Rute 3:1-18

  • Naomi anapereka malangizo kwa Rute (1-4)

  • Rute ndi Boazi kopunthira mbewu (5-15)

  • Rute anabwerera kwa Naomi (16-18)

3  Tsopano Naomi, apongozi ake a Rute, anamuuza kuti: “Mwana wanga, kodi sindiyenera kukupezera nyumba,*+ kuti zikuyendere bwino?  Pajatu Boazi ndi wachibale wathu.+ Ndipo atsikana ake antchito wakhala ukugwira nawo ntchito. Usiku walero iye akhala akupeta balere pamalo ake opunthira.  Choncho samba nʼkudzola mafuta komanso utchene ndipo upite kumalo opunthirawo. Koma ukaonetsetse kuti iye asakadziwe kuti wafika mpaka atamaliza kudya ndi kumwa.  Ndiyeno akamakagona, ukaone kuti wagona pati. Kenako ukapite pamene wagonapo ndipo ukamuvundukule mapazi nʼkugona pomwepo. Iye akakuuza zochita.”  Rute anayankha kuti: “Ndikachita zonse zimene mwanena.”  Choncho anapita kopunthirako nʼkuchita zonse zimene apongozi ake anamuuza.  Boazi anadya ndi kumwa ndipo anali wosangalala kwambiri. Kenako anapita kukagona kumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndipo anavundukula mapazi a Boazi nʼkugona.  Pakati pa usiku Boazi anayamba kunjenjemera ndipo anadzuka nʼkukhala tsonga. Koma anadabwa kuona kuti mkazi wagona kumapazi ake.  Choncho anafunsa kuti: “Ndiwe ndani?” Rute anayankha kuti: “Ndine Rute kapolo wanu. Ndifunditseni chovala chanu ine kapolo wanu, chifukwa ndinu wotiwombola.”+ 10  Atatero, Boazi anati: “Yehova akudalitse mwana wanga. Chikondi chokhulupirika chimene wasonyeza panopa chikuposa choyamba chija,+ chifukwa sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. 11  Ndiye tamvera mwana wanga, usachite mantha. Ndikuchitira zonse zimene wanena,+ chifukwa aliyense mumzindawu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri. 12  Ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ koma pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine amene angakuwombole.+ 13  Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole mawa, zili bwino akuwombole.+ Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndikuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo, ndikuwombola. Gona mpaka mʼmawa.” 14  Choncho anagonabe kumapazi a Boazi mpaka mʼmamawa. Kenako anadzuka kudakali mdima chifukwa Boazi sanafune kuti anthu adziwe kuti kopunthira mbewuko kunabwera mkazi. 15  Ndiyeno anamuuza kuti: “Bweretsa nsalu wafundayo ndipo uitambasule.” Iye anaitambasuladi ndipo Boazi anathirapo miyezo 6* ya balere nʼkumusenza pamutu. Kenako Boazi analowa mumzinda. 16  Tsopano Rute anabwerera kwa apongozi ake, ndipo iwo anamufunsa kuti: “Wayendako bwanji* mwana wanga?” Iye anawafotokozera zonse zimene Boazi anamuchitira. 17  Anafotokozanso kuti: “Wandipatsa balere uyu wokwana miyezo 6 nʼkundiuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’” 18  Atatero, Naomi anayankha kuti: “Tiye tingodikira mwana wanga, mpaka utadziwa mmene nkhaniyi ithere. Chifukwa iye sakhala pansi mpaka ataithetsa nkhaniyi lero.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mpumulo.”
Nʼkutheka kuti inali miyezo 6 ya seya kapena malita pafupifupi 44. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwe ndani?”