Rute 4:1-22
4 Zitatero, Boazi anapita kugeti la mzinda+ nʼkukhala pansi. Ali kumeneko anaona wowombola anamutchula uja+ akudutsa. Ndiyeno Boazi anati: “Iwe uje, tabwera udzakhale apa.” Choncho anapita nʼkukakhala pansi.
2 Kenako Boazi anaitana akulu ena a mzindawo okwana 10+ nʼkuwauza kuti: “Takhalani apa.” Ndipo iwo anakhaladi.
3 Ndiyeno Boazi anauza wowombola uja+ kuti: “Naomi amene wabwerera kuchokera kudziko la Mowabu+ ayenera kugulitsa malo amene anali a mchimwene wathu Elimeleki.+
4 Ndiye ine ndaganiza zoti ndikuuze kuti, ‘Ugule malowo pamaso pa anthu ndiponso pamaso pa akulu a mzindawu.+ Ngati ukufuna kuwawombola, awombole. Koma ngati sukufuna undiuze, chifukwa iweyo ndiye woyenera kuwombola malowo ndipo pambuyo pako pali ineyo.’” Iye anayankha kuti: “Ndiwombola ineyo.”+
5 Kenako Boazi anati: “Ukadzagula malowo kwa Naomi, ndiye kuti wagulanso kwa Rute wa ku Mowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+
6 Wowombolayo atamva zimenezi anati: “Sinditha kuwombola, chifukwa ndingawononge cholowa changa. Inuyo wombolani mʼmalo mwa ine, chifukwa ine sinditha kuwombola.”
7 Kalelo mu Isiraeli munali mwambo wokhudza ufulu wowombola ndiponso wokhudza kusinthana ufuluwo, kuti chilichonse chimene chachitika chitsimikizirike. Mwambo wake unali woti munthu ankavula nsapato yake+ nʼkuipereka kwa mnzake. Umenewu unali umboni woti agwirizana kuti zikhale choncho.
8 Choncho pamene wowombola uja anauza Boazi kuti: “Mugule inuyo,” wowombolayo anavula nsapato yake.
9 Kenako Boazi anauza akulu ndi anthu onse kuti: “Inu ndinu mboni+ lero kuti ndikugula kwa Naomi zinthu zonse zimene zinali za Elimeleki ndiponso zonse zimene zinali za Kiliyoni ndi Maloni.
10 Komanso ndikutenga Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni, kukhala mkazi wanga kuti dzina la mwamuna wake amene anamwalira libwerere pacholowa chake+ komanso kuti lisafafanizidwe pakati pa abale ake ndiponso mumzindawu. Inu ndinu mboni lero.”+
11 Zitatero, anthu onse ndi akulu amene anali pageti la mzindawo ananena kuti: “Ndife mboni! Yehova adalitse mkazi amene akulowa mʼnyumba mwako kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, akazi amene anamanga nyumba ya Isiraeli.+ Zinthu zikuyendere bwino mu Efurata+ ndipo ukhale ndi dzina labwino mu Betelehemu.+
12 Ndipo kudzera mwa ana amene Yehova adzakupatsa kwa mtsikanayu,+ nyumba yako ikhale ngati nyumba ya Perezi,+ amene Tamara anaberekera Yuda.”
13 Choncho Boazi anatenga Rute kukhala mkazi wake ndipo anagona naye. Yehova anamudalitsa ndipo anatenga pakati nʼkubereka mwana wamwamuna.
14 Zitatero azimayi anayamba kuuza Naomi kuti: “Atamandike Yehova, amene wachititsa kuti upeze wokuwombola lero. Dzina lake lifalitsidwe mu Isiraeli.
15 Mwanayu watsitsimutsa moyo wako ndipo adzakusamalira mu ukalamba wako, chifukwa yemwe wamubereka ndi mpongozi wako amene amakukonda,+ amenenso ndi woposa ana aamuna 7.”
16 Naomi ananyamula mwanayo ndipo ankamulera.
17 Azimayi okhala naye pafupi anamupatsa mwanayo dzina lakuti Obedi. Ndipo iwo anati: “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Obedi+ anali bambo ake a Jese,+ yemwe anabereka Davide.
18 Mzere wa ana a Perezi+ unayenda chonchi: Perezi anabereka Hezironi,+
19 Hezironi anabereka Ramu, Ramu anabereka Aminadabu,+
20 Aminadabu+ anabereka Naasoni, Naasoni anabereka Salimoni,
21 Salimoni anabereka Boazi, Boazi anabereka Obedi,
22 Obedi anabereka Jese ndipo Jese+ anabereka Davide.+