Kalata Yopita kwa Tito 3:1-15
3 Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndiponso kumvera maboma ndi olamulira.+ Akhalenso okonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
2 Asamanenere zoipa munthu aliyense ndiponso asamakonde kukangana. Koma akhale ololera+ ndipo azikhala ofatsa kwa anthu onse.+
3 Paja nafenso poyamba tinali opanda nzeru, osamvera, osocheretsedwa, akapolo a zilakolako zosiyanasiyana ndiponso a zinthu zosangalatsa, ochita zoipa, akaduka, onyansa komanso tinkadana.
4 Koma Mpulumutsi wathu Mulungu+ atasonyeza kukoma mtima ndi kukonda anthu,
5 (osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene tinachita,+ koma chifukwa cha chifundo chake),+ anatipulumutsa potisambitsa kuti tifike ku moyo watsopano.+ Komanso anatipulumutsa potithandiza ndi mzimu woyera kuti tikhale atsopano.+
6 Iye anatikhuthulira mzimu umenewu kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,+
7 kuti titayesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu,+ tingakhale olandira cholowa+ mogwirizana ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.+
8 Mawu amenewa ndi oona, ndipo ndikufuna kuti upitirize kutsindika zinthu zimenezi, kuti amene akhulupirira Mulungu aziganizira kwambiri mmene angapitirizire kuchita ntchito zabwino. Zimenezi nʼzabwino ndiponso zothandiza kwa anthu.
9 Koma iwe uzipewa kutsutsana pa zinthu zopusa komanso zokhudza mibadwo ya makolo. Uzipewanso kukangana ndi kulimbana ndi anthu pa nkhani zokhudza Chilamulo, chifukwa zimenezi nʼzosathandiza ndiponso zopanda phindu.+
10 Munthu wolimbikitsa mpatuko,+ ukamudzudzula* koyamba ndi kachiwiri,+ usagwirizane nayenso+
11 podziwa kuti munthu woteroyo wasochera, akuchimwa ndipo akudziimba mlandu.
12 Ndikadzatuma Atema kapena Tukiko+ kwa iwe, udzayesetse kuti udzandipeze ku Nikopoli, chifukwa ndaganiza zokakhala kumeneko nyengo yozizirayi.
13 Zena, wodziwa Chilamulo uja, komanso Apolo, uwapatse zinthu zofunika pa ulendo zokwanira, kuti asasowe kanthu.+
14 Koma abale athu aphunzire kugwira ntchito zabwino kuti azitha kuthandiza pakafunika kutero,+ kuti asakhale opanda phindu.+
15 Onse amene ndili nawo kuno akupereka moni. Undiperekere moni kwa anthu amene amatikonda chifukwa tili ndi chikhulupiriro chofanana.
Kukoma mtima kwakukulu kukhale ndi nonsenu.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “ukamuchenjeza.”