimeleki kuti: “Gaala mwana wa Ebedi ndi abale ake abwera ku Sekemu ndipo akulimbikitsa anthu amumzindawu kuti akuukireni. 32  Inuyo ndi anthu anu mubwere usiku, ndipo mukamʼbisalire mʼtchire. 33  Ndiyeno mawa dzuwa likangotuluka, mudzadzuke nʼkuukira mzindawu. Ndipo iye ndi anthu amene ali nawo akadzatuluka kudzamenyana nanu, mudzachite chilichonse chomwe mungathe kuti mumʼgonjetse.” 34  Choncho Abimeleki ndi anthu onse amene anali naye anadzuka usiku nʼkubisala kunja kwa mzinda wa Sekemu, atagawana mʼmagulu 4. 35  Gaala mwana wa Ebedi atatuluka nʼkuima pageti la mzinda, Abimeleki ndi anthu amene anali naye anatuluka pamalo amene anabisala. 36  Gaala ataona anthuwo, anauza Zebuli kuti: “Taona, kukubwera anthu kuchokera pamwamba pa mapiri.” Koma Zebuli anati: “Si anthu amenewo, ukuona zithunzithunzi za mapiri.” 37  Patapita nthawi Gaala ananenanso kuti: “Taona, anthu akubwera kuchokera chapakati apo, ndipo gulu limodzi ladzera njira yodutsa kumtengo waukulu wa Meyonenimu.” 38  Zebuli anamuyankha kuti: “Suja umadzitama kuti, ‘Abimeleki ndi ndani kuti tizimutumikira?’+ Amenewa si anthu amene unawakana aja? Ndiyetu pita ukamenyane nawo.” 39  Choncho Gaala anatsogolera atsogoleri a ku Sekemu nʼkuyamba kumenyana ndi Abimeleki. 40  Abimeleki anayamba kuthamangitsa Gaala, ndipo Gaala anathawa. Anthu ambiri anaphedwa ndipo mitembo inali paliponse mpaka kukafika kugeti la mzinda. 41  Abimeleki anapitiriza kukhala ku Aruma, ndipo Zebuli+ anathamangitsa Gaala ndi abale ake ku Sekemu. 42  Tsiku lotsatira anthu anapita kunja kwa mzinda, ndipo Abimeleki anauzidwa za nkhaniyi. 43  Atamva zimenezi anatenga anthu ake nʼkuwagawa mʼmagulu atatu ndipo anabisalira anthuwo mʼtchire. Ataona anthu akutuluka mumzindawo, anapita nʼkukawapha. 44  Abimeleki ndi magulu amene anali nawo anathamanga nʼkukaima pageti la mzinda, pamene magulu awiri anathamangira kwa anthu amene anali kunja kwa mzinda, ndipo anayamba kuwapha. 45  Ndiyeno Abimeleki anamenyana ndi anthu amumzindawo tsiku lonse nʼkuulanda. Anapha anthu amene anali mumzindawo ndipo anaugwetsa+ nʼkuthira mchere panthaka ya mzindawo. 46  Atsogoleri onse okhala munsanja ya Sekemu atamva zimenezi, nthawi yomweyo analowa mʼchipinda chotetezeka cha mʼnyumba ya* Eli-beriti.+ 47  Abimeleki atauzidwa kuti atsogoleri onse amunsanja ya Sekemu asonkhana pamodzi, 48  iye limodzi ndi anthu onse amene anali naye anapita kuphiri la Zalimoni. Abimeleki anatenga nkhwangwa, ndipo anadula nthambi ya mtengo nʼkuinyamula paphewa. Kenako anauza anthu amene anali naye kuti: “Zimene mwaona ine ndikuchita, inunso muchite zomwezo mofulumira!” 49  Ndiyeno aliyense anadula nthambi yake nʼkutsatira Abimeleki. Kenako anaika nthambizo pachipinda chotetezekacho nʼkuchiyatsa moto. Choncho anthu onse okhala munsanja ya Sekemu, amuna ndi akazi pafupifupi 1,000, anafa. 50  Abimeleki anapita ku Tebezi kumene anamenyana ndi anthu amumzindawo nʼkuulanda. 51  Pakati pa mzindawo panali nsanja yolimba ndipo amuna ndi akazi onse komanso atsogoleri onse amumzindawo, anathawira munsanjayo. Atalowa mmenemo, anatseka chitseko nʼkukwera padenga la nsanjayo. 52  Abimeleki anapita kunsanjayo nʼkuyamba kuigwetsa. Ndiyeno anapita pakhomo la nsanjayo kuti aiwotche ndi moto. 53  Zitatero, mayi wina anaponya mwala wa mphero pamutu wa Abimeleki nʼkuuphwanya.+ 54  Nthawi yomweyo, Abimeleki anaitana mtumiki wake womunyamulira zida nʼkumuuza kuti: “Tenga lupanga lako undiphe, kuti anthu asadzanene kuti, ‘Anaphedwa ndi mkazi.’” Atatero, mtumiki wakeyo anamubaya ndi lupanga, ndipo anafa. 55  Anthu a mu Isiraeli ataona kuti Abimeleki wafa, aliyense anapita kwawo. 56  Choncho Mulungu anabwezera Abimeleki zoipa zimene anachitira bambo ake chifukwa chopha abale ake 70.+ 57  Mulungu anachititsanso kuti zoipa zonse za amuna a ku Sekemu ziwabwerere pamutu pawo. Choncho zimene Yotamu mwana wa Yerubaala+ ananena powatemberera,+ zinakwaniritsidwa.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “nzika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndine fupa lanu ndi mnofu wanu.”
Kapena kuti, “mʼkachisi wa.”