Kalata Yopita kwa Tito 2:1-15

  • Malangizo abwino kwa achinyamata ndi achikulire (1-15)

    • Kukana moyo wosaopa Mulungu (12)

    • Kudzipereka pa ntchito zabwino (14)

2  Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi mfundo zolondola.+  Amuna achikulire akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana, oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba, achikondi chachikulu ndi opirira kwambiri.  Nawonso akazi achikulire akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche, kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino,  nʼcholinga choti azilangiza* akazi achitsikana kuti azikonda amuna awo, azikonda ana awo,  azikhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo,* abwino ndiponso ogonjera amuna awo,+ kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.  Komanso upitirize kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+  Ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino mʼnjira iliyonse. Uziphunzitsa zolondola* ndipo uzisonyeza kuti ndiwe wopanda chibwana.+  Mawu ako azikhala oyenera, omwe sangatsutsidwe,+ kuti otsutsa achite manyazi ndipo asapeze chifukwa chotinenera.+  Akapolo azigonjera ambuye awo pa zinthu zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo 10  kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse, kuti azikometsera zimene Mpulumutsi wathu Mulungu amatiphunzitsa.+ 11  Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweretsa chipulumutso kwa anthu, kaya akhale otani.+ 12  Zimenezi zimatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu. Zimatiphunzitsanso kuti tisamalakelake zinthu zoipa zamʼdzikoli,+ koma kuti tikhale oganiza bwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu mʼdzikoli*+ 13  pamene tikuyembekezera zinthu zosangalatsa+ ndiponso kuonekera kwaulemerero kwa Mulungu wamkulu komanso kwa Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, 14  amene anadzipereka mʼmalo mwa ife+ kuti atilanditse*+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse, kuti tikhale anthu ake apadera, odzipereka pa ntchito zabwino.+ 15  Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu pogwiritsa ntchito ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Usalole kuti munthu aliyense akuderere.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “azikumbutsa; aziphunzitsa.”
Kapena kuti, “osamalira nyumba zawo.”
Kapena kuti, “zoyera.”
Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atiperekere dipo; atiwombole.”